Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Yohane 14:6—“Ine Ndine Njira, Choonadi ndi Moyo”

Yohane 14:6—“Ine Ndine Njira, Choonadi ndi Moyo”

 “Yesu anamuuza kuti: ‘Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.’”—Yohane 14:6, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.”—Yohane 14:6, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Yohane 14:6

 Munthu amene akufuna kulambira Atate, yemwe ndi Yehova a Mulungu, ayenera kuzindikira udindo wa Yesu.

 “Ine ndine njira.” Yesu amapereka “njira” yoti munthu azilambira Mulungu movomerezeka. Mwachitsanzo, munthu amayenera kupemphera kwa Mulungu m’dzina la Yesu. (Yohane 16:23, 24) Chifukwa cha imfa ya Yesu, anthu akhoza kuyanjanitsidwa ndi Mulungu kuti akhale naye pa ubwenzi wabwino. (Aroma 5:8-11) Yesu anaperekanso chitsanzo chimene anthu amayenera kutsatira kuti azisangalatsa Mulungu.—Yohane 13:15.

 “Ine ndine . . . choonadi.” Nthawi zonse, Yesu ankalankhula zoona zokhazokha komanso ankazitsatira pa moyo wake. (1 Petulo 2:22) Munthu akamamvetsera zimene Yesu ankanena, ankatha kuphunzira zoona zake zokhudza Mulungu. (Yohane 8:31, 32) Yesu analinso “choonadi” chifukwa anakwaniritsa maulosi a m’Baibulo. Pochita zimenezi, anakwaniritsanso malonjezo a Mulungu.—Yohane 1:17; 2 Akorinto 1:19, 20; Akolose 2:16, 17.

 “Ine ndine . . . moyo.” Yesu anapereka moyo wake kuti anthu amene amamukhulupirira adzapeze moyo wosatha. (Yohane 3:16, 36) Iye alinso “moyo” kwa anthu amene anamwalira chifukwa adzawaukitsa.—Yohane 5:28, 29; 11:25.

 “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” Anthu amene amafuna kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ayenera kuzindikira udindo wapadera wa Yesu. Amasonyeza kuti amazindikira udindowu akamapemphera kwa Mulungu m’dzina la Yesu. (Yohane 15:16) Iwo amazindikiranso kuti akhoza kudzapulumuka chifukwa cha Yesu.—Machitidwe 4:12; Afilipi 2:8-11.

Nkhani yonse ya Yohane 14:6

 Mu Yohane chaputala 13 mpaka 17 muli malangizo omaliza amene Yesu anapereka kwa atumwi ake 11 okhulupirika usiku woti aphedwa mawa lake. M’chaputala 14, Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti azisonyeza kuti amakhulupirira iye komanso Atate wake. Anawalimbikitsanso kuti azikonda iye ndi Atate wake komanso kuwamvera. (Yohane 14:1, 12, 15-17, 21, 23, 24) Yesu anasonyezanso kuti ali pa ubwenzi wolimba kwambiri ndi Atate wake. (Yohane 14:10, 20, 28, 31) Ngakhale kuti anali atatsala pang’ono kubwerera kumwamba, Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti sadzawasiya. (Yohane 14:18) Iye analonjezanso kuwapatsa “mthandizi” yemwe anamufotokoza kuti ndi ‘mzimu woyera, amene Atate wake adzatumiza m’dzina lake.’ (Yohane 14:25-27) M’njira zimenezi komanso zina, Yesu anakonzekeretsa otsatira ake kuti athe kupirira mavuto obwera m’tsogolo.