Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Watsegula Maso Anga

Yehova Watsegula Maso Anga

Yehova Watsegula Maso Anga

Yosimbidwa ndi Patrice Oyeka

Ndinkasungulumwa moti ndinkangokhalira kumvera wailesi ndipo madzulo a tsiku lina, pambuyo potopa ndi mavuto anga, ndinaganiza zoti ndingodzipha. Ndinasungunula poizoni m’kapu n’kuika patebulo. Ndiyeno ndinaganiza kuti ndisambe kaye kenako ndivale zovala zabwino ndisanamwe poizoniyo. Koma kodi n’chifukwa chiyani ndinkafuna kudzipha? Nanga chinachitika n’chiyani kuti ndipezeke ndidakali moyo panopa n’kumafotokoza nkhaniyi?

NDINABADWA pa February 2, 1958, m’chigawo cha Kasaï Oriental, m’dziko la Democratic Republic of the Congo. Bambo anga anamwalira ndili ndi zaka 9 ndipo mchimwene wanga wamkulu ndi amene ananditenga n’kumandisamalira.

Nditamaliza sukulu, ndinayamba ntchito m’munda wina wa mitengo yopangira labala. Tsiku lina m’mawa m’chaka cha 1989 ndikulemba lipoti mu ofesi, mwadzidzidzi m’maso mwanga munachita mdima moti sindinathenso kuona chilichonse. Poyamba ndinkaganiza kuti magetsi azima, koma ndinkamva kulira kwa jenereta komanso unali m’mawa. Kenako ndinachita mantha kwambiri nditazindikira kuti ndikulephera kuona ngakhale zimene ndinkalemba.

Nthawi yomweyo ndinaitana mmodzi mwa anthu amene ndinkawayang’anira kuti andiperekeze pakachipatala ka pamalopo. Koma wamkulu wa pakachipatalako atandiona ananena kuti ndiyenera kukaonana ndi dokotala wa maso wa mumzindawo. Dokotalayo atazindikira mmene maso anga anawonongekera, anaona kuti vutoli linali lalikulu kwambiri choncho ananditumiza ku Kinshasa, lomwe ndi likulu la dzikoli.

Nditafika ku Kinshasa

Nditafika ku Kinshasa ndinaonana ndi madokotala osiyanasiyana a maso, koma onsewo sanathe kundithandiza. Nditakhala m’chipatala kwa masiku 43, madokotala ananena kuti ndidzakhala wakhungu moyo wanga wonse. Abale anga anayesetsa kupita nane m’matchalitchi osiyanasiyana amene amati amachiritsa anthu mozizwitsa koma palibe amene anandichiritsa.

Kenako ndinataya mtima kuti sindidzaonanso. Palibe chimene chinkayenda bwino pa moyo wanga. Ndinakhala wosaona, ntchito inandithera komanso mkazi wanga anandithawa ndipo pochoka anatenga katundu yense. Ndinkachita manyazi kutuluka panja komanso kucheza ndi anthu. Choncho, ndinayamba kumadzipatula ndipo nthawi zambiri ndinkangokhala m’nyumba. Zimenezi zinachititsa kuti ndizingokhala ndekhandekha ndipo ndinayamba kudziona ngati munthu wosafunikira.

Kawiri konse ndinkafuna kudzipha ndipo nthawi yachiwiri ndi imene ndafotokoza kumayambiriro kwa nkhani ino. Pa nthawi imeneyi ndinapulumuka chifukwa cha zimene mwana wina anachita. Ndikusamba, iye mosadziwa anatenga kapu imene munali poizoni ija n’kutayira pansi. Mwamwayi mwanayo sanamwe poizoniyo. Nditatuluka kubafa ndinadabwa kuti kapu ija palibe. Ndiyeno ndinaululira abale anga kuti ndimafuna kumwa poizoni kuti ndife.

Ndimayamikira Mulungu ndi abale anga chifukwa chondisamalira. Zimenezi zinachititsa kuti mapulani anga ofuna kudzipha alephereke.

