Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI KUTI KUWERENGA BAIBULO KUZIKUSANGALATSANI

Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?

Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?

Baibulo ndi lapadera kwambiri chifukwa lili ndi malangizo ochokera kwa Mlengi wathu. (2 Timoteyo 3:16) Uthenga wake ukhoza kutithandiza kwambiri. Ndipotu limanena kuti: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.” (Aheberi 4:12) Baibulo likhoza kutithandiza m’njira ziwiri. Lili ndi mfundo zotithandiza pa moyo wathu watsiku ndi tsiku komanso limatithandiza kudziwa Mulungu ndiponso zimene analonjeza.—1 Timoteyo 4:8; Yakobo 4:8.

Lingakuthandizeni pa moyo wanu panopa. Baibulo lingakuthandizeni pa zinthu zambiri. Mwachitsanzo, lili ndi malangizo okhudza:

Banja lina lachinyamata ku Asia linathandizidwa kwambiri ndi malangizo a m’Baibulo. Mofanana ndi anthu ambiri amene angolowa kumene m’banja, iwo ankavutika kuzolowerana komanso kukambirana zinthu momasuka. Koma kenako anayamba kugwiritsa ntchito zimene ankawerenga m’Baibulo. Kodi zimenezi zinawathandiza bwanji? Mwamuna wa m’banjali, dzina lake Vicent, anati: “Zimene ndinkawerenga m’Baibulo zinandithandiza kuthetsa mavuto a m’banja lathu mwachikondi. Kutsatira mfundo za m’Baibulo kwatithandiza kukhala ndi banja losangalala.” Mkazi wake, dzina lake Annalou, ananenanso kuti: “Kuwerenga nkhani za anthu otchulidwa m’Baibulo kwatithandiza kwambiri. Panopa ndikuona kuti zinthu zikuyenda bwino m’banja lathu ndipo tonse tili ndi zolinga zabwino zimene tikufuna kukwaniritsa.”

Lingakuthandizeni kudziwa Mulungu. Kuwonjezera pa zimene ananena zokhudza banja lake, Vicent anati: “Ndimaona kuti kuwerenga Baibulo kwandithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova kuposa kale.” Izi zikusonyeza kuti Baibulo lingakuthandizeni kuti mudziwe bwino Mulungu. Mukamawerenga Baibulo, malangizo a Mulungu amakuthandizani kwambiri ndipo mumayamba kuona kuti iye ndi mnzanu weniweni. Mudzaonanso kuti Mulungu anafotokoza zinthu zosangalatsa zokhudza nthawi imene tidzakhale ndi ‘moyo weniweni,’ womwe sudzatha. (1 Timoteyo 6:19) Kunena zoona, palibe buku lina lililonse lomwe lingafotokoze zimenezi.

Mukayamba kuwerenga Baibulo komanso kupitiriza kuchita zimenezi, mukhoza kupindula kwambiri. Mukhoza kukhala ndi moyo wosangalala panopa komanso kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. Komabe mukamawerenga Baibulo mukhoza kukhala ndi mafunso ambiri. Zikatero, muzikumbukira chitsanzo chabwino cha nduna ya ku Itiyopiya imene inakhala ndi moyo zaka zoposa 2,000 zapitazo. Ndunayi inali ndi mafunso ambiri okhudza nkhani za m’Baibulo. Iye atafunsidwa ngati ankamvetsa zimene akuwerenga, anati: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulira?” * Kenako analola kuti athandizidwe ndi Filipo, yemwe anali wophunzira wa Yesu ndipo ankadziwa bwino Baibulo. (Machitidwe 8:30, 31, 34) Ngati nanunso mukufuna kudziwa zambiri zokhudza Baibulo, mukhoza kupita pawebusaiti ya www.isa4310.com/ny n’kulemba fomu yopempha munthu woti aziphunzira nanu Baibulo. Mukhozanso kulemba kalata pogwiritsa adiresi yoyenera yomwe ili m’magaziniyi. Apo ayi, mungapeze a Mboni za Yehova amene muli nawo pafupi kapena mungapite ku Nyumba ya Ufumu yam’dera lanu. Mungachite bwino kwambiri kuyamba lero kuwerenga Baibulo n’kulola kuti lizikuthandizani pa moyo wanu.

Ngati mumakayikira zimene Baibulo limanena, tikukulimbikitsani kuti muonere vidiyo yakuti Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona? Mungapeze vidiyoyi mukapita pa jw.org/ny pamene palembedwa kuti MABUKU > MAVIDIYO > BAIBULO

^ ndime 8 Kuti mudziwe malangizo ena amene ali m’Baibulo, pitani pawebusaiti yathu ya jw.org/ny pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO.