Pitani ku nkhani yake

Kodi Mulungu Ali Ndi Dzina?

Kodi Mulungu Ali Ndi Dzina?

Yankho la m’Baibulo

 Munthu aliyense ali ndi dzina lake. Kodi sizoyenera kuti Mulungu akhalenso ndi dzina lake? Kudziwana mayina ndiponso kuwagwiritsira ntchito n’kofunika kwambiri chifukwa kumathandiza kuti ubwenzi wa anthufe udziyenda bwino. Chotero kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu tiyeneranso kudziwa dzina lake.

 M’Baibulo, Mulungu anati: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” (Yesaya 42:8) Ngakhale kuti alinso ndi mayina ena audindo, monga “Mulungu Wamphamvuyonse,” “Ambuye Wamkulu Koposa” komanso “Mlengi,” iye amalemekeza anthu amene amamulambira powapatsa mwayi wakuti azimutchula ndi dzina lake lenileni.—Genesis 17:1; Machitidwe 4:24; 1 Petulo 4:19.

 M’Mabaibulo ambiri, dzina la Mulungu limapezeka pa Ekisodo 6:3. Vesili limati: “Ndinali kuonekera kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo monga Mulungu Wamphamvuyonse. Koma za dzina langa lakuti Yehova, ine sindinadzidziwikitse kwa iwo.”

 M’Chichewa dzina la Mulungu ndi Yehova ndipo lakhala likugwiritsidwa ntchito kwa zaka zambiri. Ngakhale kuti akatswiri ambiri a Baibulo amanena kuti dzina la Mulungu liyenera kulembedwa kuti “Yahweh,” anthu ambiri amadziwa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Mbali yoyambirira ya Baibulo sinalembedwe m’Chingelezi koma inalembedwa m’Chiheberi. Zilembo za Chiheberi zimawerengedwa kuchokera kumanja kupita kumanzere. M’chinenero chimenechi, dzina la Mulungu limalembedwa chonchi, יהוה. Zilembo zinayi zoimira dzina la Mulunguzi akazimasulira ndi YHWH.