Ndinayambanso Kusangalala Ndi Moyo

Lamlungu lina m’chaka cha 1992, nditakhala pansi n’kumasuta fodya, kunyumba kwathu kunafika a Mboni za Yehova awiri omwe pa nthawiyo ankalalikira kunyumba ndi nyumba. Atazindikira kuti ndine wosaona, anandiwerengera lemba la Yesaya 35:5 limene limati: “Pa nthawi imeneyo, maso a anthu akhungu adzatsegulidwa, ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva.” Ndinasangalala kwambiri nditamva mawu amenewa. Mosiyana ndi zimene ndinali nditauzidwa m’matchalitchi osiyanasiyana amene ndinapita, a Mboni za Yehova sanandiuze kuti angandichiritse mozizwitsa. M’malomwake iwo anandiuza kuti ngati ndingaphunzire ndi kumudziwa Mulungu, ndingadzayambirenso kuona m’dziko latsopano limene Mulungu akulonjeza. (Yohane 17:3) Nthawi yomweyo ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova pogwiritsa ntchito buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha M’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Ndinayambanso kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova ku Nyumba ya Ufumu ya kumene ndinkakhala komanso ndinasiya zinthu zina zimene ndinkachita kale, kuphatikizapo kusuta fodya.

Koma chifukwa chosaona ndinkalephera kupita patsogolo mwauzimu. Choncho ndinapita kusukulu ina ya anthu osaona kuti ndikaphunzire kuwerenga ndi kulemba zilembo za anthu akhungu. Zimenezi zinachititsa kuti ndithe kulowa nawo sukulu yomwe imathandiza a Mboni kuti azitha kulalikira imene imachitika pa Nyumba ya Ufumu. Choncho ndinayamba kulalikira kwa anthu a m’dera lathu. Zimenezi zinachititsa kuti ndiyambenso kusangalala ndi moyo. Ndinapita patsogolo mwauzimu, moti pa May 7, 1994 ndinabatizidwa posonyeza kudzipereka kwanga kwa Yehova.

Pomwe chikondi changa pa Yehova ndi anthu chinkakula, ndinayamba kufunitsitsa kuti ndizilalikira nthawi zonse. Ndakhala ndikuchita utumiki umenewu kuyambira pa December 1, 1995. Komanso kuyambira m’mwezi wa February 2004, ndinakhala ndi mwayi wotumikira monga mkulu mu mpingo wathu. Nthawi zina ndimaitanidwa kukakamba nkhani zochokera m’Baibulo ku mipingo ina ya m’dera lathu. Zimenezi zimandithandiza kukhala wosangalala kwambiri komanso kuzindikira kuti kulumala sikungalepheretse munthu kukwaniritsa cholinga chake chotumikira Yehova Mulungu.

Yehova Wandipatsa Maso Ena

Monga ndafotokozera, mkazi wanga anandisiya chifukwa choti ndine wosaona. Koma Yehova wandipatsanso madalitso ena. Ndinganene kuti wandipatsa maso kuti ndizitha kuona. Anny Mavambu anavomera kuti ndikhale mwamuna wake ngakhale kuti ndine wosaona. Iye ali ngati maso anga popeza nayenso amalalikira nthawi zonse ndipo amapita nane limodzi kokalalikira. Amandiwerengeranso malifalensi a nkhani zanga n’cholinga choti ndilembe manotsi a nkhanizo m’zilembo za anthu a khungu. Iye wakhaladi dalitso kwa ine. Mkazi wangayu wandithandiza kuzindikira kuti mawu opezeka palemba la Miyambo 19:14 ndi oona. Lembali limati: “Cholowa chochokera kwa makolo ndicho nyumba ndi chuma, koma mkazi wanzeru amachokera kwa Yehova.”

Yehova wadalitsanso banja lathu chifukwa watipatsa ana awiri, wamwamuna ndi wamkazi. Ndikuyembekezera mwachidwi kudzaona nkhope zawo m’Paradaiso. Madalitso ena amene ndapeza ndi oti mchimwene wanga wamkulu, amene anatikomera mtima kuti tizikhala pamalo ake, anavomera kuphunzira Baibulo ndipo anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Panopa tonse tili mu mpingo umodzi.

Ngakhale kuti sindiona, ndimafunitsitsa nditachita zambiri potumikira Mulungu chifukwa cha madalitso ochuluka amene iye wandipatsa. (Malaki 3:10) Tsiku lililonse ndimapempha kuti Ufumu wake ubwere kuti udzachotse mavuto onse padzikoli. Kuchokera pamene ndinadziwa Yehova, ndimalankhula motsimikiza kuti: “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa, ndipo sawonjezerapo ululu.”​—Miyambo 10:22.

[Zithunzi patsamba 13]

Ndikukamba nkhani yochokera m’Baibulo; ndili ndi banja langa komanso mchimwene wanga