Pitani ku nkhani yake

Kodi Kukhala “Msamariya Wachifundo” Kumatanthauza Chiyani?

Kodi Kukhala “Msamariya Wachifundo” Kumatanthauza Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

Mawu oti “Msamariya Wachifundo” amagwiritsidwa ntchito ponena za munthu yemwe amathandiza anthu amene akuvutika. Mawuwa anachokera pa nkhani kapena kuti fanizo limene Yesu anafotokoza. Iye anafotokoza fanizoli pofuna kusonyeza kuti munthu wabwino ndi amene mwachifundo amathandiza anthu ena, posatengera mtundu kapena kumene munthuyo akuchokera.

Zimene zili munkhaniyi

 Kodi fanizo la “Msamariya Wachifundo” limanena za chiyani?

Mwachidule, nkhani imene Yesu anafotokozayi imanena za munthu wa Chiyuda yemwe ankayenda kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko. Ali m’njira, anakumana ndi achifwamba amene anamumenya kwambiri n’kumusiya atatsala pang’ono kufa.

Wansembe wa Chiyuda anangomudutsa. Kenakonso mtsogoleri wina wachipembedzo cha Chiyuda anachitanso zomwezo. Ngakhale kuti munthuyo anali wamtundu wawo, koma palibe anaima kuti amuthandize.

Pomalizira pake, kunabwera munthu wamtundu wina. Iye anali wa Chisamariya. (Luka 10:33; 17:16-18) Atagwidwa chifundo, Msamariyayo anamanga mabala a munthuyo. Kenako anapita naye kunyumba ya alendo kumene anamusamalira usiku wonse. Mawa lake, Msamariyayo analipira mwini nyumba ya alendoyo kuti apitirize kusamalira munthu wovulalayo ndipo anamuuza kuti ngati angawononge ndalama zina posamalira munthuyo, adzamubwezera ndalama zowonjezerazo.—Luka 10:30-35.

 N’chifukwa chiyani Yesu ananena fanizoli?

Yesu anafotokoza nkhaniyi kwa munthu amene ankaganiza kuti ayenera kungokonda anthu amtundu wake komanso achipembedzo chake basi. Yesu ankafuna kuphunzitsa munthuyo mfundo yofunika kwambiri yakuti azikondanso anthu ena, osati Ayuda anzake okha. (Luka 10:36, 37) Nkhaniyi inalembedwa m’Baibulo kuti ithandize anthu onse amene akufuna kusangalatsa Mulungu.—2 Timoteyo 3:16, 17.

 Kodi tikuphunzirapo chiyani pa fanizoli?

Nkhaniyi imasonyeza kuti munthu wabwino ndi amene amachitira ena chifundo kudzera m’zochita zake. Iye amathandiza munthu amene akuvutika, posatengera chikhalidwe, mtundu komanso komwe munthuyo akuchokera. Munthu wabwino amachitira anthu ena zimene iyeyo angafune kuti enawo amuchitire.—Mateyu 7:12.

 Kodi Asamariya anali ndani?

Asamariya ankakhala m’dera lakumpoto kwa Yudeya. Ena mwa iwo anali ana omwe anabadwa Ayuda atakwatirana ndi anthu amitundu ina.

Pofika m’nthawi ya atumwi, Asamariya anali atakhazikitsa chipembedzo chawochawo. Iwo ankangokhulupirira mabuku 5 oyambirira a Malemba a Chiheberi koma sankakhulupirira mabuku enawo.

Ayuda ambiri a m’nthawi ya Yesu ankadana ndi Asamariya ndipo ankawapewa. (Yohane 4:9) Ayuda ena ankagwiritsa ntchito mawu oti “Msamariya” pofuna kunyoza munthu.—Yohane 8:48.

 Kodi nkhani ya “Msamariya Wachifundo” inachitikadi?

Malemba sanena ngati fanizo la Msamariya linachokera pa nkhani yomwe inachitikadi. Koma Yesu pofotokoza fanizoli, anatchula za miyambo komanso malo odziwika n’cholinga chothandiza anthu kumvetsa mfundo zimene ankafotokoza.

Zinthu zambiri zimene anatchula m’fanizoli zinalipodi pa nthawiyo. Mwachitsanzo:

  • Msewu umene unkachokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko, womwe unali wamtunda wa makilomita oposa 20, unali wotsetsereka. N’chifukwa chake nkhaniyi m’Mabaibulo ena imanena kuti anthu opita ku Yeriko pamsewuwu ‘ankatsika kuchokera ku Yerusalemu.’—Luka 10:30, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

  • Nthawi zambiri ansembe ndi Alevi amene ankakhala ku Yeriko ankagwiritsa ntchito msewu umenewu popita ku Yerusalemu.

  • Achifwamba ankakonda kubisala m’mbali mwa msewuwu n’kumadikirira anthu odutsa, makamaka amene ankayenda okha.