Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndiyenera Kulowa Chipembedzo Chinachake?

Kodi Ndiyenera Kulowa Chipembedzo Chinachake?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Ndiyenera Kulowa Chipembedzo Chinachake?

▪ Kodi mumaopa kulowa m’chipembedzo chifukwa mumaona kuti anthu ambiri amene amapita kutchalitchi ngakhalenso akuluakulu a zipembedzo sagwirizana komanso ndi achinyengo kwambiri? Ngati ndi choncho, mwina zimene mwambi wina wa ku France umanena ndi zofanana ndi zimene inu mumaganiza pa nkhaniyi. Mwambiwu umati: “Wokhala pafupi ndi tchalitchi ali kutali ndi Mulungu.”

N’kutheka kuti mumakhulupirira Baibulo ndipo mumaona kuti maboma ndiponso anthu ayenera kulemekeza ufulu wa munthu wolowa m’chipembedzo chimene akufuna. Koma mwina mumadzifunsa kuti: ‘Kodi Mulungu amanenadi kuti munthu amene akufuna kumulambira movomerezeka ayenera kulowa m’chipembedzo chinachake?’

Yankho losapita m’mbali ndi lakuti inde. N’chifukwa chiyani tikunena choncho? Nanga kodi zikutanthauza kuti palibe vuto ngati mutalowa chipembedzo china chilichonse?

Taganizirani za Yesu. Kodi iye anali mu chipembedzo chilichonse? Ali mwana, iyeyo, anthu ena ndiponso makolo ake omwe anali Ayuda, ankapita kukachisi wa ku Yerusalemu kukalambira. (Luka 2:41-43) Komanso atakula, iye ndi Ayuda anzake ankapita kukalambira Mulungu ku sunagoge. (Luka 4:14-16) Polankhula ndi mayi wina yemwe anali wa chipembedzo china, Yesu ananena kuti: “Ife timalambira chimene tikuchidziwa.” (Yohane 4:22) Pamenepa Yesu anasonyeza kuti iye anali m’chipembedzo chachiyuda.

Kenako Yesu ananena kuti popeza mtundu wa Ayuda unamukana iyeyo, Mulungu adzakana kulambira kwawo, kumenenso kunali kutaipitsidwa. (Mateyu 23:33–24:2) Komabe anasonyeza kuti anthu amene akufuna kulambira Mulungu movomerezeka ayenera kukhala m’gulu linalake lachipembedzo. Iye anauza otsatira ake kuti: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yohane 13:35) Wophunzira wa Khristu amene salambira ndiponso kuchita zinthu ndi Akhristu anzake sangathe kuwakonda mwa njira imeneyi. Ndipotu Yesu ananena mosapita m’mbali kuti pa nkhani yolambira, pali njira ziwiri zokha. Iye anati njira ina ndi ‘yaikulu ndiponso yotakasuka’ koma ‘ikupita kuchiwonongeko.’ Koma ponena za njira inayo anati: “Chipata cholowera ku moyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.”​—Mateyu 7:13, 14.

Ndiyetu zikuonekeratu kuti si kuti chipembedzo china chilichonse n’chabwino. Baibulo limatichenjeza kuti sitiyenera kukhala m’chipembedzo cha anthu “ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.” Baibulo limatinso: “Anthu amenewa uwapewe.” (2 Timoteyo 3:5) Koma tingapindule kwambiri titadziwa anthu amene akuyenda pa njira yopita ku moyo wosatha, n’kuyamba kulambira nawo limodzi. Kuchita zimenezi kungatilimbikitse ndiponso kutithandiza kwambiri pa moyo wathu. Kuwonjezera pamenepa, tingakhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.​—Aheberi 10:24, 25.

Ndiyeno kodi mungadziwe bwanji chipembedzo chimene anthu ake akuyenda pamsewu wopapatiza? Mayankho ochokera m’Baibulo a funso limeneli mungawapeze m’mutu 15 wa buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? * Buku limeneli lingakuthandizeni kusankha mwanzeru chipembedzo chimene mufunika kulowa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Buku limeneli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.