Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO | SARA

“Ndiwe Mkazi Wokongola”

“Ndiwe Mkazi Wokongola”

SARA ankakhala ku Middle East ndipo anali mkazi wokongola kwambiri. N’kutheka kuti tsiku lina anaima m’chipinda china cha m’nyumba yake n’kumayang’ana katundu yemwe anali m’nyumbamo. Mwina pa nthawiyi ankaoneka wokhumudwa. Ngati zinalidi choncho, n’zosadabwitsa. Panali zambiri zimene zinachitika pa moyo wa mayi ameneyu ndi mwamuna wake wokondedwa. Mwamuna wakeyu dzina lake anali Abulahamu. * Iwo anali atakhala m’nyumba yawoyi kwa zaka zambiri.

Sara ndi mwamuna wake ankakhala mumzinda wa Uri womwe unali wotukuka. Anthu ambiri a mumzindawu ankachita malonda komanso munali anthu ambiri aluso lopanga zinthu zosiyanasiyana. Choncho banjali liyenera kuti linali ndi katundu wambiri. Koma sikuti nyumba ya Sara inangokhala malo osungiramo katundu. Iye ndi mwamuna wake anakhala m’nyumbayi kwa zaka zambiri ndipo inkawakumbutsa zinthu zosangalatsa komanso zokhumudwitsa zimene anakumana nazo. Akakhala m’nyumbayi ankapemphera kwa Mulungu wawo, Yehova. Choncho mpake kuti Sara ankakonda kwambiri nyumba yakeyi.

Komabe Sara anali wokonzeka kusamuka n’kusiya chilichonse. Ngakhale kuti mwina anali ndi zaka 60, anavomera kusamuka n’kupita kumalo achilendo ndipo panalibe chiyembekezo choti adzabwereranso. Ankadziwanso kuti kumeneko angathe kukakumana ndi mavuto ambiri. Koma kodi n’chiyani chinachititsa kuti zinthu zisinthe choncho pa moyo wake? Nanga tingaphunzire chiyani pa chikhulupiriro cha Sara?

“TULUKA M’DZIKO LAKO”

Sara ayenera kuti anakulira mumzinda wa Uri. Masiku ano pamene panali mzindawu pali bwinja. Koma m’nthawi ya Sara a malonda ankabweretsa mumzindawu katundu wamtengo wapatali kudzera m’maboti omwe ankadutsa mumtsinje wa Firate. Anthu ankakhala pikitipikiti mumzindawu. Panalinso sitima zambiri zomwe zinkabweretsa katundu amene ankagulitsidwa m’mashopu. Ndiye popeza Sara anakulira komweku, ayenera kuti ankadziwa anthu ambiri a mumzindawu. Nawonso ayenera kuti ankamudziwa kwambiri mayi ameneyu popeza anali wokongola zedi komanso anali ndi banja lalikulu.

Baibulo limati Sara anali ndi chikhulupiriro cholimba. Komatu sikuti iye ankakhulupirira mulungu wa mwezi amene anthu ambiri a mumzindawu ankamulambira. Mumzinda wa Uri munali nsanja yaitali ya mulungu ameneyu. Koma Sara ankalambira Yehova, yemwe ndi Mulungu woona. Baibulo silinena kuti n’chiyani chinathandiza Sara kuti akhale ndi chikhulupiriro. Ndipotu pa nthawi ina bambo ake ankalambira mafano. Kenako Sara anakwatiwa ndi Abulahamu yemwe anali wamkulu kuposa iyeyo ndi zaka 10. * (Genesis 17:17) Patapita nthawi Abulahamu ankadziwika kuti anali ‘tate wa onse okhala ndi chikhulupiriro.’ (Aroma 4:11) Abulahamu ndi Sara anali ndi banja lolimba ndipo ankalemekezana komanso ankalankhulana momasuka. Akakhala ndi mavuto, ankayesetsa kuthana nawo limodzi. Koma chachikulu n’choti onse ankakonda kwambiri Mulungu.

Sara ankamukonda kwambiri mwamuna wake ndipo nyumba yawo inali pafupi ndi achibale awo. Koma pasanapite nthawi, banjali linakumana ndi vuto lina. Baibulo limati Sara “anali wosabereka, choncho analibe mwana.” (Genesis 11:30) Pa chikhalidwe chawo, kusabereka linali vuto lalikulu. Koma Sara anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu komanso kwa mwamuna wake. Iwo ankakhala ndi Loti, yemwe anali mwana wa mchimwene wake wa Abulahamu, ndipo ankangomutenga ngati mwana wawo weniweni. Banjali linkakhala bwinobwino, koma kenako panachitika zinazake.

