Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Akazi ambiri a kumayiko osauka amamwalira pa nthawi yomwe ali ndi pakati kapena pamene akubereka poyerekezera ndi akazi a kumayiko olemera. Kumayiko olemera kukamwalira mkazi mmodzi, kumayiko osauka kumakhala kuti kwamwalira akazi pafupifupi 300.”—BUSINESSWORLD, PHILIPPINES.

Malinga ndi kafukufuku wina ku Germany, ana 40 pa 100 alionse a zaka zapakati pa 11 ndi 15 sadziwa kuti dzuwa limatulukira kum’mawa, ndipo ana 60 pa 100 alionse sadziwa kuti mwezi ukaonekera wathunthu umatenga milungu inayi kuti udzaonekenso wathunthu.—WELT ONLINE, GERMANY.

Akatswiri ofukula zinthu zakale apeza kachisi wa Afilisiti mumzinda wakale wa Gati. Kachisiyu ali ndi zipilala ziwiri, ndipo munthu kungoona kachisiyu angaganizire za nkhani ya m’Baibulo yonena za Samisoni, yemwe anagwira zipilala za kachisi n’kugwetsa kachisiyo.—THE JERUSALEM POST, ISRAEL.

Kuitanitsa Akazi Kuchokera Kunja

“Amuna a kumayiko olemera a ku Asia monga Japan ndi South Korea akumaitanitsa akazi kuchokera kumayiko osauka a ku Asia monga ku Vietnam ndi ku Philippines,” inatero nyuzipepala ya pa Intaneti ya ku Philippines yotchedwa BusinessWorld. Pakati pa chaka cha 1995 ndi 2006, amuna 73 pa 100 alionse a ku Japan anakwatira akazi akunja. N’chifukwa chiyani? Akuti “akazi a ku mayiko olemera amanyada chifukwa amaona kuti palibe chimene akusowa” ndipo safuna kukwatiwa. Pamene akazi a ku mayiko osauka amafuna kukwatiwa ndi amuna a ku mayiko olemera, ngakhale amunawo atakhala kuti ndi osauka, chifukwa amaonabe kuti “akakwatiwa nawo zinthu zidzayamba kuwayendera bwino.”

Kuthandiza Anthu Osakhulupirika Kuti Asagwidwe

Malo enaake a pa Intaneti omwe amapezeka m’mayiko asanu amalimbikitsa ntchito zake ndi mawu akuti: “Moyo ndi waufupi. Khalani ndi chibwenzi.” Malinga ndi zimene munthu amene anayambitsa malowa ananena, sikuti malowa ndi amene amachititsa anthu kuti akhale osakhulupirika kwa akazi kapena amuna awo, chifukwa anthu amene amabwera pamalowa amakhala kuti “ndi osakhulupirika kale.” Iye ananenanso kuti: “Mavuto ambiri amene anthu osakhulupirika amakumana nawo amayamba mkazi kapena mwamuna wawo akawagwira. Ifeyo timangothandiza anthu amene akufuna kukhala ndi zibwenzi kuti achite zimenezi mochenjera. Sindife amene tinayambitsa khalidwe losakhulupirika. Ntchito yathu ndi kungowathandiza kuti asagwidwe.” Pakali pano malowa ali ndi mamembala pafupifupi 6.4 miliyoni.

Kuvina N’kwachibadwa

“Anthu ali ndi luso lapadera kwambiri loti akangomva nyimbo amayamba kugwedeza thupi,” linatero lipoti lofalitsidwa ndi akatswiri ofufuza payunivesite ya York, ku England, ndi yunivesite ya Jyväskylä, ku Finland. Akatswiriwo apeza kuti ngakhale ana oti sanayambe kulankhula, amatha kuyamba kuvina akangomva kulira kwa nyimbo. Akamakwanitsa kuvinako m’pamene amasangalala kwambiri. Zimenezi zikusonyeza kuti kuvina n’kwachibadwa.