Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Amachita ku Mumbai Kuti Azidya Chakudya Chotentha Kuntchito

Zimene Amachita ku Mumbai Kuti Azidya Chakudya Chotentha Kuntchito

Zimene Amachita ku Mumbai Kuti Azidya Chakudya Chotentha Kuntchito

TIYEREKEZERE kuti tsiku lililonse mumachoka kunyumba 5 koloko m’mawa kupita kuntchito. Pa nthawi yopuma masana mumadya chakudya chophikidwa kunyumba choikidwa zokometsera zimene inuyo mumakonda. Zimenezi n’zimene zimachitika ku Mumbai, m’dziko la India. Anthu masauzande ambiri amene amagwira ntchito mumzinda umenewu amadzapatsidwa chakudya ndi ma dabbawala. Amenewa ndi anthu amene amanyamula chakudya chotentha kuchokera kunyumba kupita nacho kuntchito. *

Mwayi wa Bizinezi

Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, mumzinda wa Mumbai, womwe pa nthawiyo unkadziwika kuti Bombay, munayamba kuchitika ntchito zambirimbiri zamalonda. Anthu ambiri ochita bizinezi mumzindawu ankayenda mitunda italiitali popita kuntchito. Ena mwa iwo anali nzika za ku Britain ndipo ena anali nzika za ku India komweko. Kayendedwe kanali kovuta ndipo kunali malo odyera ochepa kwambiri. Anthu ambiri ankakonda kudya chakudya chophikidwa kunyumba, choncho anthu ogwira ntchito m’nyumba za anthu ankapititsira mabwana awo chakudya kuntchito. Munthu wina ataona mwayi wa bizinezi umenewu, anayamba kulemba ntchito achinyamata ochokera kumudzi omwe ankasowa ntchito kuti azinyamula chakudya kuchokera kunyumba kupititsa kumaofesi. M’kupita kwa nthawi, imeneyi inakhala bizinezi yotentha.

Ngakhale kuti masiku ano kuli malo odyera ambiri, anthu ambiri amakondabe chakudya chophikidwa kunyumba chifukwa sichiboola m’thumba komanso n’chimene chimawakomera. Ndiponso chifukwa cha matenda, anthu ambiri amasala zakudya zina. Anthu enanso amasala zakudya chifukwa cha chipembedzo chawo. Mwachitsanzo, anthu ena sadya anyezi ndipo ena sadya adyo. Koma zakudya zambiri za kulesitilanti amaikamo zinthu ngati zimenezi. Choncho pofuna kupewa mavuto amenewa, anthu ambiri a m’maofesi amakonda zakudya zochokera kunyumba kwawo.

Njira Yodalirika Kwambiri

Ngakhale kuti papita zaka zambiri, njira yosavuta yoperekera zakudya kumaofesi imeneyi sinasinthe kwenikweni, kungoti panopa bizineziyo yakula kwambiri. Masiku ano, pali amuna oposa 5,000, komanso akazi ochulukirapo ndithu, amene amakapereka chakudya chamasana kwa anthu oposa 200,000, tsiku lililonse. Chakudyachi chimachokera m’madera apafupi ndi kumene anthu operekawo amakhala. Anthuwo amapita nyumba ndi nyumba kukatenga chakudyacho n’kupita nacho kumaofesi omwe ali paliponse mumzinda wa Mumbai, womwe uli ndi anthu oposa 20 miliyoni. Munthu mmodzi amatha kuyenda ulendo woposa makilomita 60 ndipo amanyamula pa wilibala makontena osanjikizana okwana 30 kapena 40. Anthu ena amanyamula makontenawa pa njinga kapena kukwera nawo sitima. Kaya ayenda nawo bwanji, amakapereka makontena oyenerera kwa munthu woyenerera pa nthawi yoyenereranso. Ndipotu anthuwa salakwitsa wambawamba. Akuti mwina pa makontena 6 miliyoni, amatha kungolakwitsapo imodzi. Kodi zimatheka bwanji kuti azipereka chakudya mwadongosolo chonchi?

Mu 1956, ma dabbawala analembetsa kuboma kuti akhale bungwe lothandiza anthu lokhala ndi akuluakulu oliyendetsa. Gulu la antchito angapo, pamodzi ndi bwana wawo, limagwira ntchito ngati kabungwe kodzilamulira kokha. Komabe, magulu onsewa ali ndi masheya m’bungweli ndipo akuti zimenezi n’zimene zimachititsa kuti bizinezi yawo iziyenda bwino kwambiri. Ndipotu anthu ogwira ntchito m’bungweli sananyanyalepo ntchito pa zaka zoposa 100 zimene bungweli lakhalapo.

Ma dabbawala amakhala ndi khadi lowadziwikitsa ndipo anthu amawazindikira msanga chifukwa cha yunifolomu yawo. Iwo amavala shati yoyera, thalauza lotaya ndiponso chipewa choyera. Akapanda kuvala chipewa, akachedwa kapena kujomba popanda chifukwa chomveka, kapenanso akawagwira akumwa mowa nthawi ya ntchito, amawalipitsa ndalama.

