Miyambo 14:1-35

  • Ngati munthu mtima ukumupweteka amadziwa yekha (10)

  • Njira imene imaoneka ngati yabwino ikhoza kubweretsa imfa (12)

  • Munthu amene sadziwa zambiri amakhulupirira mawu alionse (15)

  • Munthu wolemera amakhala ndi anzake ambiri (20)

  • Mtima wodekha umapangitsa kuti thupi likhale lathanzi (30)

14  Mkazi amene alidi wanzeru amamanga nyumba yake,+Koma wopusa amaigwetsa ndi manja ake.   Munthu amene amachita zabwino amaopa Yehova,Koma amene amachita zinthu mwachinyengo* amanyoza Mulungu.   Mawu odzikuza a munthu wopusa ali ngati chikwapu cholangira munthu,Koma milomo ya anthu anzeru idzawateteza.   Ngati palibe ngʼombe, chodyeramo chimakhala choyera.Koma zokolola zimachuluka ngati pali ngʼombe yamphongo yamphamvu.   Mboni yokhulupirika sinama,Koma mboni yabodza imalankhula zabodza zokhazokha.+   Munthu wonyoza amafunafuna nzeru koma sazipeza,Koma munthu womvetsa zinthu amaphunzira zinthu mosavuta.+   Usayandikire munthu wopusa,Chifukwa suphunzira chilichonse mʼmawu otuluka pakamwa pake.+   Nzeru zimathandiza munthu wochenjera kuzindikira njira imene akuyenda,Koma anthu opusa amapusitsika* ndi kupusa kwawo komwe.+   Anthu opusa akapalamula mlandu amangoseka,*+Koma anthu owongoka mtima amakhala ofunitsitsa kugwirizananso. 10  Ngati munthu mtima ukumupweteka amadziwa yekha,Ndipo munthu wina sangamvetse mmene mnzake akusangalalira mumtima mwake. 11  Nyumba ya munthu woipa idzawonongedwa,+Koma tenti ya munthu wowongoka mtima idzakhazikika.* 12  Pali njira imene imaoneka ngati yabwino kwa munthu,+Koma pamapeto pake imabweretsa imfa.+ 13  Ngakhale pamene munthu akuseka, mtima wake ukhoza kumamupweteka.Ndipo kusangalala kungathere mʼchisoni. 14  Munthu wa mtima wosakhulupirika adzakumana ndi zotsatira za zochita zake,+Koma munthu wabwino amapeza mphoto chifukwa cha zochita zake.+ 15  Munthu amene sadziwa zambiri amakhulupirira mawu alionse,Koma wochenjera amaganizira zotsatira za zimene akufuna kuchita.+ 16  Munthu wanzeru amachita zinthu mosamala ndipo amapewa zoipa,Koma wopusa amachita zinthu mosasamala* ndipo amakhala wodzidalira. 17  Munthu amene amakwiya msanga amachita zinthu zopusa,+Koma munthu amene amaganiza bwino amadedwa. 18  Anthu osadziwa zambiri adzakhala opusa,Koma kwa ochenjera, kudziwa zinthu kudzakhala ngati chisoti chachifumu.+ 19  Anthu oipa adzagwadira anthu abwino,Ndipo oipa adzagwada pamageti a anthu olungama. 20  Munthu wosauka amadedwa ngakhale ndi anzake,+Koma munthu wolemera amakhala ndi anzake ambiri.+ 21  Munthu amene amanyoza mnzake ndiye kuti akuchimwa,Koma wosangalala ndi munthu amene amakomera mtima anthu onyozeka.+ 22  Anthu okonza chiwembu amasochera, Koma amene ali ndi mtima wofunitsitsa kuchita zabwino amawachitira zinthu mokhulupirika komanso kuwasonyeza chikondi chokhulupirika.+ 23  Kugwira ntchito iliyonse mwakhama kumapindulitsa,Koma kungolankhula chabe kumasaukitsa.+ 24  Chisoti chaulemu cha anthu anzeru ndi chuma chawo.Koma kupusa kumapangitsa kuti anthu opusa apitirizebe kukhala opusa.+ 25  Mboni yokhulupirika imapulumutsa miyoyo ya anthu,Koma mboni yabodza imalankhula zabodza zokhazokha. 26  Munthu woopa Yehova amamukhulupirira pa chilichonse,+Ndipo ana a munthu ameneyu adzapeza malo othawirako.+ 27  Kuopa Yehova kuli ngati kasupe wa moyo,Chifukwa kumateteza moyo kumisampha ya imfa. 28  Kuchuluka kwa anthu kumabweretsa ulemerero kwa mfumu,+Koma wolamulira amene alibe anthu oti aziwalamulira ulamuliro wake umatha. 29  Munthu amene sakwiya msanga ndi wozindikira zinthu kwambiri,+Koma wosaugwira mtima amasonyeza uchitsiru wake.+ 30  Mtima wodekha umapangitsa kuti thupi likhale lathanzi,Koma nsanje imawoletsa mafupa.+ 31  Amene amabera munthu wosauka mwachinyengo amanyoza amene anamupanga,+Koma amene amakomera mtima munthu wosauka amalemekeza amene anamupanga.+ 32  Woipa adzagwetsedwa ndi kuipa kwakeko,Koma kukhulupirika kwa munthu wolungama kudzakhala malo ake othawirako.+ 33  Munthu womvetsa zinthu salankhula modzitama kuti ali ndi nzeru,+Koma munthu wopusa, nthawi zonse amalengeza zimene akudziwa. 34  Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu,+Koma tchimo limachititsa manyazi mitundu ya anthu. 35  Mfumu imasangalala ndi wantchito amene amachita zinthu mozindikira,+Koma imakwiya ndi wantchito wochita zinthu zochititsa manyazi.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “zopotoka.”
Mabaibulo ena amati, “anthu opusa amapusitsa anzawo.”
Kapena kuti, “Anthu opusa akapalamula mlandu zoti akonze zinthu zimangowaseketsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “idzalemera.”
Kapena kuti, “amakhala wokwiya.”