Tsiku lina Abulahamu anapita kwa Sara akuoneka wosangalala kwambiri. Anali atalankhula ndi Yehova Mulungu amene anaonekera kwa iye kudzera mwa mngelo. Sara atamva zimenezi mtima wake unali phaphapha ndipo ankafunitsitsa kuti amve zimene mngeloyo ananena. Mwina Abulahamu anakhala kaye pansi, uku akuyesa kuganizira zoti anene. Kenako anauza Sara kuti Yehova wamuuza kuti: “Tuluka m’dziko lako ndi pakati pa abale ako. Tiye ukalowe m’dziko limene ine ndidzakusonyeza.” (Machitidwe 7:2, 3) Kenako banjali linayamba kuganizira zimene Yehova anawauzazi. Ankafunika kusiya moyo wawofuwofu n’kukayamba moyo wosamukasamuka komanso wokhala m’mahema. Ndiye kodi pamenepa Sara akanatani? Kodi akanavomera kusamuka ndi mwamuna wake, ngakhale kuti izi zikanasintha kwambiri moyo wawo? Abulahamu ayenera kuti ankangoyang’anitsitsa mkazi wakeyu kuti aone kuti atani.

Mwina tingaganize kuti zimene zinachitikira Sara sizingatichitikire ifeyo. Tingamaganize kuti, ‘Mulungu sanatipemphepo kuti tichite zinthu ngati zimenezi.’ Komatu zoona n’zakuti tonsefe nthawi zina timafunika kusankha pa zinthu ngati zimenezi. Dziko limene tikukhalali lingatipangitse kuti tizingoganizira zokhala ndi moyo wawofuwofu, katundu wambiri komanso kukonza tsogolo. Koma Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziika zinthu zokhudza kulambira Mulungu pamalo oyamba. (Mateyu 6:33) Choncho tikamaganizira zimene Sara anasankha pa nkhaniyi, tizidzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikufuna kusankha kuchita chiyani pa moyo wanga?’

“ANASAMUKA”

Sara atayamba kulongedza katundu, ankafunika kusankha zoti atenge ndi zoti asiye. Sakanatha kutenga zinthu zikuluzikulu chifukwa abulu ndi ngamila sakanakwanitsa kunyamula zinthu zimenezo. Komanso katundu woteroyo sakanagwirizana ndi moyo wosamukasamuka. Choncho katundu wawo wambiri ayenera kuti anamugulitsa kapena anapatsa anthu ena. Ankadziwanso kuti asiyana ndi moyo wa m’tauni umene sankavutika kupita kumsika komanso kumashopu ogulitsa zinthu ngati tirigu, nyama, zipatso, zovala ndi zinthu zina zabwinozabwino.

Chifukwa cha chikhulupiriro, Sara analolera kusamuka n’kusiya moyo wawofuwofu

Mwina chimene chinali chovuta kwambiri kwa Sara, kunali kusiya nyumba yawo. N’kutheka kuti nyumba yawoyi inali yofanana ndi nyumba za mumzinda wa Uri zimene akatswiri ofukula zinthu zakale anapeza. Ngati zinalidi choncho, ndiye kuti anasiya nyumba yapamwamba kwambiri. Nyumba zambiri za mumzindawu zinkakhala ndi zipinda zoposa 12 komanso zinkakhala ndi madzi a m’mipope, masinki komanso zimbudzi za madzi. Ngakhale nyumba yoti si yaikulu kwambiri inkakhala ndi denga labwino, makoma olimba komanso zitseko zamphamvu. Izi zinali zosiyana kwambiri ndi mahema. Anthu amene akukhala m’mahema sangakhale otetezeka kwa akuba ndiponso kwa zinyama monga mikango, akambuku, zimbalangondo komanso mimbulu. Nyama zimenezi zinali zofala kwambiri m’madera otchulidwa m’Baibulo.

Koma panalinso nkhani ina yovuta kwambiri kwa Sara. Iye anafunika kusiya achibale ake. Paja Mulungu anauza Abulahamu kuti: “Tuluka m’dziko lako ndi pakati pa abale ako.” Mayi wachikondi komanso wochezeka ameneyu ayenera kuti ankagwirizana kwambiri ndi azichimwene ake, azichemwali ake, azimalume ake, azakhali ake komanso ana aamuna ndi aakazi a azibale akewa. Ndipotu panalibe umboni woti adzakumana nawonso. Komabe Sara anachita zinthu molimba mtima ndipo anapitiriza kukonzekera ulendo.

Ngakhale kuti panali mavuto onsewa, Sara anamaliza kulongedza ndipo ankangodikira tsiku lonyamuka. Tera anali woti apita nawo pa ulendowu ngakhale kuti anali ndi zaka pafupifupi 200. (Genesis 11:31) N’zosakayikitsa kuti Sara anali ndi ntchito yaikulu yosamalira apongozi ake achikulirewa. Tsiku lonyamuka litafika, banjali linamvera Mulungu ‘n’kusamuka m’dziko la Akasidi’ ndipo nayenso Loti anapita nawo limodzi.Machitidwe 7:4.

