Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Ankachita Nawo Ndale?

Kodi Yesu Ankachita Nawo Ndale?

Kodi Yesu Ankachita Nawo Ndale?

AMENE analemba Mauthenga Abwino anafotokoza kuti Yesu anakumana ndi zinthu zosiyanasiyana pa utumiki wake zimene zikanachititsa kuti ayambe ndale. Mwachitsanzo, Yesu atangobatizidwa kumene, ali ndi zaka pafupifupi 30, Mdyerekezi ankafuna kumupatsa udindo woti akhale wolamulira wa dziko lonse. Kenako anthu ankafuna kuti Yesu akhale mfumu. Komanso patapita nthawi anthu ena ankafuna kuti Yesu akhale katswiri wazandale. Kodi Yesu anatani? Tiyeni tikambirane nkhani zimenezi.

Wolamulira wa dziko lonse. Nkhani za m’Mauthenga Abwino zimanena kuti Mdyerekezi ankafuna kupatsa Yesu “maufumu onse a padziko.” Taganizani mmene zinthu zikanasinthira n’kuyamba kuyenda bwino Yesu akakhala kuti anavomereza zoti akhale wolamulira wa dzikoli. Kodi pali wolamulira wokonda dziko lake, yemwe amafunitsitsa kuti ndale ziziyenda bwino yemwenso amafunitsitsa kuthetsa mavuto a anthu, amene angakane atapemphedwa kuti akhale wolamulira wa dziko? Komatu Yesu anakana.​—Mateyu 4:8-11.

Mfumu. Anthu ambiri a m’nthawi ya Yesu ankalakalaka atakhala ndi wolamulira amene akanathetsa mavuto awo azachuma komanso azandale. Atachita chidwi ndi zimene Yesu ankachita, iwo anafuna kuti akhale wandale. Kodi Yesu anatani? Yohane, yemwe analemba nawo Mauthenga Abwino, ananena kuti: “Yesu atadziwa kuti iwo akufuna kumugwira kuti amuveke ufumu, anachoka ndi kupitanso kuphiri yekhayekha.” (Yohane 6:10-15) Apatu n’zoonekeratu kuti Yesu anakana kulowerera ndale.

Katswiri wazandale. Taganizirani zimene zinachitika Yesu atatsala pang’ono kuphedwa. Ophunzira a Afarisi amene sankafuna kulamulidwa ndi Aroma, komanso anthu a chipani cha Herode amene ankagwirizana ndi Aroma, anapita kwa Yesu. Cholinga chawo chinali kuchititsa Yesu kuti asonyeze mbali yomwe anali pa nkhani ya ndale. Iwo anamufunsa ngati kunali koyenera kuti Ayuda azipereka msonkho ku boma la Roma.

Maliko analemba zimene Yesu anayankha. Iye anati: “‘Bwanji mukundiyesa? Bweretsani khobidi la dinari kuno ndilione.’ Iwo anam’patsadi. Ndipo iye anawafunsa kuti: ‘Kodi chifaniziro ichi ndi mawu akewa n’zandani?’ Iwo anayankha kuti: ‘Ndi za Kaisara.’ Pamenepo Yesu anati: ‘Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma zinthu za Mulungu muzizipereka kwa Mulungu.’” (Maliko 12:13-17) Pothirira ndemanga pa chifukwa chimene Yesu anayankhira chonchi, buku lina linati: “Iye anapewa kukhala mesiya wazandale ndipo mosamala anasonyeza kusiyana kumene kulipo pakati pa zinthu zoyenera kuchitira Kaisara ndi zoyenera kuchitira Mulungu.”​—Church and State​—The Story of Two Kingdoms.

Sikuti Khristu sankakhudzidwa ndi mavuto a anthu monga umphawi, katangale komanso kupanda chilungamo. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti iye ankakhudzidwa ndi zinthu zomvetsa chisoni zimene zinkawachitikira anthu. (Maliko 6:33, 34) Komabe, Yesu sanayambe ntchito yochotsa kupanda chilungamo kumene kunkachitika, ngakhale kuti anthu ena anayesetsa kumunyengerera kuti azilowerera m’zochitika za pa nthawiyo.

Zitsanzo zimenezi zikuchita kusonyezeratu kuti Yesu anakana kulowerera nkhani zandale. Nanga bwanji Akhristu masiku ano? Kodi iwo ayenera kulowerera nkhani zandale?