Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Muzolowere Mukasamukira Mumpingo Wina?

Kodi Mungatani Kuti Muzolowere Mukasamukira Mumpingo Wina?

KODI munayamba mwasamukirapo mumpingo wina? Ngati ndi choncho mukhoza kuvomereza zimene Jean-Charles ananena. Iye anati: “Zimakhala zovuta kuzolowera mpingo watsopano, pa nthawi yomweyo n’kumaonetsetsa kuti aliyense m’banja lanu akupitiriza kuchita zinthu zomwe zingalimbitse ubwenzi wake ndi Yehova.” Kuwonjezera pa kupeza ntchito, malo okhala, mwinanso sukulu zatsopano, anthu omwe asamuka amafunika kuzolowera nyengo yatsopano, chikhalidwe china komanso gawo latsopano lolalikira.

Nicolas ndi Céline anakumana ndi vuto la mtundu wina. Iwo anavomera ofesi ya nthambi ya ku France itawapempha kuti asamukire mumpingo wina. Iwo anati: “Poyamba tinasangalala kwambiri koma kenako tinayamba kuwasowa anzathu. Tinali tisanayambe kuzolowerana kwambiri ndi abale amumpingo watsopanowu.” a Ngakhale kuti pamakhala mavuto ngati amenewa, kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisangalalabe tikasamukira mumpingo watsopano? Kodi ena angathandize bwanji? Nanga mungatani kuti muzilimbikitsidwa komanso kulimbikitsa ena mumpingo watsopanowu?

MFUNDO 4 ZOMWE ZINGAKUTHANDIZENI

Muzidalira Yehova

1. Muzidalira Yehova. (Sal. 37:5) Mlongo Kazumi wa ku Japan, anasamuka mumpingo umene anakhalamo kwa zaka 20 pamene mwamuna wake anasinthidwa kuti azikagwira ntchito kudera lina. Ndiye kodi iye anatani kuti ‘Yehova amutsogolere panjira yake’? Iye anati: “Mobwerezabwereza ndinkamufotokozera Yehova za mantha amene ndinali nawo, nkhawa zanga komanso kuti ndinkadziona kuti ndili ndekhandekha. Nthawi iliyonse ndikachita zimenezi, iye ankandipatsa mphamvu zimene ndinkafunikira.”

Kodi mungatani kuti muzidalira kwambiri Yehova? Mofanana ndi mbewu imene imafunika madzi ndi zakudya zina za munthaka kuti ikule, chikhulupiriro chathu chimafunikanso zinthu zina kuti chikule. Nicolas yemwe tamutchula kale uja anapeza kuti kuganizira kwambiri za anthu monga Abulahamu, Yesu ndi Paulo, omwe analolera kusiya zinthu zambiri kuti atumikire Mulungu, kunamuthandiza kuti azikhulupirira kwambiri kuti Yehova amuthandiza. Kuphunzira Baibulo nthawi zonse kungakuthandizeni kuti muzolowere zinthu zimene zasintha komanso kuti mupeze zinthu zimene mungalimbikitse nazo ena mumpingo wanu watsopano.

Muzipewa kuyerekezera

2. Muzipewa kuyerekezera. (Mlal. 7:10) Jules atasamuka kuchoka ku Benin kupita ku United States ankafunika kusintha kuti azolowere chikhalidwe china. Iye anati: “Ndinkafunika kufotokozera munthu aliyense yemwe ndakumana naye koyamba chilichonse chokhudza ineyo.” Popeza chikhalidwechi chinali chosiyana ndi zimene anazolowera, anayamba kupewa abale ndi alongo. Koma atawadziwa bwino anasintha mmene ankawaonera. Iye anati: “Tsopano ndikudziwa kuti kulikonse padzikoli anthu ndi ofanana. Iwo amangolankhula kapena kuchita zinthu mosiyana. Kuchita zinthu ndi anthu mogwirizana ndi zimene anazolowera n’kofunika kwambiri.” Choncho muzipewa kuyerekezera mpingo wanu wakale ndi watsopano. Mpainiya wina dzina lake, Anne-Lise, ananena kuti: “Sindinasamuke kuti ndikapeze zofanana ndi zimene ndinasiya, koma kuti ndikaphunzire zatsopano.”