Atanyamuka, analowera kumpoto chakumadzulo ndipo anadutsa m’mbali mwa mtsinje wa Firate. Atayenda mtunda wamakilomita 960, anafika ku Harana. Anthuwa anakhala kumeneku kwa kanthawi. N’kutheka kuti chifukwa cha ukalamba Tera anali atatopa kwambiri komanso atafooka moti sakanatha kupitiriza kuyenda. Choncho banjali linakhalabe ku Harana mpaka pamene Tera anamwalira ali ndi zaka 205. Kenako Yehova analankhulanso ndi Abulahamu ndipo anamuuza kuti achoke n’kupita kudziko limene adzamusonyeze. Koma pa nthawiyi anamulonjeza kuti: “Ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe.” (Genesis 12:2-4) Apa n’kuti Abulahamu ali ndi zaka 75 ndipo Sara anali ndi zaka 65, koma analibe mwana. Ndiye zikanatheka bwanji kuti mwa Abulahamu mudzatuluke mtundu waukulu? Kodi iye adzakwatira mkazi wina? Mwina Sara ankadzifunsa mafunso amenewa chifukwa pa nthawiyo anthu ambiri ankakwatira mitala.

Banjali linanyamukadi ku Harana. Baibulo limati Abulahamu ndi banja lake anatenga chuma chimene anapeza “komanso akapolo awo onse amene anapeza kudziko la Harana.” (Genesis 12:5) N’zosachita kufunsa kuti Abulahamu ndi Sara ankauza ena zimene ankakhulupirira. Nkhani zakale za Ayuda zimati akapolo amenewa anali anthu a mitundu ina amene anagwirizana ndi Abulahamu ndi Sara n’kuyamba kulambira Yehova. Ngati zinalidi choncho, ndiye kuti Sara analidi ndi chikhulupiriro cholimba ndipo anthu ankamumvetsera akamawauza za Mulungu. Tingaphunzire zambiri kwa Sara chifukwa masiku ano anthu ambiri alibe chikhulupiriro komanso chiyembekezo. Tikaphunzira mfundo inayake ya m’Baibulo, tingachite bwino kuuzako ena.

“ANANYAMUKA KULOWERA KU IGUPUTO”

Atawoloka mtsinje wa Firate anayamba kulowera chakumwera m’dziko limene Yehova anawalonjeza. N’kutheka kuti anawoloka mtsinjewu pa 14 mwezi wa Nisani m’chaka cha 1943 B.C.E. (Ekisodo 12:40, 41) Yerekezerani kuti mukuona Sara akuyang’ana uku ndi uku n’kumachita chidwi ndi zinthu zokongola zimene ankaona m’dzikoli komanso nyengo yake. Banjali litafika ku Sekemu, pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya More, Yehova anaonekeranso kwa Abulahamu n’kumuuza kuti: “Ndidzapereka dziko ili kwa mbewu yako.” Abulahamu ayenera kuti anaganizira kwambiri mawu akuti “mbewu.” Mwina anakumbukira mawu amene Yehova ananena mu Edeni akuti mbewu idzawononga Satana. Yehova anali atauza kale Abulahamu kuti anthu onse a padziko lapansi adzapeza madalitso kudzera mwa iyeyo.Genesis 3:15; 12:2, 3, 6, 7.

Komabe, banjali linkakumana ndi mavuto ngati anthu ena onse. Mwachitsanzo, m’dziko la Kanani munagwa njala ndipo Abulahamu anaganiza zosamukira ku Iguputo limodzi ndi banja lake. Koma anadziwa kuti ku Iguputoko akhoza kukakumana ndi vuto linalake. Choncho anauza Sara kuti: “Ndikudziwa ndithu kuti ndiwe mkazi wokongola m’maonekedwe ako. Aiguputo akakuona, mosakayikira anena kuti, ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Ndipo andipha ndithu, koma iweyo akusiya wamoyo. Ndiye chonde, unene kuti ndiwe mlongo wanga kuti zindiyendere bwino. Ukatero upulumutsa moyo wanga.” (Genesis 12:10-13) N’chifukwa chiyani Abulahamu anauza Sara kuti anene kuti ndi mlongo wake?