Zimene Zimachitika Tsiku Lililonse

Nthawi ikamakwana 8:30 m’mawa, winawake kunyumba kwa kasitomala, mwina mkazi wa kasitomalayo, amakhala ataphika chakudya chamasana n’kuchiika m’makontena otchedwa dabba. Ma dabba amakhala ndi makontena angapo omwe amawaika mosanjikizana ndipo amakhala ndi chogwirira chawaya. Dabbawala amatolera makontena ambirimbiri m’dera limodzi n’kuwakweza pa njinga kapena pa wilibala. Akatero amapita nawo msangamsanga kumalo okwerera sitima kumene amakakumana ndi ma dabbawala ena a m’gulu lake. Kumeneko amaika makontenawo m’magulumagulu mogwirizana ndi kumene akupita, ngati mmene amachitira anthu ogwira ntchito kumalo otumizira makalata.

Makontena onse opita kwa munthu mmodzi amawalemba mawu enaake, manambala ndiponso kuwapenta ndi penti ya mtundu winawake kuti asasokoneze ndi makontena ena. Amalembaponso kumene chakudyacho chikuchokera, malo apafupi okwerera sitima, malo otsikira sitima, dzina la nyumba imene muli ofesi ya kasitomala ndi malo enieni amene ofesiyo ili. Makontena opita dera limodzi amasonkhanitsidwa pamodzi n’kuwaika m’mabokosi ataliatali amatabwa omwe amatha kunyamula makontena osanjikizana okwana 48. Sitima ikafika, amakweza makontenawo m’chipinda chapadera chapafupi ndi woyendetsa sitima. Akafika pasiteshoni yaikulu, amatsitsa makontenawo n’kuwaikanso m’magulu mogwirizana ndi kumene akupita. Kenako amawakwezanso sitima zina zopita kudera limene makontenawo akupita. Akafika kumeneko, amawaikanso m’magulumagulu n’kukawapereka kwa makasitomala pa njinga kapena pa wilibala.

Njira zonyamulira makontena zimenezi n’zachangu komanso zotsika mtengo. Ndiponso, ma dabbawala sachedwa chifukwa cha kuchuluka kwa magalimoto mumsewu. Iwo amatha kudutsa ndi njinga yawo mphepete mwamsewu kapena pakati pa magalimoto. Choncho nthawi ikamakwana 12:30 masana, amakhala atapereka chakudya ku ofesi iliyonse. Kenako pakati pa 1:15 ndi 2 koloko masana, pambuyo poti nawonso adya, amapita kukatolera makontena aja n’kukawabweza kunyumba kwa makasitomala awo. Munthu wina wa kunyumbako amawatsuka kuti adzawagwiritsenso ntchito tsiku lotsatira. Kuyambira pachiyambi mpaka pamapeto, ntchito yonseyi imachitika mwachangu ndipo imayenda bwino kwambiri chifukwa aliyense amagwira ntchito yake modzipereka.

Ntchito Yooneka Ngati Yonyozeka Koma Yotamandika Kwambiri

Anthu ambiri achita chidwi ndi mmene ma dabbawala amagwirira ntchito. Mabungwe ena abizinezi aunika njira imene anthuwa amagwiritsa ntchito popereka zakudya, n’cholinga choti atengere zimenezi pochita bizinezi zawo. Ena afika ngakhale popanga mafilimu ofotokoza za ma dabbawala. Magazini ina yotchuka (Forbes Global Magazine) inawapatsa satifiketi yapamwamba kwambiri chifukwa chakuti amagwira ntchito yawo mwadongosolo kwambiri. Ma dabbawala atchulidwapo m’buku limene amalemba za anthu amene achita zodabwitsa padziko lapansi (The Guinness Book of World Records), ndiponso m’kafukufuku wa yunivesite ya Harvard ku United States. Iwo ayenderedwaponso ndi akuluakulu a boma, kuphatikizapo munthu wina wa m’banja lachifumu ku Britain. Iye anagoma kwambiri ndi ntchito ya ma dabbawala moti anawaitana ena mwa iwo kuti akakhale nawo pa ukwati wake ku England.

Masiku ano, ma dabbawala amagwiritsa ntchito makompyuta ndi mafoni am’manja polandira maoda komanso posunga mayina a makasitomala. Komabe njira yawo yoperekera zakudya sinasinthe. Choncho, nthawi ya chakudya chamasana ikamakwana, anthu ambiri ogwira ntchito m’maofesi ku Mumbai sakayikira ngakhale pang’ono kuti chakudya chawo chotentha chophikidwa kunyumba chatsala pang’ono kufika, ndipo chifika pa nthawi yake.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mawu akuti Dabba amatanthauza “kontena.” Wala ndi munthu amene amagwira ntchito yonyamula zakudya. Kalembedwe ka mawuwa kamasiyanasiyana.

[Chithunzi patsamba 11]

Akulongedza ma “dabba” m’sitima pa ulendo wokapereka zakudya

[Chithunzi patsamba 11]

“Dabba” imakhala ndi makontena angapo amene amawasanjikiza kuti asamavute kunyamula

[Chithunzi patsamba 12]

Anthu ambiri a bizinezi atengera njira yabwino kwambiri ya ma “dabbawala” yoperekera katundu