Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Akadziwotche Omwe Amamva Kwambiri

Akadziwotche Omwe Amamva Kwambiri

PALI mtundu winawake wa akadziwotche omwe amamva kwambiri kuposa chilichonse. Ngakhale akadziwotchewa amamva kwambiri chonchi, ali ndi timakutu tating’ono kwambiri.

Taganizirani izi: Kwa zaka zambiri, akatswiri asayansi akhala akufufuza mmene akadziwotchewa amamvera. Posachedwapa, ochita kafukufuku pa yunivesite ya Strathclyde ku Scotland anafufuza zokhudza akadziwotchewa. Anagwiritsa ntchito phokoso losiyanasiyana kuti adziwe zambiri zokhudza mmene akadziwotchewa amamvera. Anayeza mmene mwinikhutu aliyense amanjenjemerera ndipo anajambula kuchuluka kwa phokoso lomwe mwinikhutu aliyense amamva. Anapezanso kuti mwinikhutu aliyense amanjenjemerabe ngakhale phokoso litakhala lotsika kwambiri poyerekeza ndi lomwe mileme, nsomba zazikulu zotchedwa anangumi komanso anthu, angamve. Mileme komanso anangumi zili m’gulu la zinthu zomwe zimamva kwambiri.

Asayansi akufuna apange zipangizo zamakono pogwiritsa ntchito zimene apeza zokhudza mmene akadziwotchewa amamvera. Malinga ndi zimene Dr. James Windmill wa pa yunivesite ya Strathclyde ananena, asayansiwa akuganiza kuti zimenezi zingawathandize kupanga maikolofoni aang’ono koma amphamvu kwambiri. Akuganiza kuti maikolofoniwa azidzawaika m’mafoni komanso m’zipangizo zothandiza anthu ovutika kumva.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti akadziwotche a mtundu umenewu azimva kwambiri kapena pali winawake amene anawapanga?