Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Lingakuthandizeni Kuti Mukhale ndi Tsogolo Labwino

Baibulo Lingakuthandizeni Kuti Mukhale ndi Tsogolo Labwino

TIYEREKEZE kuti mukuyenda mumsewu. Dzuwa lalowa kalekale ndipo kunja kuli mdima. Komabe simukuda nkhawa kuti musochera chifukwa muli ndi tochi. Mukailozetsa pansi mukutha kuona bwinobwino zinthu zimene zili pafupi ndi mapazi anu. Komanso mukailozetsa kutsogolo kwanu, mukuona bwinobwino njira yonse.

Baibulo tingaliyerekezere ndi tochi imeneyi. Monga taonera munkhani zapita zija, Baibulo lingatithandize kudziwa zoyenera kuchita pa mavuto amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku m’dziko loipali. Koma si zokhazi. Baibulo limafotokozanso zimene zidzachitike m’tsogolo ndipo zimenezi zingakuthandizeni kudziwa zimene muyenera kuchita kuti mukhale ndi tsogolo labwino. (Salimo 119:105) Koma kodi Baibulo lingatithandize bwanji kuti tikhale ndi tsogolo labwino?

Tiyeni tikambirane njira ziwiri. 1 Limatithandiza kudziwa cholinga cha moyo komanso 2 limatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Mlengi wathu.

1 CHOLINGA CHA MOYO

M’Baibulo muli malangizo abwino amene angatithandize tikakumana ndi mavuto, ngakhale kuti cholinga chake si kungotipatsa malangizo pa moyo wathu. M’malo motilimbikitsa kumangoganizira za mavuto athu okha, Baibulo limatiphunzitsa kuti tiziganiziranso za anthu ena. Kuchita zimenezi n’kumene kungatithandize kuti tizisangalala.

Mwachitsanzo, taganizirani mfundo iyi: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Kodi munamva bwanji mutathandiza munthu winawake wovutika pom’patsa ndalama kapena zinthu zina? Nanga munamva bwanji mutamvetsera pamene mnzanu ankakufotokozerani mavuto ake? N’kutheka kuti munasangalala kwambiri poona kuti mwamuthandiza kuti ayambirenso kusangalala.

Timasangalala kwambiri ngati tapereka zinthu kwa wina tilibe maganizo oti adzatibwezere kenakake. Wolemba mabuku wina anati: “N’zosatheka kupereka zinthu kwa wina popanda kubwezeredwa zinthu zambiri kuposa zimene unaperekazo. Koma izi zimatheka ngati poperekapo unalibe maganizo oti adzakubwezere.” Tikamathandiza anthu, makamaka amene sangathe kutibwezera chilichonse, timalandira madalitso. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timaganiziranso anthu ena komanso timakhala kuti tikugwira ntchito limodzi ndi Yehova. Ndipotu Yehova amaona kuti zimene timachita pothandiza anthu ovutika zili ngati kumukongoza iyeyo. (Miyambo 19:17) Iye amayamikira kwambiri zimenezi ndipo amalonjeza kuti adzatipatsa moyo wosatha m’Paradaiso.​—Salimo 37:29; Luka 14:12-14. *

Baibulo limatiphunzitsanso kuti tingakhale osangalala ngati timatumikira Mulungu woona, Yehova. Mawu ake amatiuza kuti tiyenera kumumvera, kumulemekeza ndiponso kumupatsa ulemerero. (Mlaliki 12:13; Chivumbulutso 4:11) Tikamachita zimenezi zotsatira zake zimakhala zovuta kumvetsa. Timasangalatsa Mlengi wathu. Paja iye amatiuza kuti: “Khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga.” (Miyambo 27:11) Taganizirani mfundo imeneyi. Tikamasankha zinthu mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo, timasangalatsa mtima wa Atate wathu wakumwamba. N’chifukwa chiyani zili choncho? Chifukwa choti amatikonda moti amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino ndipo zimatiyendera bwino tikamatsatira malangizo ake. (Yesaya 48:17, 18) Kodi pangakhale chinthu chosangalatsa kuposa kutumikira Mlengi wa chilengedwe chonse komanso kukhala ndi makhalidwe amene amasangalatsa mtima wake?

2 KUKHALA PA UBWENZI NDI MLENGI WATHU

Baibulo limatiuzanso kuti tiyenera kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu yemwe anatilenga. Limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yakobo 4:8) Nthawi zina tingamakayikire ngati zilidi zotheka kukhala pa ubwenzi ndi Mlengi wachilengedwe chonse. Koma Baibulo limatitsimikizira kuti ‘tikamafunafuna Mulungu, tidzamupezadi’ chifukwa “iye sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Malangizo a m’Baibulo akuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu ndi ofunika kwambiri kuti tikhale ndi tsogolo labwino. N’chifukwa chiyani tikutero?

Taganizirani mfundo iyi: Anthufe ngakhale titayesetsa bwanji, patokha sitingathe kuthetsa imfa yomwe ndi mdani wamkulu. (1 Akorinto 15:26) Koma Yehova adzakhalapo mpaka kalekale. Iye sadzafa ndipo amafunanso kuti mabwenzi ake adzakhale ndi moyo mpaka kalekale. Baibulo limasonyeza kuti Yehova amafuna kuti anthu amene amamutumikira adzakhale ndi moyo wosatha. Limati: “Mitima yanu ikhale ndi moyo kosatha.”​—Salimo 22:26.

Ndiye kodi mungatani kuti mukhale pa ubwenzi ndi Mulungu? Pitirizani kuphunzira Baibulo kuti mumudziwe bwino. (Yohane 17:3; 2 Timoteyo 3:16) Muzimupempha kuti azikuthandizani kumvetsa Malemba. Baibulo limatitsimikizira kuti ngati ‘titamapempha Mulungu’ kuti atipatse nzeru, adzatipatsa. * (Yakobo 1:5) Komanso muziyesetsa kutsatira zimene mukuphunzira m’Baibulo. Mukatero ndiye kuti mukulola kuti Mawu a Mulungu akhale ngati “nyale younikira kumapazi” anu ndiponso “kuwala kounikira njira” yanu, panopa komanso mpaka kalekale.​—Salimo 119:105.

^ ndime 8 Kuti mumve zambiri zokhudza zimene Mulungu analonjeza zotipatsa moyo wosatha padziko lapansi, onani mutu 3 m’buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 13 A Mboni za Yehova amaphunzira Baibulo ndi anthu pofuna kuwathandiza kuti ayambe kumvetsa bwino Malemba. Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene phunziro la Baibulo limachitikira, onerani vidiyo yakuti, Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? Kuti mupeze vidiyoyi, pitani pa webusaiti ya jw.org/ny (Pitani pamene alemba kuti MABUKU > MAVIDIYO).

Mulungu sadzafa ndipo amafunanso kuti mabwenzi ake adzakhale ndi moyo mpaka kalekale