Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Anthu ambiri amapemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere. Koma kodi munadzifunsapo kuti, Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani komanso udzachita zotani?

TAONANI ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

  • Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?

    Ndi boma lakumwamba ndipo Yesu Khristu ndi Mfumu yake.​—Yesaya 9:6, 7; Mateyu 5:3; Luka 1:31-33.

  • Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani?

    Udzathetsa zoipa zonse ndipo udzabweretsa mtendere wosatha padzikoli.​—Danieli 2:44; Mateyu 6:10.

  • Kodi kufunafuna Ufumu choyamba n’kutani?

    Ndi kukhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu komanso kukhulupirira kuti ndi Ufumu wokhawu umene udzakonze zinthu padzikoli kuti zikhale mmene Mulungu amafunira.​—Mateyu 6:33; 13:44.