Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI PALI AMENE ANGAKHAZIKITSE BOMA LOPANDA CHINYENGO?

Ufumu wa Mulungu Ndi Boma Lopanda Chinyengo

Ufumu wa Mulungu Ndi Boma Lopanda Chinyengo

mkulu wa mu ofesi yowerengera ndalama m’dziko la Nicaragua, ananena kuti zachinyengo sizingathe m’boma. Ananena kuti izi zili choncho chifukwa choti “akuluakulu a boma nawonso ndi nzika za dziko. Ngati nzika za dziko zimachita zachinyengo, ndiye kuti nawonso sangasiye kuchita chinyengo.”

Apa n’zoonekeratu kuti ngati anthu a m’dziko linalake amachita zachinyengo, boma lililonse lomwe lingakhazikitsidwe m’dzikomo lizichitanso zachinyengo. Zimenezi zikusonyeza kuti anthu sangakhazikitse boma lomwe lingathetseretu zachinyengo. Koma Baibulo limanena kuti Mulungu adzabweretsa boma loterolo. Boma limeneli ndi Ufumu wa Mulungu, umene Yesu anauza otsatira ake kuti azipemphera kuti ubwere.—Mateyu 6:9, 10.

Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba lomwe lidzalamulire dziko lapansi. Bomali lidzalowa m’malo mwa maboma onse omwe alipowa. (Salimo 2:8, 9; Chivumbulutso 16:14; 19:19-21) Ufumu wa Mulungu udzathetsa zachinyengo zonse, monga katangale komanso ziphuphu. Tiyeni tikambirane mfundo 6 zimene zikutsimikizira kuti zimenezi zidzachitikadi.

1. MPHAMVU

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO: Ndalama zomwe maboma amagwiritsa ntchito zimakhala za misonkho imene nzika zawo zimapereka. Choncho zimakhala zosavuta kuti akuluakulu a boma aziba ndalamazi. Enanso amalandira ziphuphu kuchokera kwa anthu n’kuwatsitsira misonkho komanso ndalama zomwe amalipira kuboma. Zimenezi zimapangitsa kuti boma lisamapeze ndalama zambiri. Zikatere limakweza misonkho ndipo izi zimachititsa kuti anthu azichita chinyengo pofuna kuzemba misonkho. Pamapeto pake amene amavutika kwambiri ndi anthu omwe amachita zinthu mwachilungamo.

ZIMENE UFUMU WA MULUNGU UDZACHITE: Ufumu wa Mulungu umathandizidwa ndi Yehova, * yemwe ndi Mulungu Wamphamvuyonse. (Chivumbulutso 11:15) Ufumuwu suzidzadalira ndalama za misonkho za nzika zake. Aliyense adzakhala ndi zinthu zokwanira. Zili choncho chifukwa Mulungu ali ndi “mphamvu zambiri zochitira zinthu,” ndi wopanda chinyengo komanso ndi woolowa manja.—Yesaya 40:26; Salimo 145:16.

2. WOLAMULIRA

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO: Susan Rose-Ackerman, yemwe tamutchula m’nkhani yoyamba ija, ananenanso kuti ziphuphu sizingathe “pokhapokha titachotsa zimene zimayambitsa ziphuphuzo.” Anthu amasiya kudalira boma ngati likungolimbikira kuthetsa ziphuphu pakati pa apolisi ndi a kasitomu, n’kumalekerera khalidweli pakati pa akuluakulu a boma. Ngakhale wolamulira atakhala wabwino chotani, amalephera kuchita zinthu zina chifukwa nayenso si wangwiro. Baibulo limati: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa.”—Mlaliki 7:20.

