Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Musataye Mtima!

Musataye Mtima!

Kodi mwatumikira Yehova kwa zaka zambiri ndipo mukulakalaka mwamuna kapena mkazi wanu nayenso atayamba kutumikira Yehova?

Kapena kodi munakhumudwa kwambiri chifukwa choti munthu amene munkamuphunzitsa Baibulo, yemwe ankaoneka kuti mosakayikira akhala Mboni, anasiya kuphunzira?

 Ngati ndi choncho, zitsanzo zotsatirazi zochokera ku Britain zingakuthandizeni kuona kuti simuyenera kutaya mtima. Muonanso zimene mungachite kuti khama lanu lipindule, zomwe zili ngati ‘kutumiza mkate wanu pamadzi,’ n’cholinga choti muthandize anthu amene sanayambebe kutumikira Yehova.—Mlal. 11:1.

MUSASIYE KUTUMIKIRA YEHOVA

Chofunika kwambiri n’kupirira. Muyenera kupitirizabe kukonda choonadi komanso kumamatira Yehova. (Deut. 10:20) Izi ndi zimene mayi wina, dzina lake Georgina, anachita. Iye atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova mu 1970, mwamuna wake dzina lake Kyriacos, anakwiya kwambiri. Anayesetsa kumuletsa kuphunzira ndipo sankalola Mboni za Yehova kufika pakhomo pake. Komanso ankataya buku lililonse la Mboni za Yehova limene walipeza m’nyumba mwake.

Georgina atayamba kusonkhana, Kyriacos anakwiyano koopsa. Tsiku lina anapita ku Nyumba ya Ufumu komweko kuti akayambitse chisokonezo. Mlongo wina ataona kuti Kyriacos amalankhula bwino Chigiriki kuposa Chingelezi, anaimbira foni m’bale wachigiriki wa mpingo wina kuti adzawathandize. Kyriacos anamvetsera zimene m’baleyo analankhula chifukwa anamulankhula mokoma mtima. Ndipo kwa miyezi ingapo, anaphunzira naye Baibulo koma kenako Kyriacos anasiya kuphunzira.

Kyriacos anayambanso kuchitira nkhanza Georgina kwa zaka zitatu zotsatira ndipo anamuuza kuti akangobatizidwa, banja lithera pomwepo. Pa tsiku limene Georgina ankakabatizidwa, anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize kuti mwamuna wake asamusiye. Anzake ena a Mboni atapita pagalimoto kukamutenga kuti azipita kumsonkhano, mwamuna wake anati: “Tsogolani, ife tizikutsatirani m’mbuyo pa galimoto yathu.” Kyriacos anamvetsera nawo chigawo chonse cha m’mawa ndipo anaonerera mkazi wake akubatizidwa.

Patatha zaka 40 kuchokera pamene anakumana ndi a Mboni, Kyriacos anabatizidwa

Patapita nthawi, Kyriacos anasiya kuzunza kwambiri mkazi wake ndipo pang’ono ndi pang’ono anayamba kusintha kwambiri. Patatha zaka 40 kuchokera pamene anakumana ndi a Mboni, Kyriacos anabatizidwa. Kodi n’chiyani chinamuthandiza? Iye anati: “Ndinachita chidwi kwambiri kuona kuti Georgina sanalole chilichonse kumulepheretsa kutumikira Yehova.” Georgina anati: “Ngakhale kuti mwamuna wanga ankandiletsa, ndinatsimikiza mtima kuti sindisiya kutumikira Mulungu wanga. Pa nthawi yonseyi ndinkapemphera kwa Yehova ndipo sindinataye mtima ngakhale pang’ono.”

KUFUNIKA KOVALA UMUNTHU WATSOPANO

Chinthu china chofunika kuti muthandize mwamuna kapena mkazi wanu ndicho kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe achikhristu. Mtumwi Petulo analangiza akazi achikhristu kuti: “Muzigonjera amuna anu kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu.” (1 Pet. 3:1) Mayi wina dzina lake Christine anatsatira malangizo amenewa ngakhale kuti panatenga zaka zambiri mwamuna wake asanakhale Mboni. Zaka 20 zapitazo pamene Christine anakhala Mboni, mwamuna wake John sankakhulupirira n’komwe Mulungu. John sankachita chidwi ndi zachipembedzo komabe ankaona kuti mkazi wake ankakonda kwambiri zimene ankaphunzira. Iye anati: “Ndinkaona kuti mkazi wanga ankasangalala kwambiri ndi zomwe ankaphunzira. Zinamuthandiza kukhala wolimba mtima komanso wodalirika ndipo izi zinandithandiza pa nthawi yovuta.”

