Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhondo ya ku Ain Jalut Inasintha Zinthu

Nkhondo ya ku Ain Jalut Inasintha Zinthu

Nkhondo ya ku Ain Jalut Inasintha Zinthu

ASILIKALI a ku Mongolia omwe anali ndi zida zoopsa anachoka m’dziko lawo n’kuyamba kulanda mizinda yosiyanasiyana. Mu February chaka cha 1258, asilikaliwa anagwetsa mpanda wa mzinda wa Baghdad n’kulanda mzindawu. Kwa mlungu umodzi, iwo anapha anthu ambirimbiri ndiponso kuwononga zinthu. Mayiko onse achisilamu anachita mantha kwambiri ndi asilikaliwa. *

Mu January chaka cha 1260, asilikali a ku Mongolia analowera chakumadzulo kwa dzikolo ndipo anagonjetsa mzinda wa Aleppo, m’dziko la Syria. M’mwezi wa March chaka chomwecho, asilikaliwo analanda mzinda wa Damascus. Ndipo pasanapite nthawi, analanda mizinda iwiri ya ku Palesitina, mzinda wa Gaza ndi wa Nablus womwe unali pafupi ndi mzinda wa Sekemu.

Mkulu wa asilikali a ku Mongolia, dzina lake Hülegü, analamula kuti m’tsogoleri wa ku Egypt, Sultan al-Muzaffar Sayf al-Din Qutuz, yemwe anali Msilamu, atule pansi udindo wake ndipo avomere kuti azilamulidwa ndi dziko la Mongolia. Hülegü anaopseza kuti ngati savomereza ndiye kuti dziko lonse la Egypt likhala m’mavuto. Asilikali a ku Egypt analipo 20,000 ndipo chiwerengero chimenechi chinali chochepa kwambiri chifukwa asilikali a ku Mongolia analipo 300,000, zomwe zikutanthauza kuti msilikali m’modzi wa ku Egypt ankafunika kumenyana ndi asilikali 15 a ku Mongolia. Katswiri wina wa mbiri ya Chisilamu, Pulofesa Nazeer Ahmed, anati: “Mayiko onse achisilamu anatsala pang’ono kuwonongedwa.” Kodi Qutuz akanatani pamenepa?

Qutuz Anatsogolera Asilikali a Mtundu wa Mamluk

Qutuz anali wa mtundu wa Mamluk ndipo anthu amtunduwu anachokera ku Turkey. A Mamluk anali akapolo omwe ankagwira ntchito ngati asilikali a olamulira a fuko la Ayyubid, omwe ankakhala mumzinda wa Cairo ku Egypt. Koma m’chaka cha 1250, akapolowa anaukira olamulirawo n’kuyamba kulamulira dziko la Egypt. Kenako Qutuz, yemwenso anali msilikali, analanda boma m’chaka cha 1259 n’kukhala wolamulira wa dziko lonse la Egypt. Iye anali munthu wodziwa kumenya nkhondo ndipo sakanavomera mwachisawawa kuti azilamulidwa ndi dziko la Mongolia. Komabe, zinkaoneka kuti sakanatha kugonjetsa asilikali a ku Mongolia. Koma kenako panayamba kuchitika zinthu zimene zinakhudza dziko lonse.

Akukonzekera kulanda dziko la Egypt, Hülegü analandira uthenga woti Möngke, yemwe anali m’tsogoleri wa dziko la Mongolia, wamwalira. Poona kuti zimenezi zichititsa kuti anthu ayambe kulimbirana udindo, Hülegü anaganiza zobwerera ku Mongolia. Pobwerera anatenga asilikali ambirimbiri n’kusiya asilikali pakati pa 10,000 ndi 20,000 okha. Iye ankaganiza kuti asilikali amenewa angakwanitse kulanda dziko la Egypt. Pamenepa Qutuz anaona kuti tsopano ndi mwayi wake woti agonjetse asilikali a ku Mongolia.

Koma vuto linali lakuti anafunika kulimbana ndi asilikali achikhristu ochokera m’madera a pakati pa dziko la Egypt ndi Mongolia. Asilikaliwa, omwe ankadana ndi Chisilamu, anabwera ku Palesitina kudzalanda malo awo “opatulika.” Qutuz anapempha anthu amenewa kuti amulole kudutsa m’dera lawo komanso kuti azimugulitsa zinthu zofunikira pa nkhondo yake yolimbana ndi asilikali a ku Mongolia. Iwo anagwirizana nazo ndipo anaona kuti Qutuz awathandiza kulimbana ndi asilikali a ku Mongolia, omwenso ankawaona kuti ndi adani.

Atagwirizana zimenezi, nkhondo pakati pa a Mamluk ndi asilikali a ku Mongolia inayambika.

Anamenyana M’dera la Ain Jalut ku Palesitina

Nkhondo ya pakati pa anthu a mtundu wa Mamluk ndi asilikali a ku Mongolia inayambika mu September chaka cha 1260, m’chigwa cha Esdraelon chomwe chili m’dera lotchedwa Ain Jalut. Anthu ena amanena kuti dera la Ain Jalut linali pafupi ndi mzinda wa Megido. *

Katswiri wina wa mbiri yakale, dzina lake Rashid al-Din, ananena kuti pa nkhondoyi a Mamluk anaputsitsa asilikali a ku Mongolia. Qutuz anagawa asilikali ake m’magulu awiri. Asilikali ambiri anawauza kuti abisale m’mapiri a pafupi ndi chigwa cha Megido ndipo analamula asilikali ochepa chabe kuti akapute asilikali a ku Mongolia. Asilikali a ku Mongolia sanadziwe kuti asilikali ena a mtundu wa Mamluk abisala, moti anayamba kuthamangitsa asilikali ochepawo. Kenako Qutuz analamula asilikali omwe anabisala aja kuti atuluke mofulumira n’kuyamba kumenyana ndi adaniwo, moti anawagonjetsa.

