Kodi Mungatani Ngati Mwayamba Kupeza Ndalama Zochepa?
Kodi Mungatani Ngati Mwayamba Kupeza Ndalama Zochepa?
BAMBO wina dzina lake Obed, yemwe ali ndi ana awiri, ankagwira ntchito pahotela yapamwamba kwambiri mumzinda wina waukulu kwambiri mu Africa. Iye anagwira ntchitoyi kwa zaka 10 ndipo inkamuthandiza kusamalira banja lake mosavuta. Nthawi zina pa nthawi ya tchuti ankatha kupita ndi banja lake kukasangalala kumalo osungirako nyama zakutchire. Koma zonsezi zinatha iye atachotsedwa ntchito chifukwa cha kuchepa kwa makasitomala omwe ankabwera pahotelapo.
Stephen ankagwira ntchito kubanki ina yaikulu kwa zaka zoposa 22 ndipo anakhala akukwezedwa maudindo mpaka anakhala mmodzi mwa akuluakulu a bankiyo. Mwa zina, kampani yakeyi inamupatsa nyumba yabwino yoti azikhalamo, galimoto, anthu antchito komanso inkalipilira ana ake sukulu zapamwamba. Koma pamene bankiyo inkasintha kagwiridwe kake ka ntchito, Stephen anachotsedwa ntchito. Stephen anati: “Ine ndi banja langa tinathedwa nzeru. Ndinakhumudwa kwambiri komanso ndinali ndi nkhawa posadziwa kuti zindithera bwanji.”
Zinthu ngati zimenezi zikuchitikira anthu ambiri. Mavuto azachuma amene akupitirirabe padziko lonse achititsa kuti anthu ambiri, amene zinthu zinkawayendera bwino pa nkhani ya chuma, ntchito iwathere. Ndipo ambiri amene amapezanso ntchito, imakhala yamalipiro ochepa osagwirizana ndi kukwera mitengo kwa zinthu. Mayiko onse, ndi otukuka omwe, akukumana ndi mavuto obwera chifukwa cha kusayenda bwino kwa chuma komanso kusowa kwa ntchito.
Kufunika Kochita Zinthu Mwanzeru
Munthu amene akulandira ndalama zochepa kapena amene ntchito yamuthera angakhale ndi nkhawa kwambiri. N’zoona kuti sizingatheke kupeweratu nkhawa, komabe munthu wina wanzeru anati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.” (Miyambo 24:10) Choncho m’malo mosoweratu mtengo wogwira tikakumana ndi mavuto azachuma, tiyenera kutsatira zimene Mawu a Mulungu amatiuza. Mawu a Mulungu amatilimbikitsa ‘kusunga nzeru zopindulitsa.’—Miyambo 2:7.
Ngakhale kuti Baibulo si buku lazachuma, malangizo amene limapereka pa nkhaniyi athandiza anthu ambiri padziko lonse. Tiyeni tikambirane mfundo zina za m’Baibulo zimene zingatithandize.
Muzipanga bajeti. Taganizirani mawu a Yesu opezeka palemba la Luka 14:28 akuti: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo?” Kutsatira mfundo imeneyi kumatanthauza kukhala ndi bajeti komanso kuyesetsa kuitsatira. Koma malinga ndi zimene Obed ananena, nthawi zina kuchita zimenezi n’kovuta. Iye anati: “Ntchito isanandithere, tinkakonda kupita kumasitolo akuluakulu kukagula katundu wambirimbiri amene tikufuna, ndi wosafunikira yemwe. Sitinkapanga bajeti chifukwa tinkaona kuti tinkakhala ndi ndalama zogula chilichonse chimene tingafune.” Kuganizira pasadakhale zimene muyenera kugula, kungathandize kuti ndalama zochepa zimene mumapeza muzizigwiritsa ntchito pa zinthu zimene banja lanu likufunikiradi.
Muyenera kusintha zinthu zina pa moyo wanu. Kusintha kuti munthu ayambe kukhala moyo wotsikirapo n’kovuta komabe n’kofunika. Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Stephen ananena kuti: “Kuti tisamawononge ndalama zambiri, tinasamukira m’nyumba yathu, yomwe inali yaing’ono komanso yosatha kwenikweni. Ana athu tinawasamutsira kusukulu zina zotsikirako mtengo zomwe zimaphunzitsanso bwino.”
