Pitani ku nkhani yake

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Zotani?

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Zotani?

A Mboni za Yehovafe timayesetsa kutsatira zimene Yesu ankaphunzitsa komanso kutengera chitsanzo cha atumwi. Nkhaniyi ikufotokoza mwachidule zimene timakhulupirira.

  1.   Mulungu. Timalambira Mulungu m’modzi woona yemwe ndi mlengi ndipo dzina lake ndi Yehova. (Salimo 83:18; Chivumbulutso 4:11) Yehova ndi Mulungu amene Abulahamu, Mose komanso Yesu ankalambira.​—Ekisodo 3:6; 32:11; Yohane 20:17.

  2.   Baibulo. Timadalira kwambiri mawu a Mulungu chifukwa timadziwa kuti Mulungu ndi amene anathandiza anthu kuti alembe Baibulo. (Yohane 17:17; 2 Timoteyo 3:16) Choncho zimene timakhulupirira zimachokera m’mabuku onse a m’Baibulo okwana 66, omwe akuphatikizapo “Chipangano Chakale” ndiponso “Chipangano Chatsopano.” Pulofesa wina dzina lake Jason D. BeDuhn, ananena kuti a Mboni za Yehova anapanga zikhulupiriro zawo pogwiritsa ntchito zimene Baibulo limanena osati kupotoza malemba n’cholinga choti agwirizane ndi zikhulupiriro zawozo.” a

     N’zoona kuti timakhulupirira Baibulo lonse koma sikuti timakhulupirira kuti mawu onse a m’Baibulo tiyenera kungowatenga mmene alili. Timazindikira kuti mbali zina m’Baibulo zinalembedwa mophiphiritsa.​—Chivumbulutso 1:1.

  3.   Yesu. Timatsatira zimene Yesu ankaphunzitsa komanso timatengera chitsanzo chake. Timamulemekeza chifukwa ndi mwana wa Mulungu komanso Mpulumutsi wathu. (Mateyu 20:28; Machitidwe 5:31) Choncho nafenso ndi Akhristu. (Machitidwe 11:26) Komabe tinaphunzira m’Baibulo kuti Yesu si Mulungu Wamphamvuyonse komanso kuti Baibulo silinena kuti pali Mulungu Tate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu Woyera.​—Yohane 14:28.

  4.   Ufumu wa Mulungu. Umenewu ndi Ufumu weniweni umene uli kumwamba. Si maganizo amene amakhala mumtima mwa Akhristu. Ufumu umenewu udzalowa m’malo mwa maboma amene ali padzikoli ndipo udzapangitsa kuti dzikoli likhale paradaiso. (Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10) Ufumu umenewu uchita zimenezi posachedwapa chifukwa ulosi wa m’Baibulo ukusonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’​—2 Timoteyo 3:1-5; Mateyu 24:3-14.

     Yesu ndi Mfumu ya Ufumu umenewu. Ufumuwu unayamba kulamulira kumwamba mu 1914.​—Chivumbulutso 11:15.

  5.   Chipulumutso. Anthufe tidzapulumutsidwa ku uchimo komanso imfa kudzera mu nsembe ya Yesu. (Mateyu 20:28; Machitidwe 4:12) Kuti tipindule ndi nsembe imeneyi, tiyenera kukhulupirira Yesu komanso kusintha moyo wathu n’kubatizidwa. (Mateyu 28:19, 20; Yohane 3:16; Machitidwe 3:19, 20) Munthu amasonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro ngati amachita zinthu zogwirizana ndi zimene amakhulupirira. (Yakobo 2:24, 26) Komabe izi sizikutanthauza kuti zochita za munthu zokha zingachititse kuti akhale woyenerera kupulumuka. Tikutero chifukwa munthu kuti apulumuke zikudalira “kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.”​—Agalatiya 2:16, 21.

  6.   Kumwamba. Kumwamba kumakhala Yehova Mulungu, Yesu Khristu ndiponso angelo okhulupirika. b (Salimo 103:19-21; Machitidwe 7:55) Ndi anthu 144,000 okha amene adzapite kumwamba n’cholinga choti akalamulire ndi Yesu Khristu.​—Danieli 7:27; 2 Timoteyo 2:12; Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 3.

  7.   Dziko Lapansi. Mulungu analenga dziko lapansili kuti pazikhala anthu. (Salimo 104:5; 115:16; Mlaliki 1:4) Mtsogolomu Mulungu adzadalitsa anthu omvera ndipo sazidzadwala komanso adzakhala padzikoli mpaka kalekale.​—Salimo 37:11, 34.

