Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tigwirizanenso

Tigwirizanenso

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Ndakhumudwa kwanthawidi

    Mtima wanga ukuwawa.

    Mkwiyowutu ukuyaka

    Ngati moto, ndizowawa,

    Sizabwino.

    (KOLASI)

    Koma ndingodzichepetsa

    Ndibwezeretse mtendere.

    Ndisasunge chakukhosi.

    Tikhalebe paubwenzi.

  2. 2. N’kakhumudwa n’ziganiza

    Zachikondi cha Mulungu.

    Dipo lomwe wapereka

    N’lapamwamba, ndimtsanzire

    N’khululuke.

    (KOLASI)

    Koma ndingodzichepetsa

    Ndibwezeretse mtendere.

    Ndisasunge chakukhosi.

    Tikhalebe paubwenzi.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Ndiyambe ndine.

    Ndisachedwe kupitako.

    Ndipeze mtendere.

    Ndimve bwino, timve bwino!

  3. 3. Mulungutu akufuna

    Iwe ndi’ne tim’tsanzire.

    N’khululuke, ndiiwale

    N’sakumbuke ngakhaletu

    Sizophweka.

    (KOLASI)

    Koma ndingodzichepetsa

    Ndibwezeretse mtendere.

    Ndisasunge chakukhosi.

    Tikhalebe paubwenzi.

    Tikhalebe paubwenzi.

    Ndiyambe ndine.