Pitani ku nkhani yake

Banja la Mboni likuchita nawo misonkhano polumikiza vidiyo pazipangizo zamakono. Kwanthawi yoyamba, anthu ambiri chaka chino achita mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye mwanjira imeneyi.

APRIL 3, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Mwambo Wapadera Kwambiri Wokumbukira Imfa ya Khristu

Mipingo Yambiri Idzasonkhana Polumikiza Vidiyo pa Zipangizo Zamakono Chifukwa cha Mliri Umene Wavuta Padziko Lonse

Mwambo Wapadera Kwambiri Wokumbukira Imfa ya Khristu

Amboni za Yehova mamiliyoni ambiri komanso anthu ena adzasonkhana Lachiwiri pa 7 April, 2020 kuti achite mwambo wofunika kwambiri. Umenewu ndi Mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Komabe chifukwa cha mliri wa COVID-19, mwambo wachaka chino ukhala wosiyanako ndi mmene takhala tikuchitira m’mbuyomu. Anthu ambiri padziko lonse adzasonkhana polumikiza vidiyo pa zipangizo zawo zamakono.

Akuluakulu aboma m’mayiko ambiri aletsa kuti anthu ambiri asasonkhane pamalo amodzi chifukwa cha mliri wa kolonavairasi. Chifukwa cha zimenezi, mipingo yambiri padziko lonse ikumalumikizana pa zipangizo zamakono kuti achite misonkhano ya mlungu ndi mlungu. Mipingo imeneyi idzagwiritsanso ntchito njira yomweyo pochita Chikumbutso. Komanso pulogalamu yonseyi idzaikidwa pa jw.org kuti anthu ena onse adzathe kuonera.

Chaka chatha, anthu oposa 20 miliyoni anasonkhana kuti achite mwambo umenewu. Chaka chino tikuyembekezeranso kuti anthu mamiliyoni ambiri adzapezeka nawo pa Chikumbutso pochita kulumikiza vidiyo pa zipangizo zamakono, pa telefoni kapena adzaonera pulogalamu yonse pa jw.org.

Mliri wa COVID-19 ukupitirizabe kufalikira padziko lonse. Kuti abale ndi alongo athu atetezeke, tikufunika kupitirizabe kutsatira mosamala kwambiri malangizo onse amene tikulandira mpaka mliriwu utadutsa. Komabe, timadalira kwambiri kuti Yehova atithandiza. N’chifukwa chake ndife otsimikiza kutsatira lamulo la Yesu lakuti, “Muzichita zimenezi pondikumbukira.”​—Luka 22:19.