Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nthenga za Kadzidzi

Nthenga za Kadzidzi

Panagona Luso!

Nthenga za Kadzidzi

▪ Akatswiri opanga ndege amagoma ndi nthenga za kadzidzi. N’chiyani chimawachititsa chidwi? Kadzidzi amauluka mwakachetechete popanda kumveka phokoso lililonse. Nkhani ina ya pa Intaneti yolembedwa ndi bungwe la National Geographic inati: “Palibe mbalame inanso imene imauluka mwakachetechete ngati kadzidzi.” Kodi zimenezi zimatheka bwanji?

Taganizirani izi: Mbalame zambiri zikamauluka, mpweya umawombana ndi nthenga zake n’kumayenda mozungulira ndipo zimenezi zimachititsa kuti pazimveka phokoso. Koma zimenezi n’zosiyana ndi zimene zimachitika kadzidzi akamauluka. Nthenga za kadzidzi zili ndi ubweya winawake m’mphepete mwake womwe umachititsa kuti mpweya umene umayenda mozungulira pamwamba pa kadzidziyo usachite phokoso. Ndipo ubweya wina womwe umapezeka m’thupi lonse la kadzidziyo umachititsa kuti phokoso lililonse lotsalira lisamvekenso.

Akatswiri opanga ndege akufunitsitsa ataphunzira zambiri zokhudza chinsinsi cha kadzidzichi n’cholinga choti azipanga ndege zopanda phokoso. Ndege zotere zingamaloledwe kutera kapena kunyamuka pa mabwalo a ndege amene amaletsa ndege kunyamuka kapena kutera usiku kapena m’mamawa kwambiri chifukwa cha phokoso. Akatswiriwa ayamba kale kukonzekera zopanga ndege zoterezi. Pulofesa wina, dzina lake Geoffrey Lilley, yemwe poyamba ankagwira ntchito pa yunivesite ya maphunziro a za ndege ya Southampton ku England, anati: “Panopa tangoyamba kumene kuphunzira za mmene tingapangire ndege zotere.” Iye ananenanso kuti pangapite zaka zambiri kuti ndege zopanda phokosozi ziyambe kupangidwa.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika kuti kadzidzi akhale ndi nthenga zoterezi, kapena pali amene anazilenga?

[Chithunzi patsamba 23]

Yerekezerani nthenga ya kadzidzi (kumanzereku) ndi nthenga ya kabawi (kumanjaku)

[Mawu a Chithunzi patsamba 23]

Long-eared owl: © Joe McDonald/Visuals Unlimited; barn owl sequence: © Andy Harmer/Photo Researchers, Inc.; feather comparison: Courtesy of Eike Wulfmeyer/Wikimedia/GFDL