Pitani ku nkhani yake

Sukulu ya Giliyadi Yakwanitsa Zaka 70

Sukulu ya Giliyadi Yakwanitsa Zaka 70

Pa February 1, 1943, kalasi yoyamba ya sukulu yapadera kwambiri inayamba kumpoto kwa dera la New York. Pofika pano, anthu oposa 8,000 ochokera m’madera onse a dziko lapansili, amaliza maphunziro awo kusukuluyi, yomwe masiku ano imatchedwa Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo.

Pamwamba: Khomo lakutsogolo la Sukulu ya Giliyadi, ku South Lansing, New York. M’munsi: Mphunzitsi wa sukulu ya Giliyadi akulankhula ndi ophunzira a m’kalasi ya nambala 31 ya Giliyadi

Munthu wina yemwe wamaliza maphunziro ake chaposachedwapa kusukulu ya Giliyadi, dzina lake Jonathan, ananena kuti: “Zimene taphunzira kusukuluyi n’zochokera m’Baibulo ndipo zitithandiza kuti tiziphunzitsa Mawu a Mulungu mogwira mtima kulikonse kumene tingapite komanso kwa anthu a chikhalidwe chilichonse.” Mkazi wa a Jonathan, dzina lake Marnie, anawonjezera kuti: “Kusiyana ndi mmene zinalili m’mbuyomu, panopa ndikufunitsitsa kwambiri kuthandiza anthu kuti azindikire zoti munthu umakhala wosangalala kwambiri ngati ukuchita zimene Mulungu wathu amafuna. Sindikukayikira ngakhale pang’ono kuti anthu omwe tingawathandize kuti adziwe Yehova angakhale ndi moyo wosangalala kwambiri.”

Sukulu ya Giliyadi ndi yaulere ndipo kalasi iliyonse imachitika kwa miyezi 5. Zimene anthu amaphunzira kusukuluyi n’zochokera m’Baibulo. Komanso ophunzirawo amaphunzitsidwa kuti aziona zoti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri. Cholinga cha maphunziro a kusukuluyi n’chakuti ophunzira amene amaliza maphunziro awo azikalimbikitsa ndi kuthandiza mipingo ya anthu a Mulungu kuti akhale ndi makhalidwe amene angawathandize kupirira mavuto alionse amene angakumane nawo. Pa nthawi ya sukuluyi, ophunzirawo amakambirana mfundo za m’Malemba zimene zingawathandize kuti ubwenzi wawo ndi Yehova Mulungu ukhale wolimba kwambiri.

Pamwamba: 1958, M’bale Albert Schroeder akuphunzitsa ophunzira a ku Giliyadi pogwiritsa ntchito chithunzi choyerekezera cha chihema. M’munsi: 1968, M’bale Ulysses Glass akuphunzitsa ophunzira a ku Giliyadi a m’kalasi nambala 46

Kusukulu ya Giliyadi kumapita anthu okwatirana omwe ali kale mu utumiki wanthawi zonse. Akamaliza maphunziro kusukuluyi, amabwerera kukapitiriza utumiki umene ankachita asanapite kusukuluyi ndipo nthawi zina amatumizidwa kumayiko ena. Enanso amatumizidwa kukatumikira m’maofesi a nthambi a Mboni za Yehova ndipo maofesiwa alipo oposa 90 padziko lonse. Koma ambiri mwa ophunzirawo amatumizidwa m’madera amene muli anthu ambiri kuti azikathandiza mokwanira pa ntchito yolakira.

Sukulu ya Giliyadi itangoyamba kumene inkachitikira ku Kingdom Farm, ku South Lansing m’dera la New York. Koma mu 1961, sukuluyi anaisamutsira kulikulu la Mboni za Yehova la padziko lonse lomwe lili ku Brooklyn, ku New York komweko. Kenako mu 1988 sukuluyi anaisamutsira kufamu ya Watchtower, ku Wallkill m’dera lomwelo la New York. M’chaka cha 1995, sukuluyi anaisamutsanso kupita kudera limene ili mpaka pano, komwe ndi ku Likulu la Maphunziro la Watchtower, ku Patterson m’dera lomwelo la New York. Ophunzira a sukuluyi, a m’kalasi ya nambala 134 anamaliza maphunziro awo mu March 2013.

Pamwamba: 2003, Ophunzira a m’kalasi nambala 116 ya Giliyadi ali m’kalasi. M’munsi: 2011, Ophunzira akuwerenga mulaibulale ya ku Giliyadi

Kwa zaka 70 tsopano, anthu amene anamaliza maphunziro awo Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo akhala akugwira ntchito yolalikira za Yehova mwakhama komanso mokhulupirika kwambiri.