Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi “mkazi” wotchulidwa pa Yesaya 60:1 ndi ndani, nanga ‘anaimirira’ bwanji komanso anaonetsa bwanji “kuwala”?

Lemba la Yesaya 60:​1, limati: “Imirira mkazi iwe! Onetsa kuwala kwako, chifukwa kuwala kwako kwafika. Ulemerero wa Yehova wakuunikira.” Nkhani yonse ikusonyeza kuti “mkaziyu” anali Ziyoni kapena Yerusalemu, yemwe anali likulu la Yuda pa nthawiyo. a (Yes. 60:14; 62:​1, 2) Mzindawu umaimira mtundu wonse wa Isiraeli. Mawu amene Yesaya ananenawa, akubweretsa mafunso awiri: Loyamba, ndi liti pamene Yerusalemu ‘anaimirira’ ndiponso kuonetsa kuwala, nanga anachita bwanji zimenezi? Lachiwiri, kodi mawu a Yesayawa akukwaniritsidwanso kwambiri mu nthawi yathu?

Ndi liti pamene Yerusalemu ‘anaimirira’ ndiponso kuonetsa kuwala, nanga anachita bwanji zimenezi? Pa nthawi imene Ayuda anali ku ukapolo ku Babulo kwazaka 70, Yerusalemu ndi kachisi wake anali bwinja. Koma Ababulo atagonjetsedwa ndi Amedi ndi Aperisiya, Aisiraeli omwe ankakhala m’madera onse olamuliridwa ndi Ababulo anamasulidwa kuti abwerere kwawo ndi kukabwezeretsa kulambira koona. (Ezara 1:​1-4) Kuyambira mu 537 B.C.E., anthu okhulupirika amene anatsala m’mafuko onse 12, anabwerera. (Yes. 60:4) Iwo anayamba kupereka nsembe kwa Yehova, kupanga zikondwerero ndiponso kumanganso kachisi. (Ezara 3:​1-4, 7-11; 6:​16-22) Apa ulemerero wa Yehova unayambiranso kuunikira Yerusalemu, kutanthauza anthu a Mulungu omwe anabwerera kwawo. Kenako nawonso anayamba kuwala pakati pa anthu amitundu ina amene sankadziwa Yehova.

Koma maulosi a Yesaya onena za kubwezeretsa anangokwaniritsidwa pang’ono pa nthawiyo. Aisiraeli ambiri sanapitirize kumvera Mulungu. (Neh. 13:27; Mal. 1:​6-8; 2:​13, 14; Mat. 15:​7-9) Pambuyo pake, anafika pokana Yesu Khristu, yemwe ndi Mesiya. (Mat. 27:​1, 2) Mu 70 C.E., Yerusalemu ndi kachisi wake anawonongedwa kachiwiri.

Yehova anali ataneneratu kuti zimenezi zidzachitika. (Dan. 9:​24-27) Choncho, sichinali cholinga chake kuti Yerusalemu wa padziko lapansi akwaniritse mbali iliyonse ya ulosi wa pa Yesaya chaputala 60, wonena za kubwezeretsa.

Kodi mawu a Yesaya akukwaniritsidwanso kwambiri mu nthawi yathu? Inde, koma akukwaniritsidwa pa mkazi wophiphiritsa, yemwe ndi “Yerusalemu wam’mwamba.” Ponena za mkaziyu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndi mayi athu.” (Agal. 4:26) Yerusalemu wam’mwamba ndi mbali yakumwamba ya gulu la Mulungu, yomwe ndi angelo okhulupirika. “Ana” ake ndi Yesu ndi Akhristu odzozedwa okwana 144,000, omwe mofanana ndi Paulo, ali ndi chiyembekezo cha kumwamba. Akhristu odzozedwawa amapanga “mtundu woyera,” womwe ndi “Isiraeli wa Mulungu.”—1 Pet. 2:9; Agal. 6:16.

