Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Okonda Yehova ‘Alibe Chowakhumudwitsa’

Anthu Okonda Yehova ‘Alibe Chowakhumudwitsa’

“Okonda chilamulo chanu amapeza mtendere wochuluka, ndipo palibe chowakhumudwitsa.”—SAL. 119:165.

1. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene wothamanga wina anachita?

KUYAMBIRA ali mtsikana, Mary Decker ankadziwika kuti anali katswiri wothamanga. Anthu onse ankaona kuti iye ndi amene angapambane pa mpikisano wapadziko lonse wothamanga mamita 3,000 m’chaka cha 1984. Koma iye analephera chifukwa anapunthwa mwendo wa mnzake n’kugwa. Anavulala kwambiri ndipo anthu anabwera kudzamunyamula akulira. Komabe Mary sanasiye kuchita masewero othamanga. Pasanathe chaka, iye anayambiranso kuthamanga ndipo mu 1985 anathamanga pa mpikisano wina mofulumira kuposa aliyense amene anathamangapo.

2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Akhristu ali pa mpikisano wothamanga? Nanga cholinga chathu chiyenera kukhala chiyani?

2 Akhristufe tilinso pa mpikisano wothamanga. Cholinga chathu chiyenera kukhala kupambana. Koma kuti tipambane sikuti timafunika kuthamanga mwamsanga kuposa anzathu. Komabe sizikutanthauza kuti ndi mpikisano wongothamanga mwaulesi. Uli ngati mpikisano wothamanga mtunda wautali kwambiri ndipo pamafunika kupirira kuti tipambane. Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito fanizo la othamanga m’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Korinto. Mzinda umenewu unkadziwika ndi masewera othamanga. Iye analemba kuti: “Kodi simukudziwa kuti ochita mpikisano wa liwiro amathamanga onse, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphoto? Thamangani m’njira yoti mukalandire mphotoyo.”—1 Akor. 9:24.

3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti aliyense wothamanga pa mpikisanowu akhoza kulandira moyo wosatha?

3 Baibulo limatiuza kuti tizithamanga pa mpikisano umenewu. (Werengani 1 Akorinto 9:25-27.) Mphoto yake ndi moyo wosatha. Odzozedwa adzalandira moyo kumwamba  ndipo ena tonsefe tidzalandira moyowu padziko lapansi. Koma mosiyana ndi mipikisano ina, othamanga onse pa mpikisano umenewu adzalandira mphoto ngati atapirira n’kufika kumapeto. (Mat. 24:13) Anthu omwe sadzalandira mphoto ndi okhawo amene satsatira malamulo a mpikisanowu kapena amene safika kumapeto. Ndi mpikisano wokhawu umene opambana amalandira moyo wosatha.

4. N’chiyani chimachititsa kuti mpikisano wathu wa moyo wosatha ukhale wovuta?

4 Kufika kumapeto si kophweka. Pamafunika kuchita zonse zofunika komanso kukhala ndi cholinga. Yesu Khristu yekha ndi amene anafika kumapeto kwa mpikisanowu popanda kupunthwa ngakhale kamodzi. Koma Yakobo analemba kuti Akhristu onse ‘amapunthwa nthawi zambiri.’ (Yak. 3:2) Zimenezitu n’zoona. Tonsefe timavutika ndi kupanda ungwiro kwathu komanso kwa anthu ena. Choncho nthawi zina timapunthwa n’kuyamba kuyenda mwapendapenda. Nthawi zina tikhoza kugwa kumene komabe timadzuka n’kuyambanso kuthamanga. Ena amagwa kwambiri moti amafunika kuthandizidwa kuti adzuke n’kuyambiranso kuthamanga. Choncho n’zotheka kupunthwa kamodzi kapena kangapo mwinanso kugwa kumene.—1 Maf. 8:46.

Mukagwa, landirani thandizo n’kudzuka

MUKAPUNTHWA, MUSASIYE KUTHAMANGA

5, 6. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Akhristu ‘alibe chowakhumudwitsa’? Nanga n’chiyani chingawathandize kuti adzukenso akagwa? (b) N’chifukwa chiyani anthu ena akagwa sadzuka?

5 Mwina munthu akaona mawu oti “kupunthwa” kapena “kugwa” m’Baibulo akhoza kuganiza kuti akunena za zinthu zofanana. Koma m’Baibulo, mawu amenewa nthawi zina amanena zinthu zosiyana. Mwachitsanzo, taonani mawu a pa Miyambo 24:16 amene amati: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso. Koma anthu oipa, tsoka lidzawapunthwitsa.”

