Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZOTI NDIPHUNZIRE

Muziphunzira Mwakhama Kuti Mukhale Maso

Muziphunzira Mwakhama Kuti Mukhale Maso

Werengani Danieli 9:​1-19 kuti muone kufunika kophunzira mwakhama.

Muziona nkhani yonse. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zinali zitangochitika kumene, nanga zinamukhudza bwanji Danieli? (Dan. 5:29–6:5) Kodi mukanakhala Danieli mukanamva bwanji?

Muzifufuza mozama. Kodi ndi “mabuku opatulika” ati omwe Danieli ankawerenga? (Dan. 9:​2, mawu a m’munsi; w11 1/1 22 ¶2) N’chifukwa chiyani iye analapa machimo ake komanso a Aisiraeli onse? (Lev. 26:​39-42; 1 Maf. 8:​46-50; dp 182-184) Kodi pemphero la Danieli likusonyeza bwanji kuti ankaphunzira Mawu a Mulungu mwakhama?—Dan. 9:​11-13.

Onani zimene mukuphunzirapo. Dzifunseni kuti:

  • ‘Kodi ndingatani kuti ndisasokonezedwe ndi zochitika za m’dzikoli?’ (Mika 7:7)

  • ‘Kodi kuphunzira Baibulo mwakhama ngati mmene Danieli ankachitira kungandithandize bwanji?’ (w04 8/1 12 ¶17)

  • ‘Kodi ndi nkhani ziti zomwe ndingaphunzire zimene zingandithandize “kukhalabe maso”?’ (Mat. 24:​42, 44; w12 8/15 5 ¶7-8)