Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Mungatani Kuti Mukhale Bwenzi Labwino?

Kodi Mungatani Kuti Mukhale Bwenzi Labwino?

PA DECEMBER 25, 2010, mayi wina wazaka 42 wa ku Britain analemba uthenga pa webusaiti ina wonena kuti akufuna kudzipha. Uthenga wakewu unasonyeza zoti ankafuna kuti anthu ena amuthandize. Ngakhale kuti mayiyu anali ndi anzake ambirimbiri amene ankacheza nawo pa Intaneti, palibe amene anamuthandiza. Mayiyu anadziphadi atamwa mankhwala ambiri, ndipo apolisi anamupeza atafa tsiku lotsatira.

Masiku ano zinthu monga mafoni, makompyuta kapena Intaneti, zikupangitsa kuti anthu asamavutike kupeza ocheza nawo ambiri. Iwo amangofunika kusankha dzina la munthu n’kuliika pa mndandanda wa anthu ocheza nawo. Akaona kuti akufuna kusiya kucheza ndi winawake, amangochotsa dzina la munthuyo pa mndandanda uja. Koma nkhani ya mayi wa ku Britain, ikusonyeza kuti kupeza mabwenzi enieni si kophweka. Ndipotu, zotsatira za kafukufuku wina amene anachitika posachedwapa, zinasonyeza kuti ndi anthu ochepa okha amene ali ndi anzawo enieni. Izi zili choncho ngakhale kuti pali njira zambiri zopezera anthu ocheza nawo.

Anthu ambiri amaona kuti kukhala ndi mnzako wabwino n’kofunika ndipo mwina inunso mumaona choncho. Koma mwinanso mumaona zoti pamafunika zambiri kuti munthu akhale ndi anzake abwino, osati kungosankha dzina la munthu pa Intaneti. Kodi inuyo mumafuna kuti mnzanu akhale wotani? Nanga mungatani kuti mukhale bwenzi labwino? Ndipo kodi anthu omwe ndi mabwenzi angatani kuti ubwenzi wawo usathe?

Tiyeni tikambirane mfundo 4 zomwe zingakuthandizeni kupeza mabwenzi abwino. Tikambirananso malangizo a m’Baibulo amene angakuthandizeni kukhala ndi makhalidwe amene angapangitse anthu ena kukopeka nanu kuti mukhale mnzawo.

 1. Muzisonyeza Kuti Mumakonda Mnzanuyo Komanso Mumamuganizira

Kuti ubwenzi ukhale wolimba pamafunika kudzipereka. Izi zikusonyeza kuti bwenzi labwino limakuderani nkhawa ndipo limakukondani. Komatu dziwani kuti inunso mumafunika kuchita zimenezi. Kuti izi zitheke, pamafunika khama komanso kudzipereka. Komabe n’zimene zingathandize kuti ubwenzi wanu ukhale wolimba. Ndiye dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimagwiritsa ntchito nthawi komanso zinthu zanga mosanyinyirika pothandiza mnzanga?’ Kumbukirani kuti ngati mukufuna kukhala ndi mnzanu wabwino, muyenera kuyamba inuyo kukhala bwenzi labwino.

ZIMENE ANTHU AMAFUNA KUTI ANZAWO AZICHITA

Irene: “Kuti munthu ukhale ndi munda wamaluwa wokongola, umafunika kupeza nthawi yousamalira. Pamafunikanso kuchita chimodzimodzi ukafuna kukhala ndi bwenzi labwino. Choyamba, uyenera kuyesetsa kukhala munthu wabwino. Uyeneranso kusonyeza mnzakoyo kuti umamukonda komanso kumuganizira.Uzikhalanso wokonzeka kugwiritsa ntchito nthawi yako, mnzakoyo akafuna kuti umuthandize.”

Luis Alfonso: “Anthu ambiri m’dzikoli ndi odzikonda ndipo saganizira kwenikweni za ena. Choncho zimakhala zolimbikitsa kwambiri ukakhala ndi mnzako amene amakuthandiza popanda kufuna kuti apezepo kenakake.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo. Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.” (Luka 6:31, 38) Pamenepatu Yesu anatilimbikitsa kuti tizipewa mtima wodzikonda koma tikhale anthu opatsa. Zimenezi zimathandiza kuti ubwenzi ukhale wolimba. Mukamadzipereka kuthandiza anzanu, osati n’cholinga chofuna kupezapo kenakake, anzanuwonso adzayamba kukukondani.

2. Muzilankhulana Momasuka

Kuti ubwenzi ukhale wolimba, pamafunika kulankhulana pafupipafupi. Choncho muzikambirana nkhani zosiyanasiyana zomwe nonse mumakonda komanso zimene zimakudetsani nkhawa. Mnzanuyo akamalankhula, muzimvetsera ndipo muzilemekeza maganizo ake. Muzimuyamikira komanso kumulimbikitsa pakafunika kutero. Nthawi zina mungafunike kum’patsa mnzanuyo malangizo, mwinanso kumudzudzula kumene. Komatu kuchita zimenezi si kophweka. Komabe bwenzi labwino limalimba mtima n’kuuza mnzakeyo zinthu zolakwika zimene wachita ndipo limam’patsa malangizo mwaulemu.

