Pitani ku nkhani yake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Zimene Makolo Ayenera Kudziwa Zokhudza Kutumiza Mwana Kumalo Osamalira Ana Masana

Zimene Makolo Ayenera Kudziwa Zokhudza Kutumiza Mwana Kumalo Osamalira Ana Masana

 Makolo ena amene ali pa ntchito amatumiza ana awo omwe sanayambe sukulu kumalo osamalirako ana masana. Malowa amachita zinthu ngati sukulu. Kodi ndi bwino kutumiza mwana wanu kumalo oterewa?

 Mafunso ofunika kuwaganizira

 Ngati ndingamakasiye mwana wanga kumalo osamalira ana, kodi zingasokoneze ubwenzi wanga ndi iye? Zimenezi zikhoza kuchitika. Mwana akakhala wamng’ono, ubongo wake umakula mwamsanga kwambiri m’njira zimene zimakhudza ubwenzi wake ndi anthu ena. Muyenera kuyesetsa kukhala limodzi ndi mwana wanu kwambiri pa nthawi yofunika imeneyi.—Deuteronomo 6:6, 7.

  •    Makolo omwe akuganiza zotumiza mwana wawo kumalo osamalira ana masana, akuyenera kuganizira zimene achite kuti apitirize kukhala pa ubwenzi wabwino ndi mwana wawoyo.

 Kodi kutumiza mwana wanu kumalo osamalira ana kuchepetsa mphamvu zanu pa mwanayo? Zimenezi zikhoza kuchitika. Buku lakuti Hold On to Your Kids linati: “Ana omwe sanayambe sukulu akamathera nthawi yambiri ali ndi ana anzawo, m’pamenenso amatengera kwambiri zochita za anzawowo.”

  •    Makolo omwe akuganiza zotumiza mwana wawo kumalo osamalira ana masana, akufunika kuganizira ngati iwowo ndi amene akhalebe ndi mphamvu zambiri pa moyo wa mwana wawo.

 Kodi kutumiza mwana wanu kumalo osamalira ana masana kudzathandiza mwanayo akadzayamba sukulu? Anthu ena amanena kuti inde. Ena amanena kuti kutumiza mwana kumalo osamalira ana kumathandiza mwanayo pang’ono kapena sikumuthandiza n’komwe. Kaya zoona ndi ziti, katswiri wa zamaganizo a ana dzina lake Penelope Leach anati: “Musamaganize kuti zimene mwana amaphunzira kusukulu ndi zimene zimamuthandiza kwambiri pamoyo wake. Musamaganizenso kuti zingakhale zothandiza ngati mwana wanu atayamba sukulu mofulumira kwambiri. Ngati mungamaganize choncho, mukhoza kuyamba kuchepetsa kufunika kwa zinthu zimene mwakhala mukumuphunzitsa mwana wanu kuyambira pamene anabadwa.”

  •   Makolo omwe akuganiza zotumiza mwana wawo kumalo osamalira ana afunika kuganizira ngati kuchita zimenezi n’kothandiza kapenanso ngati kuli kofunika n’komwe.

 Kodi n’zotheka kuti inuyo, mwamuna kapena mkazi wanu azisamalira mwana m’malo mogwira ntchito? Nthawi zina, makolo onse amagwira ntchito n’cholinga chofuna kuti azikhalabe moyo wapamwamba. Kodi kuchita zimenezi kumathandizadi?

  •   Makolo omwe akuganiza zotumiza mwana wawo kumalo osamalira ana ayenera kuona ngati angamakhale moyo wosalira zambiri kuti kholo limodzi lizikhala pakhomo.

 Muyenera kusankha zotumiza mwana wanu kumalo osamalira ana pambuyo poti mwaganizira bwinobwino ubwino ndi kuipa kochita zimenezi. Pambuyo poganizira zimenezi, bwanji ngati mukuona kuti kutumiza mwana wanu kumalo osamalira ana kungakuthandizeni?

 Zimene mungachite

 Baibulo limanena kuti “wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” (Miyambo 14:15) Muli ndi mfundo imeneyi m’maganizo mwanu, ganizirani mosamala musanasankhe malo oti mutumize mwana wanu.

 Dziwani zomwe mungathe kusankha

  •   Makolo ena amasankha kuti mwana wawo azikasamalidwa kunyumba kwa munthu komwe kuli wosamalira ana mmodzi kapena angapo komanso ana ochepa.

  •   Makolo ena amasankha zoti wachibale wawo yemwe akukhala naye limodzi ndi amene azisamalira mwana wawo.

 Njira zonsezi zili ndi ubwino komanso mavuto ake. Mungachite bwino kufunsa makolo ena omwe anagwiritsapo njira inayake yosamalirira mwana wawo. Baibulo limanena kuti: “Anthu amene amakhala pamodzi n’kumakambirana amakhala ndi nzeru.”—Miyambo 13:10.

 Koma bwanji ngati mwasankha kutumiza mwana wanu kumalo osamalira ana masana? Ngati ndi choncho . . .

 Dziwani zokhudza malowo

  •   Kodi malowo ali ndi zinthu zofunika mogwirizana ndi malamulo? Kodi malowo ali ndi mapepala otani owayenereza kusamalira ana, nanga ali ndi mbiri yotani?

  •   Kodi malowo ndi aukhondo komanso otetezeka?

  •   Kodi ana amachita zotani pamalowo? a

 Dziwani anthu omwe amasamalira ana

  •  Kodi anaphunzira chiyani? Zimenezi zingaphatikizepo ngati anaphunzira zokhudza kuphunzitsa ana aang’ono, kupereka chithandizo choyambirira ngati munthu wavulala, komanso kuthandiza munthu kuti ayambirenso kupuma.

  •   Kodi n’zotheka kuti mufufuze ngati amene azisamalira mwana wanu ali ndi mbiri yoti anapalamulapo mlandu m’mbuyomu?

  •   Kodi omwe amasamalira ana amasiyasiya ntchito? Ngati zimenezi zimachitika, ndiye kuti mwana wanu akufunika kuzolowera kuti nthawi zonse azisamaliridwa ndi anthu osiyanasiyana.

  •   Kodi wosamalira mwana mmodzi amasamalira ana angati? Ngati munthu mmodzi amasamalira ana ambiri, zikutanthauza kuti mwana wanu azilandira chisamaliro chochepa. Ngakhale zili choncho, kuchuluka kwa chisamaliro chimene mwana wanu angafunike kukudalira zaka zake komanso zimene angathe kuchita yekha.

  •   Kodi osamalira ana ndi okonzeka kulankhula nanu pa nkhawa zimene muli nazo, kapenanso zimene iwo ali nazo?

a Mwachitsanzo, kodi ana amangokhalira kuonera TV kapena pamalowo pali zochita zosiyanasiyana zomwe zimafuna kuti ana aziganiza komanso kugwiritsa ntchito mphamvu?