Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Kodi Zithunzizi Zikusiyana Pati?

Kodi mungatchule zinthu zitatu zimene zikusiyana pakati pa chithunzi A ndi chithunzi B? Lembani mayankho anu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo malizitsani kujambula zithunzizi pozikongoletsa ndi chekeni.

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 1 Samueli 16:1-3, 6-13.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

4. Kodi chithunzi cholondola n’chiti, A kapena B?

KAMBIRANANI:

Kodi Yehova amaona chiyani mwa munthu? Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamanena kuti ‘Yehova amaona mumtima’?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Yeremiya 17:10.

Kodi maonekedwe a munthu ndi ofunika kwambiri kwa Yehova?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Miyambo 11:22; 31:30; 1 Petulo 3:3, 4.

Kodi ndi makhalidwe ati amene angakuchititseni kuti mukhale wokongola kwa Mulungu?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Luka 10:27; 2 Petulo 1:5-8.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Werengani Agalatiya 5:22, 23. Lembani khalidwe lililonse papepala lakelake. Sankhani munthu mmodzi m’banja mwanu n’kumumata kapepala kamodzi pachipumi. Munthuyo asaone zimene zalembedwa pa kapepalako. Muzimufunsa mafunso osiyanasiyana okhudza khalidwelo n’cholinga choti anene khalidwe limene lili pa kapepalako. Ena onse m’banjamo aziyankha kuti eya wofunsidwayo akayankha molondola kapena ayi akalakwitsa.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 15 DAVIDE

MAFUNSO

A. Kodi Davide ndi Yesu anabadwira mumzinda uti?

B. Ali mnyamata, Davide anali ․․․․․ wolimba mtima yemwe anapha ․․․․․ ndi ․․․․․.

C. Malizitsani mawu a Davide awa: “Ndipo iwe Solomo mwana wanga, dziwa . . . ”

[Tchati]

4026 B.C.E. Kulengedwa kwa Adamu

Anakhala ndi moyo cha m’ma 1000 B.C.E.

1 C.E.

98 C.E. Baibulo linamalizidwa kulembedwa

[Mapu]

Anachoka ku Betelehemu kupita ku Yerusalemu

Betelehemu

Yerusalemu

Anagonjetsa Goliyati m’chigwa cha Ela.—1 Samueli 17:2

Chigwa cha Ela

DAVIDE

ANALI NDANI?

Anali mwana wa Jese komanso anali mfumu yachiwiri ya Isiraeli. Davide anali ndi waluso kwambiri polemba ndakatulo komanso poimba ndipo analemba masalimo oposa 73. Iye modzichepetsa ankatsatira malamulo a Yehova pa moyo wake. (1 Samueli 23:2; 30:8; 2 Samueli 2:1) Yehova anatcha Davide kuti “munthu wapamtima panga.”—Machitidwe 13:22.

MAYANKHO

A. Betelehemu (ku Yudeya).—Yohane 7:42.

B. m’busa, mkango, chimbalangondo.—1 Samueli 17:34, 35; Salimo 78:70, 71.

C. “. . . Mulungu wa bambo wako, um’tumikire ndi mtima wathunthu.”—1 Mbiri 28:9.

Anthu ndi Mayiko

5. Dzina langa ndi Olivia. Ndili ndi zaka 6 ndipo ndimakhala ku Indonesia. Kodi mukudziwa kuti ku Indonesia kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 22,300; 42,800 kapena 63,900?

6. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ineyo ndimakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Indonesia.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Nkhani zina zakuti “Zoti Banja Likambirane” mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.isa4310.com.

● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba 22

MAYANKHO A PATSAMBA 30 NDI 31

1. Pachithunzi china pali mbuzi pamene chinacho pali ng’ombe.

2. Pachithunzi china pali mtsikana pamene chinacho palibe.

3. Pachithunzi china pali kathumba ka chikopa koikamo vinyo pamene chinacho pali nyanga ya mafuta.

4. B.

5. 22,300.

6. D.