Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndi Ndani Amene Adzapulumutse Dzikoli?

Kodi Ndi Ndani Amene Adzapulumutse Dzikoli?

 Anthu ambiri akuda nkhawa chifukwa choti amaganiza kuti anthu akuwononga dzikoli komanso moyo wapadzikoli. Akatswiri ena a zachilengedwe amanena kuti zimene anthu akuchita panopa zikhoza kuwonongeratu mitundu ina ya zinyama ndi zitsamba.

 Kodi n’zoona kuti anthu adzawononga dzikoli? Kapena kodi adzatha kukhala bwinobwino padzikoli popanda kuwononga zinthu?

Kodi anthu angapulumutse dzikoli?

 Akatswiri ambiri amaona kuti anthu akhoza kuteteza dzikoli n’kumachita zinthu popanda kuliwononga. Koma akatswiri ena amanena kuti anthu ayenera kusintha zinthu zambiri pa nthawi imodzi kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino padzikoli. Zinthu zina zimene ziyenera kusinthidwa ndi izi:

  •   Kusintha mmene timasamalirira nkhalango, madambo, nyanja ndi malo ena.

  •   Kusintha njira zolimira komanso mmene timapangira mphamvu za magetsi ndi zina zotere.

  •   Kuyamba kudya masamba ambiri n’kuchepetsa nyama ndi nsomba zimene timadya. Kuchepetsanso chakudya chimene timadya komanso kutaya.

  •   Kuzindikira kuti kukhala ndi moyo wabwino sikudalira kukhala ndi zinthu zambiri

 Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi n’zotheka kuti maboma, mabizinezi komanso anthu onse azigwirizana posintha zinthuzi? Kapena kodi mukuganiza kuti makhalidwe oipa amene anthu amasonyeza monga dyera, kudzikonda komanso kusaganizira zam’tsogolo angalepheretse zimenezi?​—2 Timoteyo 3:1-5.

Tingayembekezere zinthu zabwino

 Baibulo limalonjeza kuti dziko lathu silidzatha. Limafotokozanso kuti zimene anthu angachite sizingapulumutse dzikoli. Koma limafotokoza zinthu zimene ziyenera kusintha komanso mmene zinthuzi zidzasinthire.

 N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene anthu angachite paokha sizingapulumutse dzikoli? Yehova a Mulungu analenga dzikoli ndipo anapatsa anthu udindo wolisamalira. (Genesis 1:28; 2:15) Koma anthu akanatha kukwaniritsa udindowu pokhapokha ngati akanadalira Mulungu kuti aziwatsogolera komanso kumvera malangizo ake. (Miyambo 20:24) Koma anthu anakana kumvera Yehova ndipo anayamba kuchita zimene ankafuna. (Mlaliki 7:29) Paokha anthu sangasamalire dzikoli ndipo akayesetsa bwanji sangakwanitse kusinthiratu zinthu.​—Miyambo 21:30; Yeremiya 10:23.

 Zinthu zimene ziyenera kusintha. Mulungu sadzalola kuti anthu awononge dzikoli. (Chivumbulutso 11:18) Iye sadzangokonza maboma ndi mabungwe amene akuwononga dzikoli koma adzawachotsa. (Chivumbulutso 21:1) N’chifukwa chake Yehova ananena kuti: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.”​—Chivumbulutso 21:5.

 Mmene zinthuzi zidzasinthire. Yehova adzachotsa maboma a anthu n’kuika boma lakumwamba lomwe ndi Ufumu wa Mulungu. Boma limeneli lotsogoleredwa ndi Yesu Khristu lizidzalamulira dzikoli.​—Danieli 2:44; Mateyu 6:10.

 Ufumu wa Mulungu uzidzaphunzitsa anthu kuti azitsatira mfundo zachilungamo za Mulungu. Anthu akadzayamba kutsatira malangizo a Mulungu, adzatha kuchita zinthu mogwirizana ndi chilengedwe, osachiwononga. (Yesaya 11:9) Baibulo limafotokoza kuti boma la Mulungu lidzathandiza anthu ake kuti akhale ndi moyo wabwino kwambiri popanda kuwononga dzikoli. Lidzachita zinthu zotsatirazi:

 Tingayembekezere kuti Ufumu wa Mulungu udzachita zinthu zimenezi posachedwapa. Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti ““Kodi Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulira Dzikoli?

a Yehova ndi dzina la Mulungu.​—Salimo 83:18.