6 Yehova sadzalola kuti anthu amene amamukhulupirira apunthwe kapena kugwa moti sangathe kudzukanso. Tikudziwa kuti Yehova adzatithandiza ‘kudzukanso’ n’cholinga choti tipitirize kumutumikira mokhulupirika. Zimenezitu n’zolimbikitsa kwa anthu onse amene  amatumikira Yehova ndi mtima wonse. Koma anthu oipa akagwa safuna kudzukanso. Iwo safuna kuthandizidwa ndi mzimu wa Mulungu kapena anthu ake ndipo mwina amakana thandizolo. Koma palibe chimene chingapunthwitse anthu ‘okonda chilamulo cha Yehova’ mpaka kuwachotsa pa mpikisano wokalandira moyo wosatha.—Werengani Salimo 119:165.

7, 8. Kodi zingatheke bwanji kuti munthu amene ‘wagwa’ akhalebe wolungama pa maso pa Mulungu?

7 Chifukwa cha kupanda ungwiro, ena amachita machimo ang’onoang’ono, mwinanso mobwerezabwereza. Koma iwo amakhalabe olungama pa maso pa Yehova ngati ‘atadzuka,’ kutanthauza kulapa n’kuyambiranso kutumikira Mulungu mokhulupirika. Umboni wa zimenezi ndi mmene Mulungu ankachitira zinthu ndi Aisiraeli. (Yes. 41:9, 10) Lemba la Miyambo 24:16, limene talitchula poyamba lija, limatsindika za ‘kudzuka’ osati ‘kugwa.’ Mulungu wathu wachifundo amatithandiza kuti tidzuke. (Werengani Yesaya 55:7.) Yehova ndi Yesu Khristu amatidalira ndipo amatilimbikitsa kuti tikagwa, ‘tizidzuka.’—Sal. 86:5; Yoh. 5:19.

8 Ngakhale munthu atakhala kuti wapunthwa kapena kugwa pa mpikisano wothamanga akhoza kumalizabe mpikisanowo ngati atadzuka mwamsanga. Pa mpikisano wathu wokalandira moyo, sitidziwa ‘tsiku ndi ola’ limene mapeto adzafike. (Mat. 24:36) Koma ngati sitipunthwapunthwa, tikhoza kuthamanga pa liwiro labwino mpaka kumaliza. Ndiyeno kodi tingapewe bwanji kupunthwa?

ZOPUNTHWITSA ZIMENE ZINGATILEPHERETSE KUMALIZA MPIKISANO

9. Kodi tikambirana zinthu ziti zimene zingatipunthwitse?

9 Tiyeni tikambirane zinthu zisanu zimene zingatipunthwitse. Zinthu zake ndi izi: Zimene timalakwitsa kapena kulephera kuchita, zimene timalakalaka, anthu ena akatilakwira, tikamazunzidwa komanso zolakwa za anthu ena. Kumbukirani kuti ngati titapunthwa, Yehova amaleza nafe mtima. Sikuti nthawi yomweyo amayamba kutiona kuti ndife osakhulupirika.

10, 11. Kodi Davide anali ndi vuto lotani?

10 Zimene timalakwitsa kapena kulephera kuchita tingaziyerekezere ndi timiyala tomwe tingapezeke mumsewu umene tikuthamanga. Tikaona zimene zinachitika pa moyo wa Mfumu Davide ndi mtumwi Petulo, tingathe kuona kuti anthu awiriwa analakwitsapo zinthu. Wina analephera kudziletsa ndipo wina anali wamantha.

11 Nkhani ya Mfumu Davide yokhudza Bati-seba imasonyeza kuti iye anali ndi vuto la kusadziletsa. Komanso pamene Nabala anamuchitira chipongwe, Davide anatsala pang’ono kuchita zoipa. N’zoona kuti ankalephera kudziletsa koma iye sanasiye kuyesetsa kuchita zinthu zokondweretsa Yehova. Anthu ena akamuthandiza, iye ankayambanso kuona zinthu mmene Mulungu amazionera.—1 Sam. 25:5-13, 32, 33; 2 Sam. 12:1-13.

12. Kodi n’chiyani chinathandiza Petulo kuthamangabe mpikisano ngakhale kuti ankalakwitsa zinthu zina?

12 Nayenso Petulo analakwitsa zinthu zina chifukwa choopa anthu komabe sanasiye kukhala wokhulupirika kwa Yesu ndi Yehova. Mwachitsanzo, iye anakana Mbuye wake, osati kamodzi koma katatu. (Luka 22:54-62) Pa nthawi inanso, Petulo analephera kuchita zinthu ngati Mkhristu. Iye anayamba kusala Akhristu a mitundu ina ngati kuti Akhristu achiyuda ndi amene anali ofunika kwambiri. Apatu Petulo analakwitsa. Koma mtumwi Paulo ankadziwa kuti Akhristu sayenera kusalana. Choncho zisanafike posokoneza anthu ena mu mpingo, Paulo anamudzudzula mosapita m’mbali. (Agal. 2:11-14) Kodi Petulo anakhumudwa chifukwa cha kunyada n’kusiya kutumikira Mulungu? Ayi. Iye anaganizira bwino uphungu wa Paulo, kuutsatira ndipo anapitirizabe pa mpikisano wokalandira moyo.

