Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Manuel Reino Berengui/DeFodi Images via Getty Images

KHALANI MASO

Kodi Mpira wa World Cup Ungachititsedi Anthu Kukhala Ogwirizana?​—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Mpira wa World Cup Ungachititsedi Anthu Kukhala Ogwirizana?​—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Pafupifupi anthu 5 biliyoni akuyembekezera kuonera masewera a FIFA World Cup omwe adzayambe pa 20 November mpaka pa 18 December 2022. Ambiri akuona kuti zochitika za mpira ngati zimenezi zingathe kuchita zambiri kuposa kungogwirizanitsa anthu pamene akuonera masewerawa.

  •   A Nelson Mandela, omwe anali pulezidenti wakale wa ku South Africa, ananena kuti: “Mpira uli ndi mphamvu yosintha dziko. Uli ndi mphamvu yolimbikitsa anthu. Komanso uli ndi mphamvu yogwirizanitsa anthu m’njira yapadera.”

  •   A Gianni Infantino, omwe ndi pulezidenti wa FIFA, a ananena kuti: “Mpira . . . umagwirizanitsa anthu chifukwa chakuti umawapangitsa kumva kuti ali ndi chiyembekezo, umawapangitsa kusangalala, umawachititsa kumva kuti amakonda anthu ena komanso kuti ali ndi chinachake chofanana.”

 Kodi mpira wa World Cup kapena masewera a mpira alionse angakwanitse zolinga zimenezi? Kodi pali chiyembekezo chilichonse cha mtendere ndi mgwirizano?

Kodi ungagwirizanitsedi anthu?

 Mpira wa World Cup wa chaka chino, wapangitsa kuti anthu aziganizira zambiri osati mpira wokha. Mpirawu wachititsa anthu kuti azitsutsana pa nkhani zokhudza moyo wa anthu komanso ndale zomwe zikukhudza ufulu wa anthu, kusankhana mitundu komanso kusankhana pa nkhani za chuma.

 Ngakhale zili choncho, anthu ambiri amasangalala kuonera zochitika za mpira wa mayiko ngati mmene ulili wa World Cup. Komabe, ngakhale zoterezi zitamachitika, sizingapangitse anthu kugwirizana mpaka kalekale. M’malomwake, nthawi zambiri zimapangitsa anthu kuti azichita zinthu mogawikana ndipo zimenezi ndi zomwe Baibulo linaneneratu kuti zidzakhala chizindikiro chakuti tikukhala m’nthawi yomwe imatchedwa “masiku otsiriza.”​—2 Timoteyo 3:1-5.

Chiyembekezo chenicheni cha mgwirizano wa padziko lonse

 Baibulo limatipatsa chiyembekezo chenicheni cha mgwirizano wa padziko lonse lapansi. Limalonjeza kuti anthu onse padzikoli adzakhala ogwirizana pansi pa boma la kumwamba lotchedwa “Ufumu wa Mulungu.”​—Luka 4:43; Mateyu 6:10.

 Mfumu ya Ufumu umenewo, Yesu Khristu, adzaonetsetsa kuti padziko lonse lapansi pali mtendere. Baibulo limati:

  •   “Wolungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendere wochuluka.”​—Salimo 72:7.

  •   “Adzalanditsa wosauka amene akufuula popempha thandizo . . . Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa.”​—Salimo 72:12, 14.

 Ngakhale masiku ano, zomwe Yesu anaphunzitsa zathandiza kale anthu mamiliyoni kuti akhale ogwirizana m’mayiko 239. Iwo akwanitsa kusiya kudana ndi anthu ena. Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yokhala ndi mitu yosiyanasiyana munkhani yakuti “Kodi N’zotheka Kuthetsa Chidani?.”

a Fédération Internationale de Football Association, bungwe la padziko lonse loyang’anira masewera a mpira (wa miyendo).