Yesu anakana kulandira chiphuphu ngakhale kuti zimenezi zikanachititsa kuti apeze zinthu zambiri

ZIMENE UFUMU WA MULUNGU UDZACHITE: Yesu Khristu, yemwe Mulungu wamusankha kukhala wolamulira wa Ufumu wake, ndi wosiyana ndi anthu ndipo sangachite choipa chilichonse. Mwachitsanzo, pa nthawi ina, Satana ankafuna kuti Yesu achite ziphuphu. Anamuuza kuti amupatsa “maufumu onse a padziko ndi ulemerero wawo” ngati atangogwada n’kumuweramira kamodzi kokha. Koma Yesu anakana kuchita zimenezi ngakhale kuti zikanachititsa kuti apeze zinthu zambiri. (Mateyu 4:8-10; Yohane 14:30) Komanso Yesu anakana kumwa vinyo wosakaniza ndi ndulu pomwe ankazunzidwa, ngakhale kuti kuchita zimenezi kukanachititsa kuti asamve kupweteka kwambiri. Anadziwa kuti kumwa vinyoyo kukanapangitsa kuti asamaganize bwino. (Mateyu 27:34) Yesu atafa, Mulungu anamuukitsa ndipo zimene wakhala akuchita zikusonyeza kuti ndi woyenera kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.—Afilipi 2:8-11.

3. BOMA LAKE

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO: Mayiko ambiri amachita zisankho pafupipafupi n’cholinga choti achotse olamulira achinyengo. Koma vuto ndi loti pa nthawi ya kampeni ndi ya zisankho pamachitika zachinyengo zambiri, ngakhale m’mayiko olemera. Komanso nthawi zina akuluakulu andale amapereka ndalama ndi zinthu zina kwa otsatira awo kuti achitire kampeni. Zimenezi zimapangitsa kuti otsatira awowo asankhidwe, ngakhale atakhala kuti ndi anthu achinyengo.

Woweruza milandu wina wa khoti lalikulu la ku United States, dzina lake John Paul Stevens, ananena kuti, “zimenezi zimapangitsa kuti zinthu zisamayende bwino m’boma komanso kuti anthu asamalikhulupirire.” Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri padziko lonse amaona kuti anthu andale ndi amene amachita chinyengo kwambiri kuposa onse.

ZIMENE UFUMU WA MULUNGU UDZACHITE: Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira, sikudzakhalanso kuchita kampeni kapena kubera mavoti, chifukwa udzakhalapo mpaka kalekale. (Danieli 7:13, 14) Popeza wolamulira wake anasankhidwa ndi Mulungu, anthu sadzamuchotsa pampando, kapena kumuvotera kuti apitirize kulamulira. Chifukwa choti Ufumuwo udzalamulira kwamuyaya, mavuto amene amakhalapo chifukwa cha kusinthasintha kwa boma sadzakhalapo.

4. MALAMULO

Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba lomwe lidzalamulire dziko lapansi

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO: Anthu amaganiza kuti kukhazikitsa malamulo atsopano kungathandize kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino. Koma akatswiri anapeza kuti nthawi zambiri kuchuluka kwa malamulo kumangopangitsa kuti chinyengo chichuluke. Komanso malamulo okhazikitsidwa n’cholinga chofuna kuthetsa katangale, amawonongetsa ndalama zambiri, koma phindu lake limakhala lochepa.

ZIMENE UFUMU WA MULUNGU UDZACHITE: Malamulo a Ufumu wa Mulungu ndi apamwamba kwambiri kuposa malamulo a maboma a anthu. Mwachitsanzo, m’malo molemba mndandanda wa zoyenera ndi zosayenera kuchita, Yesu anangonena zomwe zingatithandize kuti tizichita zabwino. Iye anati: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.” (Mateyu 7:12) Ndipo mosiyana ndi malamulo a anthu, malamulo a Ufumu wa Mulungu amathandiza anthu kuchita zinthu zabwino komanso kupewa mtima wadyera. Yesu anati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mateyu 22:39) N’zoona kuti ndi Mulungu yekha amene angaonetsetse kuti malamulo oterewa akutsatiridwa, chifukwa amaona mumtima mwa munthu.—1 Samueli 16:7.

5. MTIMA WADYERA NDI WODZIKONDA

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO: Dyera komanso kudzikonda ndi zimene zimapangitsa kuti anthu azichita zachinyengo. Anthu ambiri, kuphatikizapo akuluakulu a boma, ali ndi makhalidwe amenewa. Chimene chinachititsa kuti nyumba ya mumzinda wa Seoul yomwe taitchula m’nkhani yapita ija igwe, n’choti akuluakulu a boma analandira ziphuphu kuchokera ku kampani yomwe inamanga nyumbayi. Kampaniyo inkadziwa kuti kuchita zimenezi sikuwonongetsa ndalama zambiri, poyerekeza ndi zomwe akanawononga akanagwiritsa ntchito zipangizo zoyenera komanso kutsatira malamulo a kamangidwe ka nyumba zoterezi.

