Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Njuchi Zimatera Mochititsa Chidwi

Njuchi Zimatera Mochititsa Chidwi

NJUCHI zikhoza kutera pamalo ena alionse mosavuta. Kodi zimakwanitsa bwanji kuchita zimenezi?

Taganizirani izi: Kuti njuchi itere bwino imafunika kuchepetsa liwiro, mwina mpaka kufika poima m’malere, isanatere pamalo amene ikufunapo. Pali zinthu ziwiri zimene zimathandiza njuchi kuti ichite zimenezi. Choyamba, imadziwa liwiro limene ikuulukira. Ndipo chachiwiri, imayeza mtunda wa pamene ili ndi pamene ikufuna kutera. Maso a njuchi amagwira ntchito mosiyana kwambiri ndi mmene maso a tizilombo tambiri amagwirira ntchito. Tizilombo tambiri sitingathe kuyeza mtunda wa pamene tili, ndi pamene tikufuna kutera.

Maso a njuchi amagwiranso ntchito mosiyana ndi mmene maso munthu amachitira. Maso a munthu amatha kudziwa kuti zinthu zomwe akuonazo zatalikirana bwanji. Njuchi zikamayandikira chinthu, maso ake amapangitsa kuti chinthucho chizioneka chachikulu. Chinthucho chimaoneka kuti chikukulirakulira njuchiyo ikamayandikiranso kwambiri. Kafukufuku wina amene anachitika payunivesite ina ku Australia, anasonyeza kuti njuchi zikamafuna kutera pa chinthu chinachake, zimachepetsa liwiro kuti kukula kwa chinthu chimene ikufuna iterepocho kusamasinthe kwambiri. Choncho njuchiyo ikamatera, imakhala itachepetseratu liwiro lake ndipo zimenezi zimathandiza kuti ithe kutera bwinobwino.

Magazini ina inanena kuti: “Zimene njuchi zimachita zikamatera, zingathandize akatswiri kupanga maloboti omwe atha kumawaulutsa ndi kumawawongoleranso bwinobwino.”Proceedings of the National Academy of Sciences.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti njuchi zizitha kutera choncho? Kapena pali winawake amene anazilenga kuti zizitha kuchita zimenezi?