Aka kanali koyamba kuti asilikali a ku Mongolia agonje pa nkhondo kuchokera pamene iwo anayamba nkhondo yawo ya zaka 43 yolanda mayiko a kumadzulo kwa dzikolo. Ngakhale kuti chiwerengero cha asilikali amene anamenya nkhondo ya ku Ain Jalut chinali chochepa, anthu amanena kuti nkhondo imeneyi inasintha mbiri ya dziko lonse. Nkhondoyi inathandiza kuti Asilamu asaphedwe onse ndipo inathandizanso kuti anthu asiye kuganiza kuti asilikali a ku Mongolia sangagonjetsedwe ndi wina aliyense. Komanso inathandiza kuti asilikali a mtundu wa Mamluk atengenso madera amene analandidwa.

Zochitika Nkhondo ya ku Ain Jalut Itatha

Asilikali a ku Mongolia anayesanso kubwerera kuderali kangapo konse kukamenyana ndi asilikali a dziko la Syria ndi Palesitina, koma sanayerekeze n’komwe kuopseza dziko la Egypt. Zidzukulu za Hülegü zitasamukira ku Persia, zinalowa Chisilamu ndipo patapita nthawi zinayamba kulimbikitsa chikhalidwe cha Chisilamu. Madera amene ankakhala anayamba kudziwika kuti Persian ilkhanate kapena kuti “madera okhala anthu otsika.”

Patangopita nthawi yochepa Qutuz atagonjetsa asilikali a ku Mongolia, anthu ena anamugalukira n’kumupha. M’modzi mwa anthu amenewa anali Baybars Woyamba, yemwe anali wolamulira woyamba wa ufumu wogwirizana wa Egypt ndi Syria. Anthu ambiri ankaona kuti iye ndi woyenera kulamulira chifukwa ankakhulupirira kuti ndi amene anayambitsa ufumu wa anthu a mtundu wa Mamluk. Kuyambira pa nthawi yomwe iye anayamba kulamulira mpaka pamene ufumuwo unatha mu 1517, zinthu zinkayenda bwino kwambiri pa nkhani ya chuma ndi zina. Ufumuwo unatha patapita zaka 250.

Pa zaka pafupifupi 250 zimenezi, anthu a mtundu wa Mamluk anathamangitsa Akhristu m’dera limene ankati ndi lopatulika lija, analimbikitsa ntchito zamalonda ndi mafakitale, ankalimbikitsa luso losiyanasiyana, ndiponso anamanga zipatala, mizikiti ndi masukulu. Mu ulamuliro wa mafumu a mtundu wa Mamluk, dziko la Egypt linali chimake cha Chisilamu.

Nkhondo ya ku Ain Jalut sinakhudze madera a ku Middle East okha. Nkhondoyi inathandizanso kuti mayiko a azungu ayambe kutukuka. Magazini ina inanena kuti: “Zikanakhala kuti asilikali a ku Mongolia amene Hülegü anawasiya ku Egypt anakwanitsa kulanda dzikolo, ndiye kuti iye pobwerera akanapitiriza kulanda madera ena a kumpoto kwa Africa, mpaka kukafika ku Spain.” (Saudi Aramco World) Popeza kuti pa nthawiyi asilikali a ku Mongolia anali atafika ku Poland, ndiye kuti akanavutitsanso kwambiri ku Ulaya.

Magaziniyi inafunsa kuti: “Kodi zikanakhala kuti zimenezi zinachitika, bwenzi mayiko a azungu atayamba kupita patsogolo pa nkhani ya maphunziro? Kunena zoona, zinthu padzikoli zikanakhala zosiyana kwambiri ndi mmene zilili panopa.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Kuti mudziwe zambiri zokhudza anthu a ku Mongolia komanso nkhondo zimene anamenya ndi madera amene analanda, werengani Galamukani! ya May 2008.

^ ndime 11 Chifukwa chakuti nkhondo zambiri zikuluzikulu zinkachitikira m’dera limeneli, mawu akuti “Megido” anayamba kugwiritsidwa ntchito ponena za nkhondo yodziwika bwino kwambiri ya Aramagedo, yomwe m’Chiheberi amati Har–Magedon. Baibulo likamanena za Aramagedo limatanthauza nkhondo ya “tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”—Chivumbulutso 16:14, 16.

[Mapu patsamba 12]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Damasiko

SIRIYA

Phiri la Tabor

Chigwa cha Esdraelon

Ain Jalut (pafupi ndi Megido)

Nablus (Sekemu)

Yerusalemu

Gaza

EGUPUTO

[Chithunzi patsamba 12]

Dera limene kunali mzinda wa Megido

[Chithunzi patsamba 13]

Asilikali a mtundu wa Mamluk anamenyana ndi asilikali a ku Mongolia mu September m’chaka cha 1260 m’dera la Ain Jalut lomwe lili m’chigwa cha Esdraelon

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

[Chithunzi patsamba 14]

Mabwinja a mzinda wa Sekemu, ndiponso mbali ina ya mzinda wa Nablus