Christine sankaumiriza mwamuna wake kuti akhale wa Mboni. Mwamuna wakeyo anati: “Christine ankadziwa kuti ndi bwino asamandiuze za chipembedzo chake ndipo ankaleza nane mtima n’kumandisiya kuti ndiziphunzira mmene ndikufunira.” Christine ankati akapeza nkhani imene akuona kuti John akhoza kusangalala nayo mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani!, mwina yokhudza sayansi kapena chilengedwe, ankamusonyeza n’kumuuza kuti: “Ndikuganiza kuti nkhani iyi ikhoza kukusangalatsani.”

Patapita nthawi, John anapuma pa ntchito ndipo ankangogwira tintchito tapakhomo. Popeza anali ndi nthawi yambiri yoganizira mayankho a mafunso okhudza moyo, iye anayamba kudzifunsa kuti, ‘Kodi anthufe tinangopezeka mwangozi kapena tinalengedwa ndi cholinga?’ Tsiku lina m’bale amene ankakonda kucheza ndi John anam’pempha kuti aziphunzira naye Baibulo ndipo John anavomera. John anati: “Ndinavomera kuti tiziphunzira chifukwa ndinali nditayamba kukhulupirira kuti kuli Mulungu.”

Izi zikusonyeza kuti Christine anachita bwino kusataya mtima. John anabatizidwa patatha zaka 20. Pa nthawi yonseyi, mkazi wake ankapemphera kwa Mulungu kuti John adziwe choonadi. Panopa onse akutumikira Mulungu mwakhama. John anati: “Pali zinthu ziwiri zimene zinandithandiza. Zinthu zake ndi kukoma mtima ndiponso mzimu waubwenzi wa Mboni za Yehova. Ndipo ukakwatira mkazi wa Mboni za Yehova, umadziwa kuti wakwatira munthu wokhulupirika, wodalirika komanso wachikondi.” Christine anatsatira malangizo a pa 1 Petulo 3:1 ndipo anamuthandiza.

 MBEWU ZINABALA ZIPATSO PATAPITA ZAKA ZAMBIRI

Nanga kodi tingatani ngati amene tinkaphunzira naye Baibulo anasiya pa zifukwa zina? Zikatere, ndi bwino kukumbukira mawu a Mfumu Solomo. Iye anati: “Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo, chifukwa sukudziwa pamene padzachite bwino, kaya pano kapena apo, kapena ngati zonsezo zidzachite bwino.” (Mlal. 11:6) Nthawi zina pamatenga nthawi yaitali kuti mbewu za choonadi zikule mu mtima mwa munthu. Komabe m’kupita kwa nthawi, munthu angayambe kuona kufunika kokhala pa ubwenzi ndi Mulungu. (Yak. 4:8) Tsiku lina mukhoza kudzadabwa munthuyo atayamba kutumikira Yehova.

Chitsanzo china ndi cha Alice amene anasamuka kuchoka ku India kupita ku England. Mu 1974, anayamba kuphunzira Baibulo. Iye anali Muhindi koma ankafuna kuti azilankhula bwino Chingelezi. Anapitiriza kuphunzira kwa zaka zingapo ndipo nthawi zina ankasonkhana ndi mpingo wa Chingelezi. Iye ankadziwa kuti zimene ankaphunzirazo zinali choonadi koma sankazindikira kwenikweni kufunika kwake. Komanso ankangoganiza za ndalama ndipo ankakonda kupita kumapate. Patapita nthawi, anasiya kuphunzira.