  8.   Zinthu zoipa ndiponso mavuto. Mavuto onse padzikoli anayambika chifukwa cha mngelo amene anatsutsa ulamuliro wa Mulungu. (Yohane 8:44) Mngeloyu atachita zimenezi anayamba kudziwika ndi mayina akuti “Satana” ndiponso “Mdyerekezi.” Kenako mngeloyu anapusitsa Adamu ndi Hava kuti nawonso agalukire Mulungu ndipo zimenezi zinayambitsa mavuto aakulu. Ndipo popeza ana awo anabadwa iwo atachimwa kale, nawonso anayamba kukumana ndi mavuto amenewo. (Genesis 3:1-6; Aroma 5:12) Ndiye pofuna kusonyeza kuti zimene Satana Mdyerekezi ananena ndi zabodza, Mulungu analola kuti anthu akumane ndi mavuto. Koma sikuti mavutowa adzapitirira mpaka kalekale.

  9.   Imfa. Timakhulupirira kuti anthu amene anamwalira amakhala kuti kulibenso. (Salimo 146:4; Mlaliki 9:5, 10) Iwo sikuti amakhala akuzunzika kumoto.

     Mulungu adzaukitsa anthu mabiliyoni ambiri amene anamwalira. (Machitidwe 24:15) Komabe anthu amene adzakane kuchita zimene Mulungu amafuna akadzaukitsidwa, Mulungu adzawawononga ndipo sadzawaukitsanso.​—Chivumbulutso 20:5.

  10.   Banja. Timamvera malamulo a Mulungu okhudza ukwati ndipo sitichita mitala. Timaona kuti banja likhoza kutha pokhapokha ngati wina wachita chigololo. (Mateyu 19:4-9) Timaona kuti malangizo a m’Baibulo amathandiza kuti mabanja aziyenda bwino.​—Aefeso 5:22–6:1.

  11.   Zimene timachita tikamalambira Mulungu. Sitimagwiritsa ntchito mtanda kapena zithunzi polambira Mulungu. (Deuteronomo 4:15-19; 1 Yohane 5:21) Timalambira Mulungu m’njira zotsatirazi:

  12.   Gulu lathu. Timasonkhana m’mipingo yosiyanasiyana ndipo mipingoyi imayang’aniridwa ndi bungwe la akulu. Komabe akuluwa sikuti ali ngati atsogoleri achipembedzo ndipo salandira malipiro. (Mateyu 10:8; 23:8) Sitimapereka chakhumi komanso pamisonkhano yathu sitiyendetsa mbale ya zopereka. (2 Akorinto 9:7) Ntchito yathu imayendetsedwa ndi ndalama zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo.

    Gulu lathu limatsogoleredwa ndi abale ochepa okhwima mwauzimu.  Abalewa ali m’Bungwe Lolamulira ndipo amagwira ntchito yawo kumalikulu athu.​—Mateyu 24:45.

  13.   Mgwirizano wathu. A Mboni tonse timakhulupirira zofanana. (1 Akorinto 1:10) Timayesetsanso kuti tisamachite tsankho. (Machitidwe 10:34, 35; Yakobo 2:4) Timagwirizana kwambiri ngakhale kuti nthawi zina timaona komanso kusankha zinthu mosiyana. Wa Mboni aliyense amasankha zochita mogwirizana ndi zimene anaphunzira Baibulo.​—Aroma 14:1-4; Aheberi 5:14.

  14.   Khalidwe lathu. Timayesetsa kuti tizikondana kuchokera pansi pamtima. (Yohane 13:34, 35) Timapewa zinthu zimene Mulungu amadana nazo monga kugwiritsa ntchito magazi ndipo sitiikidwa magazi kuchipatala. (Machitidwe 15:28, 29; Agalatiya 5:19-21) Timayesetsa kukhala mwamtendere ndipo sitimenya nawo nkhondo. (Mateyu 5:9; Yesaya 2:4) Timayesetsanso kumvera boma komanso kutsatira malamulo adziko limene tikukhala. Komabe nthawi zina mabomawa akatiuza kuti tichite zotsutsana ndi zimene Mulungu amafuna, timasankha kumvera Mulungu osati anthu.​—Mateyu 22:21; Machitidwe 5:29.

  15.   Zimene timachita tikakhala ndi anthu ena. Yesu anati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” Ananenanso kuti Akhristu “sali mbali ya dziko.” (Mateyu 22:39; Yohane 17:16) Timayesetsa ‘kuchitira onse zabwino’ koma sikuti timalowerera zandale kapena kuchita mgwirizano ndi zipembedzo zina. (Agalatiya 6:10; 2 Akorinto 6:14) Komabe timalemekeza zimene anthu ena amasankha pankhaniyi.​—Aroma 14:12.

 Ngati muli ndi mafunso ena okhudza zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira mungawerenge zambiri pa Webusaiti yathu. Mukhozanso kuimba foni kapena kulemba kalata kumaofesi athu, kupita ku Nyumba ya Ufumu yomwe ili m’dera lanu kapena mukhoza kufunsa wa Mboni za Yehova aliyense.

a Onani buku lamutu wakuti Truth in Translation, tsamba 165.

b Angelo oipa anathamangitsidwa kumwamba komabe sitingawaone.​—Chivumbulutso 12:7-9.