Kodi Yerusalemu wam’mwamba ‘anaimirira’ bwanji nanga anaonetsa bwanji “kuwala”? Iye anachita zimenezi kudzera mwa ana ake odzozedwa a padziko lapansi. Tiyeni tione kufanana kwa zimene zinawachitikira ndi zomwe zinaloseredwa pa Yesaya chaputala 60.

Akhristu odzozedwa anafunika ‘kuimirira’ chifukwa anali mum’dima wophiphiritsa pa nthawi imene mpatuko unafalikira atumwi onse atamwalira. (Mat. 13:​37-43) Choncho, iwo anali mu ukapolo wa Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zabodza. Odzozedwa anakhala ali mu ukapolowu mpaka “mapeto a nthawi ino,” omwe anayamba mu 1914. (Mat. 13:​39, 40) Pasanapite nthawi, mu 1919, iwo anamasulidwa ndipo nthawi yomweyo anayamba kuonetsa kuwala pogwira ntchito yolalikira mwakhama. b Kwa zaka zonsezi, anthu ochokera m’mitundu yonse akhala akutsatira kuwalaku kuphatikizapo anthu a Isiraeli wa Mulungu amene anatsala, omwe ndi “mafumu” otchulidwa pa Yesaya 60:3.—Chiv. 5:​9, 10.

M’tsogolomu, Akhristu odzozedwa adzaonetsa kwambiri kuwala kwa Mulungu. Kodi adzachita bwanji zimenezi? Akadzamaliza utumiki wawo wa padziko lapansi, iwo adzakhala mbali ya “Yerusalemu Watsopano” kapena mkwatibwi wa Khristu, yemwe ndi mafumu ndi ansembe 144,000.—Chiv. 14:1; 21:​1, 2, 24; 22:​3-5.

Yerusalemu Watsopano adzachita zambiri pokwaniritsa ulosi wa pa Yesaya 60:1. (Yerekezerani Yesaya 60:​1, 3, 5, 11, 19, 20 ndi Chivumbulutso 21:​2, 9-11, 22-26.) Yerusalemu wapadziko lapansi anali likulu la boma la Isiraeli wakale, choncho nayenso Yerusalemu Watsopano limodzi ndi Khristu, adzakhala boma la ulamuliro watsopano. Kodi Yerusalemu Watsopano akutsika bwanji “kuchokera kumwamba kwa Mulungu”? Akuchita zimenezi pochita zinthu zimene zikukhudza dziko lapansi. Anthu oopa Mulungu ochokera m’mitundu yonse ‘adzaunikiridwa ndi kuwala kwake.’ Iwo adzamasulidwanso ku uchimo ndi imfa. (Chiv. 21:​3, 4, 24) Zotsatira zake n’zakuti ‘zinthu zonse zidzabwezeretsedwa’ ngati mmene Yesaya ndi aneneri ena ananenera. (Mac. 3:21) Kubwezeretsa kwakukulu kunayamba pamene Khristu anakhala Mfumu ndipo kudzatha pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000.

a Pa Yesaya 60:​1, Baibulo la Dziko Latsopano limagwiritsa ntchito mawu akuti “mkazi” osati “Ziyoni” kapena “Yerusalemu,” chifukwa mawu a Chiheberi omwe anawamasulira kuti “imirira” komanso “onetsa kuwala,” amasonyeza kuti amene akuuzidwayo ndi wamkazi, ngatinso mmene zilili ndi mawu akuti “iwe.”

b Kubwezeretsedwa kwa kulambira koona komwe kunachitika mu 1919 ndi kumene kwafotokozedwanso pa Ezekieli 37:​1-14 ndi Chivumbulutso 11:​7-12. Ezekieli ananeneratu kuti Akhristu onse odzozedwa, adzamasulidwa mu ukapolo pambuyo pa nthawi yaitali. Ulosi wa pa Chivumbulutso umanena za kubadwanso kophiphiritsa kwa kagulu ka abale odzozedwa omwe anayambiranso kutsogolera pambuyo pokhala kwakanthawi asakutha kutumikira Yehova bwinobwino chifukwa anamangidwa mopanda chilungamo. Mu 1919,” iwo anaikidwa kukhala “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru.”—Mat. 24:45.