Choncho kuti ziphuphu zithe, anthu afunika kuphunzitsidwa kuti asiye mtima wadyera komanso wodzikonda. Koma maboma a anthu sangakwanitse ndipo saganiza n’komwe zochita zimenezi.

ZIMENE UFUMU WA MULUNGU UDZACHITE: Ufumu wa Mulungu ungathe kuthetsa ziphuphu. Ungachite zimenezi pophunzitsa anthu kuti asiye dyera komanso kudzikonda. * Zimenezi zingathandize kuti asinthe n’kuyamba kukhutira ndi zomwe ali nazo komanso kuti azichita zinthu moganizira ena.—Aefeso 4:23; Afilipi 2:4; 1 Timoteyo 6:6.

6. NZIKA ZAKE

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO: Ngakhale zitakhala kuti akuluakulu a boma sachita zachinyengo komanso anthu aphunzitsidwa makhalidwe abwino, anthu ena akhoza kumachitabe ziphuphu komanso zinthu zina zachinyengo. Akatswiri amanena kuti zimenezi ndi zomwe zimachititsa kuti maboma a anthu azilephera kuthetsa ziphuphu. Zimene angakwanitse, ndi kuchepetsa ziphuphu kapena mavuto amene amayamba chifukwa cha ziphuphuzo.

ZIMENE UFUMU WA MULUNGU UDZACHITE: Nthambi ya bungwe la United Nations yolimbana ndi ziphuphu inati: “Kuti mayiko akwanitse kuthetsa ziphuphu ayenera kuphunzitsa anthu awo kukhala okhulupirika komanso oona mtima. Ayeneranso kuwaphunzitsa kuti azidziwa zoti m’dziko mukamachitika zachinyengo, limavutika ndi dziko lomwelo.” Ngakhale kuti zimenezi zingaoneke ngati n’zosatheka, Ufumu wa Mulungu ukuthandiza anthu kuti akhale ndi makhalidwe amenewa. Ndipotu munthu aliyense amene akufuna kudzakhala mu Ufumuwu ayenera kukhala ndi makhalidwewa. Baibulo limanena kuti anthu “aumbombo” komanso “abodza” sadzakhala nzika za Ufumu wa Mulungu.—1 Akorinto 6:9-11; Chivumbulutso 21:8.

N’zotheka kuphunzitsa anthu kuti asiye makhalidwewa. Mwachitsanzo m’nthawi ya atumwi, munthu wina dzina lake Simoni, ankafuna kupereka chiphuphu kuti atumwi amupatse mphamvu ya mzimu woyera. Koma atumwi anakana ndipo anamuuza kuti: “Lapa choipa chakochi.” Simoni atadziwa kulakwa kwake, anapempha atumwiwo kuti amupempherere kuti asakhalenso ndi maganizo amenewa.—Machitidwe 8:18-24.

KODI MUNGATANI KUTI MUKHALE NZIKA YA UFUMU WA MULUNGU?

Aliyense akhoza kukhala nzika ya Ufumu wa Mulungu. (Machitidwe 10:34, 35) Koma kuti zimenezi zitheke, muyenera kuphunzira mfundo zomwe zingakuthandizeni.Padziko lonse, a Mboni za Yehova amaphunzira Baibulo ndi anthu kwaulere. Iwo angakusonyezeni mmene amachitira zimenezi. Phunziroli likhoza kuchitika kwa mphindi 10 kapena kuposa pamenepo, mlungu uliwonse. Kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni kudziwa zambiri zokhudza “uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.” Kungakuthandizeninso kudziwa zimene Ufumuwu udzachite pothetsa zinthu zachinyengo zomwe zimachitika padzikoli. (Luka 4:43) Mungafunse a Mboni za Yehova a m’dera lanu kapena mungapite pa webusaiti yathu ya jw.org/ny.

Kodi mukufuna kuti wa Mboni aziphunzira nanu Baibulo kwaulere?

^ ndime 8 Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.

^ ndime 22 Onani nkhani yakuti, “Kodi N’zotheka Kuchita Zinthu Mwachilungamo M’dziko Laziphuphuli?” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2012.