Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

JW LANGUAGE

Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri Okhudza JW Language (Pa Zipangizo za iOS)

Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri Okhudza JW Language (Pa Zipangizo za iOS)

Zinenero zina monga Chithai, zimakhala ndi mawu ena ovuta kuwalemba pogwiritsa ntchito afabeti yawo. Choncho nthawi zina pulogalamu ya pa zipangizo za Apple sionetsa zilembo zake molondola.

 

Pulogalamu Yophunzirira Chinenero ya pa JW imagwira ntchito pa zipangizo izi:

  • Matabuleti a iPad 2 ndi ena a posachedwapa (okhala ndi pulogalamu ya iOS 7.0 kapena mapulogalamu ena a posachedwapa)

  • Matabuleti a iPad Mini (okhala ndi pulogalamu ya iOS 7.0 kapena mapulogalamu ena a posachedwapa)

  • Mafoni a iPhone 4 kapena ena a posachedwapa (okhala ndi pulogalamu ya iOS 7.0 kapena mapulogalamu ena a posachedwapa)

  • Ma iPod Touch (a m’gulu la nambala 5) (okhala ndi pulogalamu ya iOS 7.0 kapena mapulogalamu ena a posachedwapa)

Panopa tilibe maganizo odzakhala ndi zinthu zothandiza pogwiritsa ntchito zipangizo zotsatirazi:

  • Matabuleti a iPad 1

  • Mafoni a iPhone 3GS komanso ena a m’mbuyomo

 

Munthu wina amene amadziwa bwino kugwiritsa ntchito Pulogalamu Yophunzirira Chinenero ya pa JW akhoza kukuthandizani. Ngati palibe, lembani fomu yokuthandizani kupeza mayankho ndipo kenako tumizani fomuyo.