Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Njira Yabwino Yothetsera Vuto Logwiritsa Ntchito Mankhwala Mwachisawawa

Njira Yabwino Yothetsera Vuto Logwiritsa Ntchito Mankhwala Mwachisawawa

Njira Yabwino Yothetsera Vuto Logwiritsa Ntchito Mankhwala Mwachisawawa

LENA amene tamutchula m’nkhani yoyambirira ija, ali ndi zaka 32, anayamba kudziona kuti ndi “munthu wochimwa kwambiri, wolephera ndiponso ankangolakalaka kufa.” Ankaona choncho chifukwa anali ndi vuto logwiritsa ntchito mankhwala mwachisawawa. Iye analemba kuti: “Ndinali ndi mwamuna komanso ana ndipo ndinkayesetsa kukhala munthu wabwino. Koma ndinkamva chisoni ndi zinthu zambiri zimene zinkachitika pamoyo wanga ndiponso m’dzikoli moti sindinkaonanso chifukwa chokhalira wabwino. Ndipo ndinayesapo kangapo kusintha koma ndinalephera.”

Kenako Lena anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Pasanapite nthawi, choonadi cha m’Baibulo chinamuthandiza kukhala ndi mtendere wa mumtima. Iye anati: “Ndinayamba kumva bwino kwambiri kuposa nthawi ina iliyonse m’mbuyomu.” Chifukwa chodziwa mfundo za m’Baibulo ndiponso zinthu zabwino zimene Mulungu walonjeza, anasintha khalidwe lake ndipo anasiya chizolowezi chake chogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.

Mfundo Zothandiza Kwambiri

Malamulo ndiponso mfundo za m’Baibulo zimene Mlengi wathu, Yehova Mulungu, anapereka, n’zothandiza pamoyo wathu. N’chifukwa chake, lemba la Salmo 19:7, 8 limati: “Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo . . . Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima: Malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.”

Mwachitsanzo, pa 2 Akorinto 7:1, Baibulo limatilimbikitsa “kuchotsa chilichonse choipitsa cha thupi ndi cha mzimu.” Lena anamvera malangizo a palembali ndipo anasintha khalidwe lake. Nayenso Myra, yemwe tinamutchulanso m’nkhani yoyambirira ija, anachita chimodzimodzi. Mankhwala amene iye ankamwa chifukwa chodwala mutu anamulowerera kwambiri. Kodi iye anathetsa bwanji vuto lake? Anafotokozera dokotala vuto lake, ndipo dokotalayo anamuthandiza kuti ayambe kumwa mankhwala amtundu wina. * Ndiponso ankatsatira malangizo amene mpingo unkamupatsa.

Lena ndi Myra anapemphanso Mulungu kuti awathandize. Lemba la Afilipi 4:6, 7 limati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, limodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.” Kale, mtumiki wina wa Mulungu amene anapeza mtendere wa mumtima wotere analemba kuti ‘zolingalira zitamuchulukira m’kati mwake,’ mawu olimbikitsa a Mulungu anamukhazika mtima pansi, kumutonthoza ndi kum’pangitsa kukhalabe wosangalala. (Salmo 94:19) Mawu otonthoza amenewa tingawapeze m’Baibulo ndiponso kwa Akhristu anzathu, kuphatikizapo akulu.

Koma nthawi zina munthu amene ali ndi vuto logwiritsa ntchito mankhwala mwachisawawa, angamadzione kuti ndi wosafunika. Mkhristu wina, dzina lake Janice, yemwe anali ndi vuto lomwa mankhwala akuchipatala kwa zaka zambiri, analemba kuti: “Anthu amene mankhwala anawalowerera amaonanso kuti ubwenzi wawo ndi Mulungu wasokonekera ndipo amadziona kuti ndi olakwa, moti paokha amalephera kupempha Yehova kuti awathandize.” Zikatere, ndi bwino kupempha Akhristu odalirika kuti awathandize. Iwo angawalimbikitse mwachikondi ndipo mapemphero awo achikhulupiriro ‘angachiritse wodwalayo.’ (Yakobe 5:15) Komabe, ngati mwana ndi amene ali ndi vuto, makolo ayenera kuyesetsa kwambiri kumuthandiza mwauzimu komanso ayenera kuonana ndi dokotola kuti vutolo lisayambirenso.

