Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Nyama

Nyama

Pafupifupi kulikonse kumene kuli anthu kumakhalanso nyama. Kodi Mulungu amafuna tiziziona bwanji nyama?

Kodi tiyenera kuziona bwanji nyama?

ZIMENE ANTHU AMANENA

Ena amaona kuti anthu ali ndi ufulu wochitira nyama chilichonse chimene angafune. Pomwe ena amaona kuti nyama ziyenera kumasamaliridwa mofanana ndi anthu.

  • Munthu wina yemwe amamenyera ufulu wa nyama ananena kuti: “Nyama nazonso zili ndi ufulu ndipo sitiyenera kungoziona ngati njira yobweretsera ndalama kapena yopezera zinthu.” Ananenanso kuti: “Tisiye kumangoona nyama ngati katundu wathu.”

  • Nkhani ina yomwe inadabwitsa anthu ambiri ndi ya mayi wina wolemera kwambiri, dzina lake Leona Helmsley. Mayiyu anasunga ndalama zokwana madola 12 miliyoni kuti zidzagwiritsidwe ntchito posamalira galu wake, iyeyo akadzamwalira. Analembanso mu wilo yake kuti galu wakeyo akadzafa, adzamuike pafupi ndi manda ake.

Nanga inuyo maganizo anu ndi otani? Kodi tiyenera kuziona bwanji nyama?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Yehova Mulungu, yemwe analenga zamoyo zonse, anauza anthu oyambirira kuti: ‘Muyang’anire nsomba zam’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso cholengedwa chilichonse chokwawa padziko lapansi.’ (Genesis 1:28) Izi zikusonyeza kuti Mulungu amaona kuti anthu ndi apamwamba kuposa nyama.

Umboni wa zimenezi ndi mawu omwe ali pa Genesis 1:27. Vesili limati: “Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake, m’chifaniziro cha Mulungu anam’lenga iye. Anawalenga mwamuna ndi mkazi.”

Popeza anthufe tinalengedwa ‘m’chifaniziro cha Mulungu,’ ndife apamwamba kuposa nyama chifukwa timasonyeza makhalidwe a Mulungu monga nzeru, chilungamo komanso chikondi. Tilinso ndi mtima wofuna kulambira Mulungu komanso kuchita zinthu zabwino. Nyama sizichita zimenezi chifukwa sizinalengedwe ‘m’chifaniziro cha Mulungu.’ N’zotsika ndipo siziyenera kuchitiridwa zinthu mofanana ndi anthu.

Kodi izi zikusonyeza kuti anthu ali ndi ufulu wochitira nkhanza nyama? Ayi.

  • Pa malamulo amene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli, panali lamulo lomwe linkanena kuti nyama zizipatsidwa mpata wopuma komanso chakudya. Lamuloli linkanenanso kuti nyama zizitetezedwa kuti zisavulale ndiponso kuthandizidwa zikamadwala kapena zikatopa.—Ekisodo 23:4, 5; Deuteronomo 22:10; 25:4.

“Uzigwira ntchito masiku 6. Koma tsiku la 7 usamagwire ntchito, kuti ng’ombe yako ndi bulu wako zizipuma.”Ekisodo 23:12.

Kodi kupha nyama n’kulakwa?

ZIMENE ANTHU AMANENA

Alenje ndi asodzi ena amachita masewera opha nyama, kuzithamangitsa kapena kumenyana nazo n’cholinga choti azigonjetse. Pomwe anthu ena amagwirizana ndi zomwe a Leo Tolstoy a ku Russia, ananena. A Leo ananena kuti kupha kapena kudya nyama “n’kupanda khalidwe.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mulungu amalola anthu kupha nyama ngati akufuna kupeza zovala kapena ngati nyamazo zikuika moyo wawo komanso wa ena pangozi. (Ekisodo 21:28; Maliko 1:6) Baibulo limanenanso kuti anthu akhoza kupha nyama kuti adye. Mwachitsanzo, lemba la Genesis 9:3 limanena kuti: “Nyama yamoyo iliyonse ikhale chakudya chanu.” Komanso, pa nthawi ina Yesu anathandiza ophunzira ake kugwira nsomba ndipo iye ndi ophunzira akewo anadya nsombazo.—Yohane 21:4-13.

Komabe, Baibulo limanenanso kuti “Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.” (Salimo 11:5) Choncho, Mulungu safuna kuti anthu azipha kapena kuzunza nyama n’cholinga chongofuna kusangalala.

Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amaona kuti moyo wa nyama ndi wamtengo wapatali.

  • Pamene Mulungu ankalenga zinthu, “anapanga nyama zakutchire monga mwa mitundu yake. Anapanganso nyama zoweta monga mwa mitundu yake, komanso nyama iliyonse yokwawa panthaka monga mwa mtundu wake. Ndipo Mulungu anaona kuti zili bwino.”Genesis 1:25.

  • Baibulo limanenanso kuti Yehova, “amapatsa zilombo chakudya chawo.” (Salimo 147:9) Kuti zimenezi zitheke, Mulungu analenga zinthu zomwe zimathandiza kuti nyama zikhale ndi chakudya chokwanira komanso malo okhala.

  • Mawu amene Mfumu Davide ya ku Isiraeli inanena amasonyezanso kuti Mulungu amaona kuti nyama ndi zofunika. Davide anapemphera kuti: “Inu Yehova, mumapulumutsa munthu ndiponso nyama.” (Salimo 36:6) Mwachitsanzo, pa nthawi ya chigumula chapadziko lonse, Mulungu anapulumutsa anthu 8 komanso nyama za mitundu yonse.—Genesis 6:19.

Apatu n’zoonekeratu kuti Yehova amaona kuti nyama n’zofunika kwambiri ndipo amafuna kuti zizisamalidwa bwino.

“Wolungama amasamalira moyo wa chiweto chake.”Miyambo 12:10.