Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizitonthozana

Tizitonthozana

Popeza tonsefe ndi opanda ungwiro, timadwala ndipo nthawi zina matenda ake amakhala aakulu. Kodi n’chiyani chimatithandiza kupirira mavuto ngati amenewa?

Kutonthozedwa ndi achibale athu, anzathu komanso Akhristu ena kumatithandiza kupirira.

Mnzathu akatilankhula mokoma mtima zimakhala ngati watipaka mankhwala ochiritsa mabala athu. (Miy. 16:24; 18:24; 25:11) Koma sikuti Akhristu oona amangoyembekezera kuti ena awatonthoze. Iwonso amayesetsa “kutonthoza amene ali m’masautso amtundu uliwonse, chifukwa [nawonso atonthozedwa] ndi Mulungu.” (2 Akor. 1:4; Luka 6:31) Woyang’anira chigawo wina ku Mexico, dzina lake Antonio, anaona umboni wa zimenezi.

Iye atapezeka ndi khansa ya m’magazi, zinamupweteka kwambiri. Koma ankayesetsa kuti asamangokhalira kukhumudwa. Kodi ankachita bwanji zimenezi? Iye ankayesa kukumbukira nyimbo za Ufumu n’kumaziimba kuti amve mawu ake n’kuwaganizira. Kupemphera mokweza ndiponso kuwerenga Baibulo kunamutonthozanso.

Koma Antonio amaona kuti Akhristu anzake ndi amene anamutonthoza kwambiri pa nthawiyo. Iye anati: “Pamene ine ndi mkazi wanga tinkada nkhawa kwambiri, tinkapempha wachibale wina, yemwe ndi mkulu mu mpingo, kuti abwere kudzapemphera nafe. Zimenezi zinkatilimbikitsa kwambiri ndipo mitima yathu inkakhala m’malo.” Iye ananenanso kuti: “Achibale athu komanso Akhristu anzathu anatithandiza kwambiri moti pasanapite nthawi yaitali tinasiya kuda nkhawa kwambiri.” Iye amayamikira kuti ali ndi anzake amene anamusonyeza chikondi komanso kumuthandiza kwambiri.

Mzimu woyera umatithandizanso tikakumana ndi mavuto. Mtumwi Petulo ananena kuti mzimu woyera ndi “mphatso yaulere.” (Mac. 2:38) Mzimuwu unalidi mphatso yaulere kwa anthu ambiri pamene anadzozedwa pa Pentekosite mu 33 C.E. Koma tonsefe tikhoza kulandiranso mzimu woyera. Mphamvu ya Mulungu imeneyi sichepa choncho tiyeni tizimupempha kuti atipatse mphamvu yambiri.—Yes. 40:28-31.

YESETSANI KUTONTHOZA ANTHU AMENE AKUVUTIKA

Mtumwi Paulo anakumana ndi mavuto ambiri ndipo nthawi zina ankatsala pang’ono kufa. (2 Akor. 1:8-10) Koma iye sankaopa kwambiri imfa. Sankada nkhawa kwambiri chifukwa chodziwa kuti Mulungu amuthandiza. Paulo analemba kuti: “Atamandike Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akor. 1:3, 4) Paulo sankangokhalira kudera nkhawa mavuto ake. Koma mavuto ake anamuthandiza kuti azimvera chisoni anthu ena amene anali kuvutika ndiponso kudziwa mmene angawatonthozere.

Antonio uja atachira, anayambiranso kukhala woyang’anira woyendayenda. M’mbuyomo ankaganizira Akhristu anzake koma atachira, iye ndi mkazi wake anayamba kuyesetsa ndithu kukaona odwala ndiponso kuwalimbikitsa. Mwachitsanzo, Antonio atakaona m’bale wina amene ankadwala matenda aakulu, anamva kuti m’baleyu sankafuna kupita ku misonkhano. Antonio anati: “Sikuti m’baleyu sankakonda Yehova kapena Akhristu anzake koma matendawo anamuchititsa kudziona ngati wopanda ntchito.”

Antonio anapita ku phwando linalake kumene m’bale uja anapitanso. Pofuna kumulimbikitsa, Antonio anamupempha kuti apereke pemphero pa phwandolo. Ngakhale kuti m’baleyu ankadzikayikira, anavomera. Antonio anati: “Iye anapereka pemphero labwino kwambiri ndipo kenako anayamba kumva bwino. Anasiya kudziona ngati wopanda ntchito.”

Tonsefe timavutika m’njira zosiyanasiyana. Koma malinga ndi zimene Paulo ananena, kukumana ndi mavuto kumatithandiza kudziwa mmene tingatonthozere ena pamene akuvutika. Tiyeni tonse tiziyesetsa kuganizira mavuto amene Akhristu anzathu akukumana nawo n’kumawatonthoza ngati mmene Yehova Mulungu wathu amachitira.