Pitani ku nkhani yake

Kodi Dzina la Buku la M’Baibulo, Lakuti Chivumbulutso, Limatanthauza Chiyani?

Kodi Dzina la Buku la M’Baibulo, Lakuti Chivumbulutso, Limatanthauza Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 Mawu achigiriki a buku la m’Baibulo la Chivumbulutso omwe ndi A·po·kaʹly·psis amatanthauza “kuvundukula” kapena “kuulula.” Dzinali limasonyeza tanthauzo labuku la m’Baibulo lakuti Chivumbulutso chifukwa chakuti limavundukula zinthu zimene zakhala zobisika komanso limaulula zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo. Maulosi ake ambiri sanakwaniritsidwebe.

Zimene zili m’buku la Chivumbulutso

Zinthu zimene zingatithandize kumvetsa buku la Chivumbulutso

  1.   Tanthauzo la zinthu zimene zinafotokozedwa m’buku la Chivumbulutso ndi zokhudza zinthu zosangalatsa osati zochititsa mantha kapena zoopsa kwa anthu amene amatumikira Mulungu. Ngakhale kuti anthu ambiri akangomva mawu akuti “Chivumbulutso” amaganiza za tsoka lalikulu, buku la Chivumbulutso limayamba komanso kutha ndi mawu onena kuti anthu amene amawerenga komanso kugwiritsira ntchito uthenga wopezeka m’bukuli adzakhala osangalala.​—Chivumbulutso 1:3; 22:7.

  2.   Buku la Chivumbulutso limafotokoza zinthu pogwiritsa ntchito zizindikiro kapena zithunzi zimene zingakhale zovuta kuzimvetsa ngati titaziganizira mmene zilili.​—Chivumbulutso 1:1.

  3.   Mbali zikuluzikulu za m’buku la Chivumbulutso ndiponso zizindikiro, zimafotokozedwa m’mabuku enanso a m’Baibulo:

  4.   Masomphenya amenewa amakhudza “tsiku la Ambuye” limene linayamba pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa m’chaka cha 1914 ndipo Yesu anayamba kulamulira monga Mfumu. (Chivumbulutso 1:​10) Zimenezi zikusonyeza kuti kukwaniritsidwa kwakukulu kwa masomphenyawa kukuchita masiku ano.

  5.   Kuti timvetse bwino zimene zili m’buku la Chivumbulutso tiyenera kugwiritsa ntchito zimene zimatithandiza kumvetsa Baibulo lonse. Zimenezi zikuphatikizaponso nzeru zochokera kwa Mulungu ndiponso anthu amene amalimvetsa bwino.​—Machitidwe 8:​26-39; Yakobo 1:5.