Pitani ku nkhani yake

JUNE 24, 2019
ECUADOR

Zokhudza Msonkhano wa Mayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Guayaquil, Ecuador

Zokhudza Msonkhano wa Mayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Guayaquil, Ecuador
  • Masiku: 14 mpaka 16 June, 2019

  • Malo: Estadio Monumental Banco Pichincha ku Guayaquil, Ecuador

  • Zinenero: Chinenero Chamanja cha ku Ecuador, Chingelezi, Chisipanishi

  • Chiwerengero cha Osonkhana: 53,055

  • Chiwerengero cha Obatizidwa: 702

  • Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 5,300

  • Nthambi Zoitanidwa: Argentina, Belgium, Bolivia, Central America, Colombia, Cuba, Kazakhstan, Korea, Moldova, Myanmar, Poland, Spain, United States

  • Zina Zomwe Zinachitika: Sitediyamu ya Estadio Monumental Banco Pichincha ndi ya timu ya mpira ya Barcelona ndipo pulezidenti wa timuyi, José Francisco Cevallos anati: “Sitinakumanepo ndi vuto lililonse pamisonkhano yanu ya zaka za m’mbuyomu komanso wa chaka chino. Umenewu ndi umboni wosonyeza kuti muli ndi khalidwe labwino komanso mumachita zinthu mwadongosolo pamisonkhano yanu yonse. Sizophweka kuyendetsa zinthu chonchi, koma nthawi zonse mumachita bwino ndiponso kukonzekera mokwanira misonkhano yanu yonse. Ndinu anthu abwino. Mumasonyeza khalidwe labwino, mumaphunzitsidwa bwino kwambiri, ndinu aulemu komanso adongosolo. Tikulimbikitsa akuluakulu onse a mizinda ndi mayiko kuti azilola a Mboni za Yehova kuchita misonkhano yawo.”

 

Alendo akujambulitsa pa nthawi yoona malo ku Beteli ya ku Ecuador

Abale ndi alongo a ku Ecuador ali muutumiki limodzi ndi alendo ochokera ku mayiko ena

Alendo ochokera kumayiko ena akuimba nyimbo pa tsiku loyamba la msonkhano

Ena mwa abale ndi alongo atsopano 702 akubatizidwa

Alendo akulemba notsi pamene nkhani zikukambidwa

Alendo akupanga chizindikiro chosonyeza chikondi chomwe anthu a ku Korea amapanga

M’bale Kenneth Cook wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Loweruka la msonkhano

Alendo omwe ali muutumiki wa nthawi zonse wapadera akubayibitsa anthu pa tsiku lomaliza la msonkhanowu

Abale ndi alongo a ku Ecuador akusangalatsa alendo madzulo pa nthawi yapadera