Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Adzalola Kuti Um’peze”

“Adzalola Kuti Um’peze”

Yandikirani Mulungu

“Adzalola Kuti Um’peze”

1 MBIRI 28:9

KODI Mulungu mumamudziwa? Ena angaone ngati funso limeneli ndi losavuta. Koma kudziwadi Mulungu kumaphatikizapo kudziwa bwino zimene iye amafuna ndiponso njira zake. Zikatero timakhala naye pa ubwenzi wolimba ndipo zimenezi zimakhudza kwambiri zonse zimene timachita pa moyo wathu. Komano kodi zingathekedi kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu? Ngati ndi zotheka, kodi tingatani kuti tikhale naye pa ubwenzi woterowo? Yankho la mafunso amenewa tingalipeze mu malangizo amene Mfumu Davide anauza mwana wake Solomo, opezeka pa 1 Mbiri 28:9.

Taganizirani zimene zinachitika. Davide anali atalamulira Aisiraeli kwa zaka pafupifupi 40, ndipo kwa nthawi yonseyi zinthu zinkawayendera bwino. Pa nthawiyi Solomo, amene anali atatsala pang’ono kulowa m’malo mwa Mfumu Davide, anali wamng’ono kwambiri. (1 Mbiri 29:1) Kodi ndi malangizo omaliza ati amene Davide anapatsa mwana wake?

Kuchokera pa zimene zinamuchitikira potumikira Mulungu, Davide anayamba n’kunena kuti: “Solomo mwana wanga, dziwa Mulungu wa bambo wako.” Pamenepa, Davide sanali kutanthauza kungodziwa chabe mfundo zokhudza Mulungu. Tikutero chifukwa pa nthawiyi, Solomo anali atayamba kale kulambira Yehova, Mulungu amenenso Davide ankamulambira. Komanso mbali yaikulu ya Malemba Achiheberi inali italembedwa kale ndipo ndi zosakayikitsa kuti Solomo ankadziwa zimene malemba opatulika amenewa ankanena zokhudza Mulungu. Katswiri wina wamaphunziro ananena kuti mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “dziwa” angatanthauze “kudziwana kwambiri ndi munthu.” Ndiye kuti apa Davide ankafuna kuti mwana wakeyu akhale pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu, umenenso Davideyo ankaona kuti ndi chinthu chofunika kwambiri.

Ubwenzi wolimba umenewu unayenera kukhudza maganizo ndi zochita za Solomo. Kenako Davide anauza mwana wakeyu kuti: “Um’tumikire ndi mtima wathunthu ndi moyo wosangalala.” * Onani kuti choyamba Davide anauza Solomo kuti afunika kudziwa Mulungu. Kenako ndi pamene anamulangiza kuti ayenera kumutumikira. Zimenezi ndi zomveka chifukwa munthu akadziwadi Mulungu amayamba kumutumikira. Komabe munthu sayenera kutumikira Mulungu monyinyirika kapena mwachinyengo. (Salimo 12:2; 119:113) Davide analangiza mwana wake kuti atumikire Mulungu ndi mtima wonse komanso mwakufuna kwake.

Kodi n’chifukwa chiyani Davide analimbikitsa mwana wake kukhala ndi zolinga ndiponso maganizo abwino polambira Yehova? Davide ananena kuti: “Chifukwa Yehova amasanthula mitima yonse ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.” Solomo sankayenera kutumikira Mulungu ndi cholinga chakuti angosangalatsa Davide, bambo ake. Mulungu amasangalala ndi anthu amene amafunadi kumutumikira ndi mtima wonse.

Kodi Solomo akanatengeradi chitsanzo cha bambo ake ndi kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova? Zinali kwa iye kuchita zimenezo kapena ayi. Koma Davide anauza mwana wakeyu kuti: “Ukam’funafuna, adzalola kuti um’peze, koma ukam’siya adzakutaya kosatha.” Solomo anafunika kuchita khama kuti adziwe Yehova, ndipo zimenezi ndi zimene zikanachititsa kuti akhale naye pa ubwenzi wolimba kwambiri. *

Malangizo amene Davide anapatsa mwana wake akutitsimikizira kuti Yehova amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. Koma kuti zimenezi zitheke tiyenera ‘kum’funafuna.’ Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kuphunzira kwambiri Malemba n’cholinga choti timudziwe bwino. Tikadziwa Mulungu tiyenera kuyamba kumutumikira ndi mtima wonse ndiponso mwakufuna kwathu. Yehova amafuna kuti anthu azichita zimenezi ndipo iye ndi woyeneradi kumutumikira mwa njira imeneyi.​—Mateyu 22:37.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mabaibulo ena pa lembali amati: “Um’tumikire ndi mtima wonse komanso mwakufuna kwako.”

^ ndime 6 N’zomvetsa chisoni kuti ngakhale kuti Solomo anayamba kutumikira Mulungu ndi mtima wathunthu, sanapitirizebe kukhala wokhulupirika.​—1 Mafumu 11:4.