Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi tinalengedwa kuti tizingokhalako kwa nthawi yochepa?

Kodi nthawi zina mumaona kuti moyo ndi waufupi kwambiri?

Anthu ambiri amaganiza kuti cholinga cha moyo ndi kusangalala, kugwira ntchito, kukwatira, kukhala ndi ana kenako kukalamba. Kodi inunso mumaganiza choncho? (Yobu 14:1, 2) Baibulo limasonyeza kuti ngakhale anthu ena anzeru samvetsa cholinga cha moyo.—Werengani Mlaliki 2:11.

Ndiye kodi cholinga cha moyo n’chiyani? Kuti tipeze yankho la funsoli tikuyenera kudziwa kaye mmene anthufe tinalengedwera. Anthu ambiri ataganizira mmene ubongo komanso thupi lathu linalengedwera modabwitsa, anazindikira kuti anthufe tinalengedwa ndi Mulungu. (Werengani Salimo 139:14.) Ngati anatilenga modabwitsa chonchi ndiye kuti anatilenga ndi cholinga. Ndipotu kuzindikira cholinga chimenechi kungatithandize kukhala osangalala kwambiri.

Kodi Mulungu anatilengeranji?

Mulungu anadalitsa banja loyambirira n’kulipatsa udindo wapadera. Iye ankafuna kuti, abereke ana n’kudzaza dziko lapansi, akonze dziko lapansi kuti likhale paradaiso komanso kuti akhale ndi moyo wosatha.—Werengani Genesis 1:28, 31.

Pa nthawiyo cholinga cha Mulungu sichinakwaniritsidwe chifukwa banja loyambirira lija silinamumvere. Koma sikuti Mulungu anatinyanyala kapena anasintha cholinga chake. Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu anakonza njira yopulumutsira anthu okhulupirika komanso kuti cholinga chake chokhudza dziko lapansi chidzakwaniritsidwa. Choncho Mulungu akufuna kuti mudzasangalale ndi moyo mogwirizana ndi mmene iye anafunira. (Werengani Salimo 37:29) Kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni kudziwa zimene mungachite kuti mudzakhale ndi moyo wosatha.