Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chipatso Chokoma Kwambiri cha ku Armenia

Chipatso Chokoma Kwambiri cha ku Armenia

Chipatso Chokoma Kwambiri cha ku Armenia

● Chipatso chili pachithunzichi, chomwe chimafanana kwambiri ndi pichesi, chakhala chikulimidwa kwa zaka zambiri m’mayiko ambiri a ku Asia ndi ku Ulaya. Anthu a ku Ulaya ankakhulupirira kuti chipatsochi chinachokera ku Armenia ndipo pa chifukwa chimenechi, anayamba kuchitchula kuti maapozi a ku Armenia.

Masiku ano ku Armenia amalima mitundu yosiyanasiyana yokwana 50 ya chipatsochi. Chimakhwima kuyambira m’mwezi wa June mpaka wa August. Chipatsochi chimakoma kwambiri chifukwa cha nyengo komanso nthaka yabwino ya ku Armenia, moti anthu ena amanena kuti chipatsochi ndi chokoma kwambiri kuposa zipatso zina zonse padziko lapansi.

Mitundu yomwe imapezeka kwambiri kukula kwake imafanana ndi mapichesi ndipo imaoneka mosiyanasiyana, ina imakhala yagolide pomwe ina imaoneka ngati malalanje. Mitundu ina imakhala ndi khungu ngati la mapichesi, siikhala ndi madzi ambiri ndipo ina imatsekemera pomwe ina imawawasirako. Ena amanena kuti chipatsochi chimakomako ngati mapichesi kapena mapulamu.

Alimi ena anapanga mtundu wina wa chipatsochi womwe umaoneka wakuda koma sufanana kwenikweni ndi mitundu ina yochita kumera yokha.

Mitengo ya chipatsochi imachita maluwa masamba ake asanaphukire ndipo maluwawo, omwe amakhala oyera, amanunkhira bwino kwambiri. Maluwawo amafanana ndi maluwa a mtengo wa pichesi komanso wa mapulamu. Mitengo ya zipatsozi imakula bwino m’nyengo yozizirirako komanso yotentherako chifukwa nyengo imeneyi imathandiza kuti mitengoyi itulutse maluwa komanso kuti ibereke. Zipatsozi zimagwirizana kwambiri ndi nyengo ya ku Armenia.

Chipatsochi chikakhala kuti changothyoledwa kumene chimapatsa thanzi. Mwachitsanzo, chimakhala ndi vitamini C. Koma anthu ambiri amadya chipatsochi chikakhala chouma chifukwa chikakhala chachiwisi sichichedwa kuphulika komanso kuola. Chifukwa cha zimenezi m’mayiko ambiri zipatsozi zimapezeka kwambiri zouma poyerekezera ndi zaziwisi. Komabe ngakhale zoumazo zimakhala ndi zinthu zina zopatsa thanzi komanso zimagwiritsidwa ntchito popanga mowa, jamu ndi juwisi.

Komanso anthu amagwiritsa ntchito mitengo ya zipatsozi popangira zinthu zina zamatabwa zokongola kwambiri. Zina mwa zinthuzi ndi monga chipangizo choimbira cha ku Armenia chotchedwa duduk. M’mashopu ambiri komanso m’misika ya mumzinda wa Yerevan, womwe ndi likulu la dziko la Armenia, mumapezeka zinthu zamatabwa zochokera ku mitengo ya chipatsochi.

Ngati mumakhala m’dziko limene chipatsochi chimapezeka mungachite bwino kuchilawa kuti muone mmene chimakomera.