ZIMENE ANTHU AMAFUNA KUTI ANZAWO AZICHITA

Juan: “Mnzako wabwino ndi amene amafotokoza maganizo ake momasuka koma sakwiya akaona kuti sukugwirizana nazo.”

Eunice: “Anzanga omwe ndimakonda kwambiri ndi amene amapeza nthawi yocheza nane komanso kundimvetsera, makamaka ndikakhala pa mavuto.”

Silvina: “Anzako abwino amakuuza zoona zokhazokha, ngakhale atadziwa kuti zimenezo zikukhumudwitsa. Amachita zimenezi chifukwa chokukonda.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula, wosafulumira kukwiya.” (Yakobo 1:19) Anthu amene ndi mabwenzi abwino, nthawi zonse amamvetserana. Si bwino kumangolankhula ifeyo nthawi zonse chifukwa zimenezi zimasonyeza kuti timaona zoti maganizo athu ndi ofunika kuposa a mnzathuyo. Choncho ngati mnzanu akufuna kukuuzani zakukhosi komanso zimene zikumudetsa nkhawa, muzimvetsera mwatcheru. Koma musamakwiye akakuuzani chilungamo. Lemba la Miyambo 27:6 limati: “Zilonda zovulazidwa ndi munthu wokukonda zimakhala zokhulupirika.”

 3. Muzidziwa Kuti Mnzanuyo Angalakwitse Zinthu Zina

Tikamacheza kwambiri ndi mnzathu, m’pamenenso timaona kwambiri zinthu zimene amalakwitsa. Tizikumbukira kuti mofanana ndi ifeyo, mnzathuyo nayenso si wangwiro. Choncho tisamayembekezere kuti azichita chilichonse mosalakwitsa. M’malomwake, tiziyamikira makhalidwe abwino amene ali nawo ndipo akalakwitsa zinthu zina tizingomukhululukira.

ZIMENE ANTHU AMAFUNA KUTI ANZAWO AZICHITA

Samuel: “Nthawi zambiri timafuna kuti anzathu azichita zinthu zimene ifeyo sitingakwanitse. Koma tikamakumbukira kuti nafenso timalakwitsa ndipo timafuna kuti ena atikhululukire, tidzayesetsa kukhala okhululuka.”

Daniel: “Tizivomereza mfundo yoti anzathu angalakwitse zinthu zina. Choncho tikasemphana maganizo, ndi bwino kuthetsa nkhaniyo mwamsanga n’kuiiwala.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kodi mnzanu akakulakwirani mumakhala wokonzeka kumukhululukira?​—Akolose 3:13, 14

“Ngati wina sapunthwa pa mawu, ameneyo ndi munthu wangwiro, ndipo akhoza kulamuliranso thupi lake lonse.” (Yakobo 3:2) Kumvetsa mfundo imeneyi kungatithandize kuti tisamafulumire kukhumudwa anzathu akalakwitsa zinazake. Zimenezi zingathandize kuti tisamaganizire kwambiri zinthu zing’onozing’ono zomwe anzathu atilakwira. Baibulo limati: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. . . . Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.”Akolose 3:13, 14.

 4. Muzicheza ndi Anthu Osiyanasiyana

N’zoona kuti tiyenera kusankha mosamala anthu amene timacheza nawo. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti tiyenera kumangocheza ndi anthu a msinkhu wathu kapena amene analeredwa ngati mmene ifeyo tinaleredwera. Kucheza ndi anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana komanso a misinkhu ndi zikhalidwe zosiyanasiyana, kungapangitse kuti tizisangalala.

ZIMENE ANTHU AMAFUNA KUTI ANZAWO AZICHITA

Unai: “Kumangocheza ndi anthu a msinkhu wanu komanso amene amakonda zomwe inuyo mumakonda, kuli ngati kumangovala zovala za mtundu umodzi wokha basi. Ngakhale zitakhala kuti mumakonda kwambiri mtundu umenewo, kupita kwa nthawi ukhoza kuyamba kukunyasani.”

Funke: “Kucheza ndi anthu osiyanasiyana kwandithandiza kuti ndizichita zinthu ngati munthu wamkulu. Ndaphunzira zambiri kwa anthu amenewa ndipo zandithandiza kuti ndizitha kukhala bwino ndi anthu. Izi zimachititsa kuti anzanga azisangalala kucheza nane.”

Kodi mumacheza ndi anthu osiyanasiyana?​—2 Akorinto 6:13

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Ndikulankhula nanu ngati ana anga, inunso futukulani mtima wanu.” (2 Akorinto 6:13) Lembali likusonyeza kuti si bwino kumangocheza ndi anthu amodzimodzi nthawi zonse. Kucheza ndi anthu osiyanasiyana kungachititse kuti tiphunzire zambiri kwa anthuwo komanso kuti azitikonda.