Janice anapita kuchipatala ndipo anamuthandiza kuthetsa vuto lake. Kuyambira nthawi imeneyo, sagwiritsanso ntchito mankhwala mwachisawawa. Iye analemba kuti: “Ndimadalira Yehova kuti andithandize kuthetseratu vuto langa. Panopa ndili ndi mtendere wa mumtima ndipo panopa ndayamba kusangalalanso ngati kale.”

Mavuto Athu Adzatha

Posachedwapa, vuto logwiritsa ntchito mankhwala mwachisawawa lidzatheratu. Kodi zidzatheka bwanji? Lemba la Chivumbulutso 21:3, 4 limati: “Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu . . . Iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo [kuphatikizapo mavuto amene anthu akukumana nawo masiku ano] zapita.”

Baibulo limayerekezera chiyembekezo chimene Akhristu ali nacho ndi “nangula wa miyoyo yathu. N’chotsimikizika, n’chokhazikika.” (Aheberi 6:18, 19) Kale, anthu oyendetsa chombo akakumana ndi chimphepo, ankaponyera nangula m’madzi. Nangulayo akafika pansi pa nyanja, ankathandiza chombocho kuti chisatengeke ndi mafunde. Mofanana ndi nangula, chiyembekezo ‘chotsimikizika’ ndiponso ‘chokhazikika’ cha m’Baibulo, chingatithandize kuti tikhale okhazikika maganizo ndiponso olimba mwauzimu tikakumana ndi ziyeso zokhala ngati chimphepo.

Yesetsani kuwerenga Baibulo ndipo mudzaona kuti mfundo zake n’zothandiza komanso zolimbikitsa. Mboni za Yehova zingakuthandizeni kwambiri pankhani imeneyi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Sikuti anthu onse angawasinthire mankhwala ngati mmene zinakhalira ndi Myra. Mwachitsanzo, anthu ena akadwala matenda opweteka kwambiri, amatha kupatsidwa mankhwala amphamvu omwe angathe kuwalowerera. Mankhwalawa amawamwa dokotala akuwayang’anira. Apa sitinganene kuti anthu oterewa akugwiritsa ntchito mankhwala molakwika.—Onani Miyambo 31:6.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

“Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero . . . zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu . . . udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”—Afilipi 4:6, 7

[Bokosi/Chithunzi patsamba 10]

NJIRA ZOTHANDIZA KUTI ZINTHU ZIZIKUYENDERANI BWINO

Buku lina linanena kuti kuchita masewera olimbitsa thupi “kungakuthandizeni kuti muzikhala osangalala komanso kuti musamavutike maganizo.” (Managing Your Mind—The Mental Fitness Guide) Komanso kusintha chakudya ndi zochita zanu kungakuthandizeni. Mwachitsanzo, mtsikana wina, dzina lake Valerie, anachitiridwa nkhanza ali wamng’ono. Kenako anayamba kugwiritsa ntchito mitundu ya mankhwala yoposa 12. Komabe patapita nthawi, iye anasintha chizolowezi chake ndipo anayamba kuchita zinthu bwinobwino. Kodi zinatheka bwanji?

M’malo moonera TV ndiponso kuwerenga mabuku oipa ngati kale, iye anayamba kuwerenga mokhazikika Baibulo ndi zinthu zina zofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, kuphatikizapo magazini ino. Iye ankapempheranso kwa Mulungu nthawi zonse kuti amuthandize, kupezeka pamisonkhano ya mpingo ndiponso kuthera nthawi yake yambiri akuuza ena zinthu zolimbikitsa zimene Baibulo limanena. Kuwonjezera pamenepo, iye anayamba kusankha bwino zakudya. Atachita zonsezi, vuto lake linatheratu ndipo madokotala anadabwa kwambiri. Panopa papita zaka zambiri chisiyireni kumwa mankhwala mwachisawawa. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 21 Ngati mumamwa mankhwala akuchipatala chifukwa cha vuto la kuvutika maganizo, matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochita, kapena matenda ena okhudza ubongo, ndiye kuti vuto lanu ndi losiyana ndi la Valerie. Choncho, musasinthe mankhwala popanda kukambirana ndi dokotala.