Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chigoba cha Chikumbu

Chigoba cha Chikumbu

Panagona Luso!

Chigoba cha Chikumbu

▪ Pali mtundu wina wa chikumbu chimene chimakhala ndi chigoba choyera kwambiri chopangidwa ndi timaulusi topyapyala kuposa tsitsi la munthu. Pulofesa wina wa pa yunivesite ya Exeter ku Britain, dzina lake Pete Vukusic, ananena kuti: “Nditaunika zikumbu zimenezi pa maikulosikopu ndinagoma ndi mmene zinkaonekera.”

Taganizirani izi: Zimene Vukusic anapeza zimatithandiza kumvetsa chimene chimachititsa kuti zikumbuzi zizioneka zoyera kwambiri. Kupyapyala komanso kutalikirana kwa timaulusi ta chigoba cha chikumbuchi n’zimene zimachititsa kuti chizioneka choyera ndiponso chonyezimira kwambiri. Magazini ina inati: “Mafakitale opanga zinthu zoyera kwambiri monga mapepala olembera, mapepala apulasitiki komanso penti, amathira mankhwala kuti zinthuzo zikhale zoyera. Koma kuti kuyera kwa zinthuzi kufanane ndi chigoba cha chikumbu, amafunika kuthira mankhwala ambiri kuwirikiza kawiri.”—Science Daily.

Asayansi amanena kuti kuyera kwa chigobachi kumathandiza kuti chikumbuchi chisamaoneke chikakhala pa bowa woyera. Koma asayansi akufufuzabe kuti adziwe chimene chimachititsa chikumbuchi kuoneka choyera kwambiri ndipo akukhulupirira kuti zimene angapezezo zingathandize kwambiri. Mwachitsanzo, zingathandize popanga ulusi woyera kwambiri. Vukusic ananena kuti zinthu monga mapepala omwe timagwiritsa ntchito polemba, mtundu wa mano, ndiponso kuwala kwa magetsi “zingasinthe kwambiri ngati makampani atatengera zimene zimachititsa chikumbuchi kuoneka choyera kwambiri.”

Kodi mukuganiza bwanji? Kodi chigoba cha chikumbu choyera chinakhalapo chokha kapena chinachita kulengedwa?

[Chithunzi patsamba 24]

Chikumbu choyera n’chaching’ono kwambiri kuposa nsonga ya chala chanu (chithunzichi tachikulitsa)

[Mawu a Chithunzi]

Department of Entomology, Kasertsart University, Bangkok