Patapita zaka pafupifupi 30, mayi wina dzina lake Stella yemwe anaphunzirapo Baibulo ndi Alice, analandira kalata yochokera kwa Alice. Kalatayo inati: “Ndine Alice amene munkaphunzira naye Baibulo mu 1974. Ndikukhulupirira kuti musangalala kwambiri kudziwa kuti ndabatizidwa pa msonkhano wachigawo wa posachedwapa. Munandithandiza kwambiri pa moyo wanga. Munabzala mbewu za choonadi mumtima mwanga ndipo ngakhale kuti sindinali wokonzeka kudzipereka kwa Mulungu, ndinasungabe mbewuzo mumtima mwanga.”

Kalata yochokera kwa Alice imene analembera Stella inali ndi mawu akuti: “Ndine Alice amene munkaphunzira naye Baibulo mu 1974. Ndikukhulupirira kuti musangalala kwambiri kudziwa kuti ndabatizidwa pa msonkhano wachigawo wa posachedwapa”

Kodi chinachitika n’chiyani kuti Alice afike pobatizidwa? Alice anafotokoza kuti mwamuna wake anamwalira mu 1997 ndipo izi zinachititsa kuti akhale wachisoni kwambiri. Tsiku lina iye anapemphera kwa Mulungu kuti amuthandize. Patangodutsa mphindi 10 kunabwera anthu awiri a Mboni za Yehova omwe ankalankhula Chipunjabi ndipo anamusiyira kapepala kakuti Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Okondedwa Akufa? Alice anaona kuti pemphero lake layankhidwa ndipo anaganiza zoyamba kusonkhana ndi Mboni za Yehova. Koma sankadziwa kumene a Mboni ankasonkhana. Mwamwayi, iye anapeza kope limene Stella anamupatsa lomwe munali adiresi ya mpingo wachipunjabi. Alice anapita ku Nyumba ya Ufumu ndipo abale ndi alongo anamulandira mosangalala. Alice anati: “Nditabwerera kunyumba ndinkakumbukirabe chikondi chimene anandisonyeza. Chikondi chawocho chinandithandiza kuchepetsa chisoni changa.”

Alice anayamba kupezeka pa misonkhano nthawi zonse ndipo anayambiranso kuphunzira Baibulo. Iye anayambanso kuphunzira kulankhula bwino Chipunjabi ndipo anabatizidwa mu 2003. Iye anamaliza kalata yake ndi mawu akuti: “Zikomo kwambiri chifukwa chodzala mbewu za choonadi mumtima mwanga zaka 29 zapitazo komanso chifukwa cha chitsanzo chanu chabwino.”

“Zikomo kwambiri chifukwa chodzala mbewu za choonadi mumtima mwanga zaka 29 zapitazo komanso chifukwa cha chitsanzo chanu chabwino.”—Alice

Kodi tikuphunzira chiyani pa zitsanzo zimenezi? Zingatenge nthawi yaitali kuti munthu aphunzire choonadi. Koma ngati munthuyo ali woona mtima, wodzichepetsa komanso akufunadi kudziwa Mulungu, Yehova angamuthandize kuti mbewu za choonadi zimene zili mumtima mwake zikule. Kumbukirani zimene Yesu ananena m’fanizo lake. Iye anati: “Mbewuzo zimamera ndi kukula. Koma mmene zimenezi zimachitikira, mwiniwakeyo sadziwa ayi. Pang’onopang’ono, payokha nthaka ija imabala zipatso. Choyamba mmera umabiriwira, kenako umatulutsa ngala, pamapeto pake maso okhwima a tirigu amaonekera m’ngalamo.” (Maliko 4:27, 28) Mbewu zimakula pang’onopang’ono komanso ‘pazokha.’ Choncho palibe Mkhristu aliyense amene amadziwa mmene mbewuzo zimakulira. Chotero pitirizani kubzala mbewu mowolowa manja ndipo mudzakolola zochuluka.

Komanso musaiwale kuti pemphero ndi lofunika kwambiri. Georgina ndi Christine ankapemphera kwa Yehova. Mukapanda kutaya mtima komanso ‘mukamalimbikira kupemphera,’ “pakapita masiku ambiri” mukhoza kudzapeza “mkate” umene munatumiza pa madzi.—Aroma 12:12; Mlal. 11:1.