AUGUST 15, 2019
POLAND
Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Warsaw, Poland
Masiku: 9 mpaka 11 August 2019
Malo: Municipal Stadium of Legia Warsaw ndiponso Torwar Hall, Warsaw, Poland
Zinenero: Chingelezi, Chipolishi
Chiwerengero cha Osonkhana: 32,069
Chiwerengero cha Obatizidwa: 190
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 6,892
Nthambi Zoitanidwa: Central Europe, Chile, Ecuador, Finland, France, Georgia, Hungary, Japan, Korea, Moldova, Romania, Ukraine, ndi United States
Zina Zomwe Zinachitika: A Kamil Kaźmierkiewicz, omwe ndi mkulu wa Four Points by Sheraton Warsaw Mokotów (yomwe ndi imodzi mwa mahotela amene alendo ankakhala), analemba kuti: “Zinali zosavuta kugwira nanu ntchito. Ndikufunitsitsa tikanakhala ndi alendo ambiri omwe ndi okoma mtima komanso a maganizo abwino. N’zoonekeratu kuti mumakondana kwambiri komanso mumagwirizana kwambiri. . . . Ndakutairani kamtengo chifukwa choyendetsa bwino dongosolo lokhudza msonkhanowu.”
A Kamil Lubański, omwe ndi eniake a kampani ya KL Team yomwe inapatsidwa kontilakiti yonyamula alendo pa mabasi, nawonso anati: “Kungoyambira tsiku loyamba kugwira ntchito ndi a Mboni za Yehova, ndinaoneratu kuti zikhala zosangalatsa kwambiri kugwira nawo ntchito limodzi. Iwo amachita zinthu mwadongosolo komanso mwaukatswiri. Msonkhanowu anaukonzekera bwino kwambiri ngakhale kuti unali waukulu. Kampani yathu yakhala ikugwira ntchito ndi makasitomala ambiri odziwika bwino kuphatikizaponso boma, ndipo takhala tikuyendetsa dongosolo la zochitika zosiyanasiyana za m’dziko muno komanso m’mayiko a ku Europe. Koma n’zosowa kupeza kasitomala amene wakonzekera bwino komanso wochita zinthu mwadongosolo. Kunena mwachidule, madalaivala athu komanso anthu ena ogwira ntchito ku kampani yathu akunena zabwino zokhazokha zimene zinachitika pamene ankagwira ntchito ndi a Mboni za Yehova. Tikukhulupirira kuti m’tsogolo muno tidzagwiranso ntchito limodzi.”
Alendo akulandiridwa pabwalo la ndege
Abale ndi alongo akufika pamalo a msonkhano Lachisanu m’mawa
Chithunzi chosonyeza Municipal Stadium of Legia Warsaw, amodzi mwa malo amene msonkhanowu unachitikira
M’bale Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Lachisanu
Anthu atatu akubatizidwa Loweruka
Abale ndi alongo akumvetsera msonkhano mwachidwi
Alendo akujambulitsa panja pa sitediyamu atavala zovala zachikhalidwe cha kwawo
Alendo omwe ali muutumiki wanthawi zonse ali m’bwalo la sitediyamu ndipo akuimba nyimbo yomaliza pamodzi ndi anthu onse pa tsiku Lamlungu
Alongo achitsikana akuimbira nyimbo alendo pa zochitika zamadzulo
Abale ndi alongo akuvina gule wachikhalidwe cha ku Poland pa zochitika zamadzulo