13. Kodi matenda angapunthwitse bwanji munthu?

13 Nthawi zina timalephera kuchita zinthu zina chifukwa cha matenda. Vuto limeneli  likhozanso kutipunthwitsa. Lingachititse kuti tisamathamange bwinobwino mwinanso kusiya kumene. Mwachitsanzo, mlongo wina wa ku Japan anayamba kudwala patatha zaka 17 kuchokera pamene anabatizidwa. Iye ankangoganizira za matenda akewo mpaka anafooka n’kusiya kusonkhana ndi kulalikira. Akulu awiri anapita kukamuona. Chifukwa cholimbikitsidwa ndi mawu awo, mlongoyu anayambanso kusonkhana. Iye anati: “Mmene abale anandilandirira nditafika ku Nyumba ya Ufumu, zinandikhudza kwambiri moti mpaka ndinagwetsa misozi.” Panopa mlongoyu anayambiranso kutumikira Mulungu mwakhama.

14, 15. N’chiyani chimafunika ngati tikulakalaka zinthu zoipa? Perekani chitsanzo.

14 Anthu ambiri amapunthwa ndi zimene amalakalaka. Tikakumana ndi vuto limeneli, tiyenera kuchitapo kanthu mwamsanga kuti tikhalebe oyera m’mbali zonse za moyo wathu. Kumbukirani malangizo a Yesu akuti mophiphiritsira tiyenera ‘kutaya’ chilichonse chimene chingatipunthwitse, ngakhale litakhala diso kapena dzanja lathu. Zimenezitu zikuphatikizapo maganizo ndi zochita zoipa zimene zingachititse munthu kusiya kuthamanga.—Werengani Mateyu 5:29, 30.

15 M’bale wina, amene anakulira m’banja lachikhristu, analemba kuti kwa nthawi yaitali anali ndi vuto lolakalaka kugonana ndi amuna anzake. Iye anati: “Ndinkaona kuti kulikonse ndinkangokhala ngati mlendo.” Pamene amakwanitsa zaka 20 n’kuti ali mpainiya wokhazikika komanso mtumiki wothandiza. Koma kenako anachita tchimo lalikulu ndipo akulu anamuthandiza pogwiritsa ntchito Malemba. Chifukwa chakuti anayamba kupemphera, kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kukhala ndi mtima wofuna kuthandiza ena, iye anadzuka n’kuyambiranso kutumikira Mulungu mokhulupirika. Patapita zaka, iye anati: “Nthawi zina maganizo oipa aja amandibwererabe koma sindilola kugonja. Ndikudziwa kuti Yehova sangalole kuti ndiyesedwe kuposa pamene ndingathe kupirira. Ndikukhulupirira kuti Mulungu amadziwa zoti ndikhoza kupirira.” Pomaliza m’baleyu anati: “M’dziko latsopano Mulungu adzandifupa chifukwa choyesetsa kupirira mavuto angawa. Choncho ndiyesetsa kuti ndisagonje.” Iye sakufuna ngakhale pang’ono kusiya kuthamanga pa mpikisano wokalandira moyo.

16, 17. (a) N’chiyani chinathandiza m’bale amene ankaona kuti sanachitiridwe zachilungamo? (b) Kuti tipewe kupunthwa, kodi tiyenera kuyang’ana kwa ndani?

16 Tikhozanso kupunthwa ngati Akhristu anzathu atilakwira. M’bale wina ku France, yemwe anali mkulu, anakwiya kwambiri poona kuti sanachitiridwe zachilungamo. Iye anasiya kusonkhana ndiponso kulalikira. Akulu awiri anamuyendera ndipo anamumvetsera bwinobwino pamene ankafotokoza mbali yake. Iwo anamulimbikitsa kutulira Yehova nkhawa zakezo ndipo anamuuza kuti chofunika kwambiri ndi kukondweretsa Mulungu basi. Iye anamvera ndipo pasanapite nthawi yaitali anayambiranso kutumikira mwakhama.