Akulu ayeneranso kusamala kuti asamayerekezere mpingo wawo wakale ndi watsopano. Ngati abale akuchita zinthu m’njira yosiyana mumpingo watsopanowo si nthawi zonse pamene zimakhala kuti akulakwitsa. Ndi nzeru kudziwa bwino mmene zinthu zilili mumpingo watsopanowo musanapereke maganizo anu. (Mlal. 3:​1, 7b) Chitsanzo chanu chabwino chingathandize abale mumpingomo mmalo mowakakamiza kuti azingotsatira maganizo anu.—2 Akor. 1:24.

Muzichita nawo zambiri

3. Muzichita nawo zambiri. (Afil. 1:27) Kusamuka ndi kotopetsa ndipo kumafuna nthawi yambiri. Koma ngati n’kotheka, kuyambira pamene mwangofika, muzisonkhana nawo pamasom’pamaso. Ndipo ngati abale ndi alongo mumpingo watsopanowo samakuonani kapena amangokuonani mwa apo ndi apo, kodi angakuthandizeni bwanji? Lucinda, ndi ana ake aakazi awiri, omwe anasamukira mumzinda waukulu ku South Africa, anati: “Anzanga anandilangiza kuti ndiyenera kumacheza kwambiri ndi abale ndi alongo mumpingo watsopanowu, kumalowa nawo mu utumiki, komanso kumayankha pamisonkhano. Tinauzanso abale kuti akhoza kumagwiritsa ntchito nyumba yathu pochitiramo misonkhano yokonzekera utumiki.”

Kuyesetsa kuchita zinthu zokhudza kulambira “mogwirizana” ndi abale ndi alongo mumpingo wanu watsopano, kudzakuthandizani kuti mupitirize “kukhulupirira uthenga wabwino.” Anne-Lise, amene tamutchula kale uja analimbikitsidwa ndi akulu kuti aziyesetsa kulalikira ndi aliyense mumpingo. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Iye anati: “Ndinazindikira kuti zimenezi zinandithandiza kuti ndizolowere mofulumira.” Komanso kudzipereka pogwira nawo ntchito yokonza pa Nyumba ya Ufumu kungasonyeze kuti tsopano mwayamba kuona kuti umenewu ndi mpingo wanu. Mukamachita nawo kwambiri zinthu limodzi abale ndi alongowo adzayamba kumasuka nanu ndipo mudzayamba kuwaona kuti ndi anthu a m’banja lanu lauzimu.

Muzipeza anzanu atsopano

4. Muzipeza anzanu atsopano. (2 Akor. 6:​11-13) Kuchita chidwi ndi ena kungakuthandizeni kuti mupeze anzanu atsopano. Choncho muzipeza nthawi misonkhano isanayambe kapena itatha yoti muzicheza ndi ena n’cholinga choti muwadziwe bwino. Muziyesetsa kudziwa mayina awo. Kukumbukira mayina a anthu komanso kukhala ochezeka, kungathandize kuti ena azifuna kucheza nanu ndipo izi zingathandize kuti mupeze anzanu ambiri abwino.

M’malo modera nkhawa ndi kuchita zinthu zinazake zapadera n’cholinga choti anthu akukondeni, muzilola kuti abale ndi alongo akudziweni mmene mulili. Muzichita zimene Lucinda ananena. Iye anati: “Panopa tili ndi anzathu abwino ambiri chifukwa chakuti tinayamba ndife kuwaitanira kunyumba kwathu.”

