Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Choonadi Ndi Chofunikabe Masiku Ano?

Kodi Choonadi Ndi Chofunikabe Masiku Ano?

 Kodi mukuona kuti zayamba kuvuta kwambiri kusiyanitsa pakati pa zinthu zoona ndi zabodza? Masiku ano, anthu ayamba kukopeka kwambiri ndi maganizo komanso zikhulupiriro zawo m’malo mwa choonadi ndi mfundo zolondola. Iwo akumafalitsa mabodza padziko lonse.

 Si zachilendo kuona anthu akuchita zinthu mwa njira imeneyi. Zaka 2,000 zapitazo, bwanamkubwa wa Chiroma dzina lake Pontiyo Pilato, anafunsa Yesu pofuna kumukola kuti: “Choonadi nʼchiyani?” (Yohane 18:38) Ngakhale kuti Pilato sanapatse Yesu mpata woti ayankhe, funso limeneli linali lofunika kwambiri. Anthu ambiri m’dzikoli amasokonezeka maganizo pa nkhani ya choonadi koma Baibulo limapereka yankho lomwe lingakuthandizeni kusiyanitsa zinthu zoona ndi zabodza.

Kodi choonadi chilipo?

 Inde. Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “choonadi” ponena za mfundo zolondola komanso zovomerezeka mogwirizana ndi makhalidwe abwino. Limaphunzitsa kuti choonadi chimachokera kwa Yehova a Mulungu ndipo limamutchula kuti ndi “Mulungu wa choonadi.” (Salimo 31:5) M’Baibulo muli choonadi chochokera kwa Mulungu, ndipo limayerekezera choonadi ndi kuwala chifukwa chimatitsogolera ku mfundo zolondola mosiyana ndi mfundo zabodza zomwe zikusokoneza anthu ambiri masiku ano.​—Salimo 43:3; Yohane 17:17.

Kodi mungapeze bwanji choonadi?

 Mulungu samafuna kuti tidzivomereza choonadi cha m’Baibulo m’chimbulimbuli. M’malomwake, iye akutiuza kuti tizigwiritsa ntchito mphamvu zathu za kuganiza m’malo modalira maganizo athu. (Aroma 12:1) Iye akufuna kuti timudziwe komanso tizimukonda pogwiritsa ntchito ‘maganizo athu onse,’ ndipo akutilimbikitsa kuti tizitsimikizira mfundo zomwe timaphunzira m’Baibulo kuti ndi zoona.​—Mateyu 22:37, 38; Machitidwe 17:11.

Kodi bodza linachokera kuti?

 Baibulo limanena kuti bodza linayamba ndi mdani wa Mulungu, Satana Mdyerekezi, yemwenso Baibulo limamutchula kuti “tate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Iye anauza Adamu ndi Hava zinthu zabodza zokhudza Mulungu. (Genesis 3:1-6, 13, 17-19; 5:5) Kungoyambira nthawi imeneyo, Satana wakhala akufalitsa mabodza komanso kubisa choonadi chokhudza Mulungu.​—Chivumbulutso 12:9.

N’chifukwa chiyani masiku ano bodza lili ponseponse?

 Masiku ano, omwe amatchedwa “masiku otsiriza,” Satana akupitiriza kusocheretsa anthu ambiri padzikoli. Si zachilendo kuona anthu akufalitsa mabodza pofuna kusocheretsa anzawo ngakhalenso kuwapondereza. (2 Timoteyo 3:1, 13) Zipembedzo zambiri masiku ano zimanena mabodza. Monga mmene Baibulo linanenera zokhudza nthawi yathu ino, “anthu sadzafunanso kuphunzitsidwa zolondola, koma mogwirizana ndi zimene amalakalaka, adzapeza aphunzitsi oti aziwauza zowakomera mʼkhutu. Iwo adzasiya kumvetsera choonadi.”​—2 Timoteyo 4:3, 4.

N’chifukwa chiyani choonadi ndi chofunika?

 Anthu amafunikira choonadi n’cholinga choti azikhulupirirana. Popanda kukhulupirirana, maubwenzi amasokonekera. Baibulo limanena kuti Mulungu akufuna kuti kulambira kwathu kuzikhala kochokera ku mfundo za choonadi. Limati: “Amene akumulambira [Mulungu] akuyenera kumulambira motsogoleredwa ndi mzimu komanso choonadi.” (Yohane 4:24) Kuti mudziwe mmene Choonadi chochokera m’Baibulo chingakuthandizireni kuzindikira mfundo zabodza zachipembedzo komanso kuti mumasuke, werengani magazini yamutu wakuti “Mabodza Omwe Amalepheretsa Anthu Kukonda Mulungu.”

N’chifukwa chiyani Mulungu akufuna kuti ndidziwe choonadi?

 Mulungu akufuna kuti mupulumuke, ndipo mungachite zimenezi mwa kuphunzira choonadi chokhudza iyeyo. (1 Timoteyo 2:4) Ngati mungadziwe mfundo zimene Mulungu amafuna pa nkhani ya zoyenera ndi zosayenera n’kumayesetsa kutsatira mfundozi, mudzakhala naye pa ubwenzi wolimba. (Salimo 15:1, 2) Mulungu anatumiza Yesu padzikoli kuti athandize anthu kudziwa choonadi. Mulungu amafuna kuti tizimvetsera zimene Yesu amaphunzitsa.​—Mateyu 17:5; Yohane 18:37.

Kodi Mulungu adzathetseratu mabodza?

 Inde. Mulungu amadana ndi anthu achinyengo omwe amadyera anzawo masuku pamutu. Iye akulonjeza kuti adzawononga anthu onse amene amakonda kunena mabodza. (Salimo 5:6) Mulungu akadzachita zimenezi, adzakwaniritsa lonjezo lakuti: “Milomo imene imalankhula zoona idzakhalapo mpaka kalekale.”​—Miyambo 12:19.

a Yehova ndi dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?