17 Akhristu tonse sitiyenera kuyang’ana kwa anthu opanda ungwiro, koma kwa Yesu Khristu, yemwe ndi mutu wa mpingo. Maso a Yesu, omwe ali “ngati lawi lamoto,” amaona chilichonse mmene chililidi choncho akhoza kuona bwino zinthu kuposa ifeyo. (Chiv. 1:13-16) Mwachitsanzo, iye amadziwa kuti zinthu zimene ife tikuona kuti si zachilungamo, zikhoza kukhala zabwinobwino kungoti ifeyo sitikuzimvetsa kapena tikungoganiza kuti sizinayende bwino. Yesu adzakonza zinthu zonse mu mpingo mwachilungamo komanso pa nthawi yoyenera. Choncho tisalole zochita za Akhristu anzathu kutipunthwitsa pa mpikisano wathu.

18. N’chiyani chingatithandize kupirira tikakumana ndi vuto lililonse?

18 Zinthu zinanso zimene zingatipunthwitse ndi kuzunzidwa komanso zolakwa za Akhristu anzathu. M’fanizo la wofesa mbewu, Yesu  ananena kuti anthu ena amapunthwa chifukwa cha “chisautso kapena mazunzo” zobwera chifukwa choti aphunzira mawu. Kaya ozunzawo ndi a m’banja lathu, aneba kapena akuluakulu a boma, anthu amene “alibe mizu” m’choonadi ndi amene amapunthwa. (Mat. 13:21) Koma ngati tikhalabe ndi mtima wabwino, mbewu za Ufumu zidzazika mizu m’mitima yathu ndipo tidzakhala ndi chikhulupiriro cholimba. Tikakumana ndi mavuto, tizipemphera n’kumaganizira zinthu zotamandika. (Werengani Afilipi 4:6-9.) Yehova akhoza kutithandiza kuti tipirire mayesero komanso kuti tisalole vuto lililonse kutipunthwitsa.

Musalole chilichonse kukulepheretsani kumaliza mpikisano

19. Kodi tingatani kuti zolakwa za ena zisatipunthwitse?

19 N’zomvetsa chisoni kuti anthu ena apunthwa n’kusiya kuthamanga chifukwa cha kupanda ungwiro kwa anthu ena. Iwo amakhumudwa chifukwa chosiyana maganizo ndi anthu ena pa nkhani zokhudza chikumbumtima. (1 Akor. 8:12, 13) Ngati munthu wina watilakwira, kodi ndi bwino kuikoka nkhaniyo? Baibulo limalangiza Akhristu kuti aleke kuweruza ena. Koma limawalimbikitsa kukhululuka komanso kupewa kuumirira maganizo awo. (Luka 6:37) Mukakumana ndi zinthu zomwe zingakupunthwitseni ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi palidi vuto kapena ndikungofuna kuti anthuwo achite zimene ineyo ndikuona kuti n’zoyenera? Popeza abalewa ndi opanda ungwiro, kodi ndidzalola kuti zolakwa zawo zindilepheretse mpikisano wokalandira moyo?’ Kukonda Yehova kungatithandize kuti tisalole zochita za munthu aliyense kutilepheretsa kumaliza nawo mpikisanowu.

MUZIPIRIRA POTHAMANGA NDIPO MUZIPEWA ZOPUNTHWITSA

20, 21. Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani pa mpikisano wokalandira moyo?

20 Kodi inuyo mukufunitsitsa ‘kuthamanga mpaka pa mapeto’? (2 Tim. 4:7, 8) Ngati ndi choncho, muziphunzira Baibulo panokha. Muzifufuza zinthu pogwiritsa ntchito Baibulo ndiponso mabuku athu komanso muzisinkhasinkha. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muzindikire zinthu zimene zingakupunthwitseni. Muzipempha mzimu woyera kuti ukupatseni mphamvu kuti muzitumikira bwino Mulungu. Kumbukirani kuti kupunthwa kapena kugwa sikuchititsa kuti munthu alephere mpikisanowu chifukwa akhoza kudzuka n’kuyambiranso kuthamanga. Akhozanso kuphunzirapo kanthu pa mayesero amene wakumana nawo.

21 Baibulo limasonyeza kuti munthu amene ali pa mpikisano wokalandira moyo wosatha amafunika kuchita khama osati kungokhala. Tifunika kuthamanga ndithu kuti tikapeze moyo. Tikamatero, “mtendere wochuluka” wochokera kwa Yehova udzakhala ngati mphepo yotikankhira kutsogolo kuti tipitirizebe kuthamanga. (Sal. 119:165) Tikukhulupirira kuti ngati sitisiya kuthamanga pa mpikisanowu, Yehova apitirizabe kutidalitsa panopa mpaka muyaya.—Yak. 1:12.