Pitani ku nkhani yake

Phunziro la Baibulo Limodzi Linakhala Maphunziro Ambiri

Phunziro la Baibulo Limodzi Linakhala Maphunziro Ambiri

 Marta, yemwe ndi wa Mboni za Yehova ku Guatemala, akuphunzira chilankhulo cha Chikekichi n’cholinga choti aziuza anthu olankhula chilankhulochi uthenga wa m’Baibulo. Tsiku lina iye anaona bambo wina akuchokera kuchipatala. Chifukwa cha mmene ankaonekera, Marta anaganiza kuti bamboyo anali wa m’mudzi wina wa anthu amtundu wa Kekichi kumapiri kumene a Mboni za Yehova salalikira kawirikawiri. Iye anayandikira bamboyo n’kumulankhula mawu ochepa amene ankadziwa m’Chikekichi.

 Marta anamufunsa ngati angakonde kuphunzira Baibulo. Iye anavomera mosangalala koma anauza Marta kuti alibe ndalama zolipirira phunzirolo. Marta anamuuza kuti a Mboni za Yehova amaphunzira Baibulo ndi anthu kwaulere. Anamuuzanso kuti akhoza kuphunzira naye pafoni ndipo banja lake lonse lingakhalepo. Bamboyo anavomera kuphunzira. Popeza bamboyo amalankhulanso komanso kuwerenga Chisipanishi, Marta anamupatsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la Chisipanishi. Anamupatsanso buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? m’Chikekichi. Mlungu wotsatira, bamboyo, mkazi wake ndi ana awo awiri anayamba kuphunzira Baibulo ndi Marta pafoni. Iwo ankaphunzira kawiri pa mlungu. Marta anati: “Popeza sindinkalankhula bwino Chikekichi, tinkaphunzira m’Chisipanishi ndipo bamboyo ankamasulira zimene tinkanena m’Chikekichi kuti mkazi wake azimvetsa. Koma ana awo ankamva Chisipanishi.”

 Bamboyu anali m’busa kutchalitchi kwake. Choncho anayamba kuphunzitsa anthu mutchalitchicho zimene ankaphunzira pa phunziro lake la Baibulo. Anthuwo ankasangalala ndi zimene ankawaphunzitsazo moti anamufunsa kumene iye anaphunzira mfundozo. Bamboyo atawauza za phunziro lake la Baibulo, pang’ono ndi pang’ono anayamba kupezeka pa phunzirolo. Pasanapite nthawi, anthu pafupifupi 15 ankasonkhana mlungu uliwonse kuti aphunzire ndi Marta pafoni. Kenako anayamba kuika maikofoni pafupi ndi foniyo kuti aliyense azimva bwinobwino.

 Marta atauza akulu mumpingo wake za phunziro la Baibuloli, mmodzi wa iwo anapita kumudzi kumene anthuwo ankakhala. Iye anawaitanira kunkhani imene woyang’anira dera * akambe kumudzi kumene ankayenera kuyenda pagalimoto kwa ola limodzi kenako n’kuyenda wapansi kwa maola awiri kuti akafike. Anthuwo anavomera kuti apite ndipo 17 mwa iwo anapezeka pankhaniyo.

 Patapita milungu ingapo, woyang’anira dera ndi a Mboni ena anapita kukaona anthuwo ndipo anakhalako masiku 4. Tsiku lililonse m’mawa ankaonera mavidiyo a nkhani za m’Baibulo m’Chikekichi pa jw.org komanso kuphunzira kabuku kakuti Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano? Masana ankaonera zinthu zina pa JW Broadcasting. Woyang’anira dera anakonzanso kuti aliyense akhale ndi munthu woti aziphunzira naye payekha.

 Pa masiku 4 amenewo, a Mboniwo ankalalikiranso m’midzi ya Chikekichi yapafupi ndipo ankaitanira anthu kumsonkhano wapadera. Pamsonkhanowo, abale anauza anthu 47 omwe anapezekapo kuti nawonso angakhale ndi phunziro la Baibulo. Mabanja 11 anavomera kuphunzira.

 Patapita miyezi ingapo, akulu anakonza kuti pamapeto pa mlungu uliwonse azipanga misonkhano kumudzi woyamba uja. Panopa, anthu pafupifupi 40 amapezeka pamisonkhanoyi. Ndipo pamene abale anachita mwambo wokumbukira imfa ya Yesu kumudziwo, anthu 91 anapezeka.

 Poganizira zimene zachitikazi, Marta anati: “Ndikuthokoza Yehova. Nthawi zina ndimaona kuti sindingachite zambiri. Koma Mulungu angatigwiritse ntchito pothandiza ena. Iye ankadziwa zimene zinali m’mitima ya anthu akumidziwo ndipo anawakokera kwa anthu ake. Yehova amawakonda kwambiri.”

^ Woyang’anira dera ndi wa Mboni za Yehova amene amayendera mipingo yam’dera lake, yomwe imakhala pafupifupi 20.