Kuti anthu onse m’banjamo akwanitse kusintha n’kuyamba kukhala moyo wotsikirapo, pamafunika kukambirana momasuka. Mwachitsanzo, bambo wina dzina lake Austin ankagwira ntchito m’bungwe linalake lokongoza ndalama. Iye anagwira ntchitoyo kwa zaka 9 koma kenako anachotsedwa. Austin anati: “Ine ndi mkazi wanga tinakhala pansi n’kulemba zinthu zimene zinali zofunika kwambiri. Tinafunika kusiya kugula zakudya zodula, kupita kutchuti kumene kunkatiwonongera ndalama zambiri komanso tinayenera kuchepetsa kugula zovala zambiri. Ndimasangalala chifukwa banja langa linagwirizana ndi kusintha kumene tinapangaku.” Mwina ana aang’ono sangamvetse chifukwa chake mukufunika kusintha zina ndi zina, komabe makolonu ndi udindo wanu kuwathandiza kuti amvetse.
Khalani wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yomwe ingapezeke. Ngati munazolowera kugwira ntchito ya muofesi, zingakuvuteni kuti mugwire ntchito zooneka ngati zotsika. Austin anati: “Chifukwa choti ndakhala ndikugwira ntchito ngati bwana kwa nthawi yaitali, zinkandivuta kwambiri kuti ndilowe ntchito iliyonse yotsika.” Zimenezi sizachilendo chifukwa lemba la Miyambo 29:25 limati: “Kuopa anthu n’kumene kumatchera msampha.” Kuganizira kwambiri zimene anthu angaganize akamva kuti mwayamba ntchito yotsika, kungachititse kuti mulephere kugwira ntchito imene ikanakuthandizani kupeza zofunika za banja lanu. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kupewa maganizo olakwikawa?
Chofunika kwambiri n’kukhala wodzichepetsa. Obed atachotsedwa ntchito pahotela ija, mnzake anamuitana kuti azikagwira naye limodzi ntchito pamalo ake okonzera magalimoto. Nthawi zina ankafunika kuyenda wapansi mtunda wautali komanso m’misewu yafumbi kuti akagule penti wa galimoto komanso zipangizo zina. Obed anati: “Sindinkaikonda ntchito imeneyi, komabe sindikanachitira mwina. Kudzichepetsa kunandithandiza kuti ndizigwira ntchito ya malipiro ochepa kwambiri poyerekezera ndi imene ndinkagwira poyamba komabe malipiro amenewa amandithandiza kupezera banja langa zofunika.” Nanunso kukhala ndi mtima wodzichepetsa kungakuthandizeni.
Muzikhutira ndi zomwe muli nazo. Dikishonale ina inafotokoza kuti munthu wokhutira ndi zomwe ali nazo “amakhutira ndi mmene zinthu zilili pa moyo wake ndipo amakhalabe wosangalala.” Munthu amene ali pa mavuto aakulu azachuma angaone kuti zimenezi n’zosatheka. Komabe taganizirani zimene ananena mtumwi Paulo, yemwe anali mmishonale ndipo ankadziwa mmene zimakhalira munthu akamasowa zofunika pa moyo. Iye anati: “M’zochitika zosiyanasiyana ine ndaphunzira kukhala wokhutira ndi zimene ndili nazo. Ndithudi, kukhala wosowa ndimakudziwa, kukhala ndi zochuluka ndimakudziwanso.”—Afilipi 4:11, 12.
N’kutheka kuti pakali pano zinthu zili bwino pa moyo wathu koma popeza zinthu padzikoli zikusintha mofulumira, tsiku lina tikhoza kupezeka tili pa mavuto aakulu. Choncho tingapindule kwambiri ngati tingagwiritse ntchito malangizo amene mtumwi Paulo anauziridwa kulemba, akuti: “Ndithudi, kukhala wodzipereka kwa Mulungu kumeneko limodzi ndi kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo, ndi njiradi yopezera phindu lalikulu. Choncho, pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.” Pamenepa sikuti Paulo ankalimbikitsa ulesi koma anafotokoza mmene tingadziwire zinthu zofunika kwambiri pa moyo.—1 Timoteyo 6:6, 8.
Mmene Tingapezere Chimwemwe Chenicheni
Kupeza chilichonse chimene ukufuna n’kumakhala moyo wawofuwofu sikumene kumachititsa munthu kukhala wosangalala. Yesu ananena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” Choncho, kugwiritsa ntchito zinthu zimene tili nazo pothandiza ena komanso kuyesetsa kukhala wolimbikitsa kwa ena, n’kumene kumabweretsa chimwemwe chenicheni.—Machitidwe 20:35.
Mlengi wathu, Yehova Mulungu, amadziwa zonse zimene timafunikira. Kudzera m’Mawu ake Baibulo, iye wapereka malangizo abwino amene athandiza anthu ambiri kukhala ndi moyo wabwino komanso kuchepetsa nkhawa. N’zoona kuti, sikuti tikangoyamba kutsatira malangizo a m’Baibulo ndiye kuti basi nthawi yomweyo mavuto athu azachuma atha. Koma Yesu anatsimikizira anthu amene amapitirizabe “kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo [cha Mulungu]” kuti Mulungu adzawapatsa zinthu zofunikira pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.—Mateyu 6:33.