NSANJA YA OLONDA Na. 2 2020 | Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Anthu akhala akufunsa funso limeneli kwa zaka zambiri. Koma yankho lake likhoza kupezeka m’Baibulo.

“Ufumu Wanu Udze”​​​—Pemphero Limene Anthu Ambiri Amalikonda

Kodi ndi mafunso ati okhudza Ufumu wa Mulungu amene akuyenera kuyankhidwa kuti timvetse zimene pempheroli limatanthauza?

N’chifukwa Chiyani Tikufunikira Ufumu wa Mulungu?

Anthu opanda ungwiro akamalamulirana, zotsatira zake zimakhala mavuto okhaokha.

Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu Ndi Ndani?

Anthu ambiri amene analemba mabuku a m’Baibulo anafotokoza zinthu zokhudza munthu amene adzakhale Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Koma pali munthu mmodzi yekha yemwe anasonyeza kuti anthuwo ankanena za iyeyo.

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulira Dzikoli?

Otsatira ena a Yesu ankafunanso kudziwa kuti Ufumu udzabwera liti. Kodi Yesu anawayankha bwanji?

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?

Yesu ankadziwa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungathetse mavuto padzikoli. Kodi Ufumuwu wachita kale zinthu ziti zomwe zingatithandize kuukhulupirira?

Sankhani Kukhala Kumbali ya Ufumu wa Mulungu Panopa

Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti azifunafuna Ufumu choyamba. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Anthu ambiri amapemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere. Koma kodi munadzifunsapo kuti, Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani komanso udzachita zotani?