“MUZILANDIRANA”

Ena amachita mantha akalowa m’Nyumba ya Ufumu yodzaza ndi anthu amene sakuwadziwa. Ndiye kodi mungatani kuti muthandize anthu amene angosamukira kumene mumpingo wanu? Mtumwi Paulo ananena kuti: “Muzilandirana. Ngati mmene Khristu anatilandirira.” (Aroma 15:7) Potsanzira Khristu, akulu angathandize anthu amene angosamukira kumene mumpingo wawo kuti azidzimva kuti alandiridwa. (Onani bokosi lakuti “ Kodi Mungatani Kuti Kusamuka Kusakhale Kovuta?”) Komabe, onse mumpingo, kuphatikizapo ana, angathandize anthu amene abwera mumpingo kupeza anzawo atsopano.

Kulandira ena kukuphatikizapo kuwaitana kunyumba kwathu, komanso kuwathandiza pa zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, mlongo wina anapeza nthawi yolowa m’tauni ndi mlongo amene anali atangosamukira kumene mumpingo wawo kuti akamuonetse malo ndiponso kokwerera mabasi. Zimene anachitazo zinamuthandiza mnzakeyo kuti azolowere mwamsanga.

ZIMATIPATSA MWAYI WOKULA MWAUZIMU

Chiwala chikamakula, chimafundula maulendo angapo kuti mapiko amasuke n’kuyamba kuuluka. Mofanana ndi zimenezi, inunso mukasamukira mumpingo watsopano, muyenera kukhala ngati mwafundula popewa zilizonse zimene zingakulepheretseni kutumikira Yehova momasuka. Nicolas ndi Céline ananena kuti: “Kusamuka kumatiphunzitsa zinthu zambiri. Timafunika makhalidwe atsopano kuti tizolowerane ndi anthu komanso malo atsopano.” Jean-Charles, amene tamutchula kumayambiriro uja anafotokoza mmene kusamuka kwathandizira banja lake. Iye anati: “Kusamuka kwathandiza kuti ana athu azichita bwino mumpingo. Patangotha miyezi yochepa, mwana wathu wamkazi anayamba kukamba nkhani pamisonkhano ya mkati mwa mlungu ndipo mwana wathu wamwamuna anakhala wofalitsa wosabatizidwa.”

Bwanji ngati simungathe kusamukira kwina, monga kukatumikira kumene kukufunika olalikira ambiri? Mungachite bwino kutsatira malangizo omwe takambirana munkhaniyi muli mumpingo wanu womwewo. Muzidalira Yehova ndipo muzichita zambiri mumpingo pokonza zoti muzilalikira ndi anthu ena, kupanga mabwenzi atsopano komanso kupitiriza kugwirizana ndi anzanu akale. Mungamathandizenso amene abwera kumene kapena osowa powapatsa zimene akufunikira. Popeza chikondi ndi khalidwe lomwe limadziwikitsa Akhristu oona, kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti mulimbitse ubwenzi wanu ndi Yehova. (Yoh. 13:35) Mungakhale otsimikiza kuti ‘Mulungu amasangalala ndi nsembe zoterozo.’—Aheb. 13:16.

Ngakhale kuti pamakhala zovuta zina, Akhristu ambiri zinthu zimawayendera bwino akasamukira mumpingo wina, ndipo inunso zingakuyendereni bwino. Anne-Lise ananena kuti: “Kusamukira mumpingo wina kunandithandiza kuti ndidziwane ndi anthu ambiri.” Kazumi ananena motsimikiza kuti “ukasamukira mumpingo wina umaona Yehova akukuthandiza m’njira imene sunaiganizirepo.” Jules ananena kuti: “Anzanga amene ndapeza amandithandiza kuti ndisamachitenso chilendo. Panopa ndimaona kuti ndine wamumpingomu, ndipo zidzandivuta kuti ndisamukemo.”

a Mungapeze malangizo othandiza munkhani yakuti “Kulimbana ndi Malingaliro a Kulakalaka Kumudzi Kwanu mu Utumiki wa Mulungu,” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 1994.