Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kamba Wam’madzi Amalondola Njira Mogometsa Kwambiri

Kamba Wam’madzi Amalondola Njira Mogometsa Kwambiri

Kodi Zinangochitika Zokha?

Kamba Wam’madzi Amalondola Njira Mogometsa Kwambiri

● Akatswiri asayansi amanena kuti mmene kamba wam’madzi amayendera kuchoka kunyanja kupita kumtunda kukaikira mazira, ndi “chimodzi mwa zinthu zogometsa kwambiri zimene nyama zimachita.” Akuti akatswiri asayansi akhala akuchita chidwi ndi kamba wam’madzi ameneyu kwa zaka zambiri.

Taganizirani izi: Pa zaka ziwiri kapena zinayi zilizonse, kamba wamkazi amapita kumtunda kuti akaikire mazira, omwe nthawi zambiri amafika 100. Akaikira mazirawa amawakwirira mumchenga. Mazirawo akaswa, tianato timayamba ulendo wa kunyanja. Tikafika kunyanjako, timayamba ulendo wina wautali kwambiri wam’madzi, mwina wa makilomita 12,900. Kenako pambuyo pazaka zingapo, akamba aakazi amabwereranso kumtunda komwe anabadwira kuja kuti akaikire mazira.

Kodi n’chiyani chimachititsa kuti akambawa azitha kuyenda ulendo wautali chonchi osasochera? Wasayansi wina wa payunivesite ya North Carolina, dzina lake Kenneth Lohmann, ananena kuti, “akamba amenewa amakhala ngati anabadwa ndi mapu m’mutu mwawo.” (National Geographic News) Anthu ochita kafukufuku apeza kuti akamba amenewa amatha kudziwa bwinobwino kuti kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi n’kuti. Nzeru zimenezi n’zimene zimathandiza kuti tiana ta akamba amenewa tizitha kuyenda ulendo wautali wa makilomita 12,900 m’nyanja ya Atlantic. Lohmann ananena kuti n’zochititsa chidwi kwambiri kuti akamba amenewa amatha kulondola bwinobwino njira “popanda kutsatira akamba ena.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti akambawa azitha kulondola njira mogometsa chonchi, kapena ndi umboni wakuti anachita kulengedwa?

[Bokosi patsamba 25]

DZIWANI IZI

● Kamba wamkazi akaikira mazira n’kuwakwirira mumchenga, amawasiya ndipo sabwereranso kuti adzawasamalire.

● Pobadwa, kamwana ka kamba wam’madzi kamagogomola dzira ndi dzino lapadera limene kenako limaguluka.

● Akamba am’madzi amathera pafupifupi moyo wawo wonse ali m’madzi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

© Masa Ushioda/​WaterF/​age fotostock