Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Tindevu ta Mphaka

Tindevu ta Mphaka

MPHAKA amakonda kuyenda komanso kufufuza chakudya usiku. Tindevu take timamuthandiza kudziwa ngati komwe akulowera kuli chinthu. Timamuthandizanso kudziwa malo omwe kuli tizinyama ngati makoswe, tomwe amakonda kudya.

Taganizirani izi: Tindevu ta mphaka timalumikizana ndi minyewa ndipo minyewayi imatha kuzindikira ngakhale kuwomba kwa mphepo. Zimenezi zimathandiza kuti mphaka azitha kuzindikira zinthu zomwe zili pafupi asanazione n’komwe. Amachita zimenezi ngakhale ali mumdima.

Popeza tindevuti timatha kuzindikira ngakhale kuwomba kwa mphepo, mphaka amatha kudziwa malo amene pali tinyama toti angathe kugwira komanso komwe tikulowera. Komanso mphaka akafuna kulowa pamalo enaake, amagwiritsa ntchito tindevuti kuti adziwe kukula kwa malowo kuti aone ngati angakwanepo. Buku lina linanena kuti, “anthu sadziwa zonse zokhudza mmene mphaka amagwiritsa ntchito tindevu take. Koma chomwe amadziwa n’choti atatidula, mphaka akhoza kumalephera kuchita zinthu zina bwinobwino.”—Encyclopædia Britannica.

Asayansi akupanga zimaloboti zokhala ndi tizinthu togwira ntchito ngati tindevu ta mphaka. Zimaloboti zoterezi zizitha kuzindikira kutsogolo kwake kukakhala chinthu. Izi zizithandiza kuti zisagundane ndi chinthucho. Wasayansi wina wa pa yunivesite ya California ku Berkeley, dzina lake Ali Javey, anati potengera mmene tindevu ta mphaka timagwirira ntchito, “asayansi akhoza kupanga maloboti apamwamba. Malobotiwa akhoza kumachita zinthu ngati anthu komanso nyama.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti tindevu ta mphakati tizitha kuchita zimenezi kapena pali winawake amene anatipanga?