Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KHALANI MASO

Anthu Akuwononga Dziko Lapansi—Kodi Baibulo Limanena zotani?

Anthu Akuwononga Dziko Lapansi—Kodi Baibulo Limanena zotani?

 Mu lipoti lomwe linatuluka pa 4 April 2022, lonena za msonkhano wa atsogoleri amayiko pa nkhani yakusintha kwa nyengo, António Guterres yemwe ndi mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations ananena kuti: “Anthu akuchita zinthu zomwe pamapeto pake zifika powonongeratu nyengo. Tikunena pano, madzi akusefukira m’mizinda ikuluikulu. Dzikoli likutenthanso kwambiri. Kukuchitika mphepo zamkuntho zoopsa. M’madera ambiri madzi akusowa. Mitundu yambiri ya zinyama ndi zomera ikutha. Sikuti tikungolankhula kapena kunena mokokomeza, koma ngati mayiko sachitapo chilichonse, zimenezi ndi zomwe zichitikedi mogwirizana ndi zomwe kafukufuku wasayansi akutiuza.”

 Nyuzipepala ina inanena kuti: “Asayansi akuchenjeza kuti m’zaka zikubwerazi, pafupifupi nkhalango zonse zokwana 423 za ku United States, zidzawonongekeratu ndi kusintha kwa nyengo makamaka chifukwa cha kutentha. Zinthu monga kubuka kwa moto, kusefukira kwa madzi, kusungunuka kwa ayezi, kuwonjezeka kwa madzi am’nyanga komanso kutentha, ndi zomwe zikuyembekezeka kudzachitika ndipo zikufunana ndi zinthu zoopsa zomwe timaziwerenga m’Baibulo.”—“Flooding Chaos in Yellowstone, a Sign of Crises to Come,” The New York Times, June 15, 2022.

 Kodi mavuto okhudza zachilengedwewa ndi otheka kuthana nawo? Ngati ndi choncho, ndani angawathetse? Onani zomwe Baibulo limanena.

Baibulo linaneneratu kuti anthu adzawononga zachilengedwe

 Baibulo limanena kuti Mulungu ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.” (Chivumbulutso 11:18) Pavesili tikuphunzirapo zinthu zitatu:

  1.  1. Zochita za anthu zidzawonongetsa zachilengedwe

  2.  2. Kuwonongeka kwa zinthu zachilengedwe kudzatha

  3.  3. Mulungu ndi amene adzathetse mavuto a kuwonongeka kwa zachilengedwe, osati anthu.

Dziko lapansili lili ndi tsogolo labwino kwambiri

 Baibulo limafotokoza kuti, “dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.” (Mlaliki 1:4) Padzikoli padzakhalabe anthu nthawi zonse.

  •   “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.

 Zinthu zomwe zinawonongeka, zidzabwezeretsedwanso.

  •   “Chipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala. Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi.”—Yesaya 35:1.