Anthu ena otsutsa Baibulo amanena kuti Abulahamu anali wabodza komanso wamantha. Koma zimenezi si zoona. Pajatu Sara analidi mlongo wake koma wobadwa kwa mayi ena. Zimene Abulahamu anachitazi zinali zomveka. Abulahamu ndi Sara ankadziwa kuti cholinga cha Yehova, choti adzatulutsa mtundu kudzera mwa Abulahamu, chinali chofunika kwambiri. Choncho zinali zofunika kwambiri kuti Abulahamu atetezedwe. Kuwonjezera pamenepa, akatswiri ofukula zinthu zakale anapeza kuti mafumu a ku Iguputo ankakonda kupha mwamuna n’kutenga mkazi wake. Choncho zimene Abulahamu anachitazi zinali zanzeru ndipo Sara anamvera maganizo a mwamuna wakewa.

Pasanapite nthawi, zimene Abulahamu ankaopazi zinachitikadi. Ngakhale kuti Sara sanali mtsikana, akalonga a Farao anaona kuti anali mkazi wokongola kwambiri. Choncho anauza Farao za Sara ndipo Faraoyo anawalamula kuti amubweretse kunyumba kwake. Zimenezi ziyenera kuti zinamupweteka kwambiri Abulahamu. N’kuthekanso kuti Sara anachita mantha posadziwa kuti zikamuthera bwanji. Komabe, zikuoneka kuti Sara atafika kwa Farao, ankamuchitira zinthu monga mlendo wolemekezeka osati ngati kapolo. Mwina Farao anakonza zoti amunyengerere komanso kumukopa ndi chuma chake ndipo kenako alankhule ndi mchimwene wake Abulahamu kuti amukwatire.Genesis 12:14-16.

Ndiye yerekezerani kuti mukuona Sara ali kunyumba yachifumu n’kumayang’ana malo okongola. Kodi anamva bwanji ataona kuti alinso m’nyumba yabwino komanso akupatsidwa zakudya zabwinozabwino? Kodi Sara anakopeka ndi moyo umenewu, womwe mwina unali wapamwamba kuposanso umene ankakhala ku Uri? Taganizirani mmene Satana akanasangalalira zikanakhala kuti Sara anaganiza zosiya mwamuna wake Abulahamu n’kukhala mkazi wa Farao. Koma n’zosangalatsa kuti Sara sanachite zimenezi. Iye anakhalabe wokhulupirika kwa mwamuna wake komanso kwa Yehova. Masiku ano anthu ambiri ndi osakhulupirika ndipo amakonda chiwerewere. Koma kodi mukuganiza kuti zinthu zikanakhala bwanji anthu onse apabanja akanakhala okhulupirika ngati Sara? Kodi inuyo mungatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Sara pa nkhani yokhala okhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wanu komanso anzanu?

Sara anakhalabe wokhulupirika kwa mwamuna wake ndipo sanatengeke ndi zimene anaona kunyumba kwa Farao

Yehova analowererapo ndipo anateteza Sara pogwetsa miliri kwa Farao ndi banja lake. Farao atazindikira kuti Sara anali mkazi wa Abulahamu, anamubweza kwa mwamuna wake ndipo anauza Abulahamu ndi banja lake kuti achoke ku Iguputo. (Genesis 12:17-20) Abulahamu ayenera kuti anasangalala kwambiri kukumananso ndi mkazi wake wokondedwayu. Paja pa nthawi ina anauza Sara kuti: “Ndikudziwa ndithu kuti ndiwe mkazi wokongola.” Koma apa tsopano anaona kuti mkazi wakeyo anali wokongolanso mwa njira ina. Sara analinso wokongola mumtima chifukwa anali ndi makhalidwe abwino omwe Yehova amasangalala nawo. (1 Petulo 3:1-5) Tonsefe tiyenera kuyesetsa kutsanzira Sara pa nkhani yokhala okhulupirika m’banja. Tiyeni tizitsanziranso Sara poyesetsa kukonda zinthu zauzimu, kuuza ena zokhudza Yehova komanso kukhalabe okhulupirika tikakumana ndi mayesero.

^ ndime 3 Poyamba mayina awo anali Abulamu ndi Sarai. Koma kenako Yehova anawapatsa mayina akuti Abulahamu ndi Sara ndipo anayamba kudziwika kwambiri ndi mayina amenewa.Genesis 17:5, 15.

^ ndime 8 Tingati Sara anali mchemwali wake wa Abulahamu. Onsewa bambo awo anali Tera koma amayi awo anali osiyana. (Genesis 20:12) Masiku ano n’zosayenera munthu kukwatira mchemwali wake. Koma tikumbukire kuti pa nthawiyo zinthu zinali zosiyana ndi pano. Nthawi imeneyo panali pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Adamu ndi Hava anakhala opanda ungwiro. Choncho munthu akakwatirana ndi m’bale wake wapafupi, sizinkabweretsa mavuto alionse kwa ana obadwawo. Koma patatha zaka 400, moyo unayamba kukhala waufupi ngati masiku ano. Choncho m’Chilamulo cha Mose munali lamulo loletsa munthu kukwatirana ndi wachibale wapafupi.Levitiko 18:6.